Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 1/1 tsamba 5-7
  • Alengezi Atuta Zotuta za Dziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Alengezi Atuta Zotuta za Dziko Lonse
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mexico
  • India
  • Belgium
  • Portugal
  • Thailand
  • Kenya
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kuvomereza Mbiri Yabwino m’Belgium
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhosa za Yesu Zimva Mawu Ake
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Mbiri Yabwino Kuchokera ku Norway
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 1/1 tsamba 5-7

Alengezi Atuta Zotuta za Dziko Lonse

“Pamene nthaŵi iyenda kupita ku Armagedo, Mboni za Yehova zikupititsa patsogolo ntchito zawo kupangitsa ambiri a ife monga mmene angathere kupulumuka kuchoka ku chiwonongeko chowopsyacho.”​—Mkonzi Ian Boyne mu “The Sunday Gleaner,” March 15, 1987, Kingston, Jamaica.

MKONZI wolemba wogwidwa mawu pamwambapo ali wolondola. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Armagedo, pamene Mulungu adzawononga oipa, iri pafupi ndipo kuti mtundu wa anthu ukukhala m’nthaŵi ya chiweruzo chaumulungu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Chotero, pali chifuno kaamba ka anthu kulabadira uthenga wa mbiri yabwino. Yesu Kristu, mlengezi wamkulu woposa wa anthu, anayambitsa gulu lomwe linalengeza “ku malekezero a dziko lapansi” m’zana loyamba. (Machitidwe 1:8, New English Bible; Akolose 1:23) Iye analosera ntchito yolengeza yofananayo kaamba ka tsiku lathu. (Mateyu 24:14) Gulu limene tsopano likuchita chimenecho liri lopangidwa ndi Mboni za Yehova, zomwe zimalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi changu m’maiko 210 ndi magawo.

Mboni za Yehova, ngakhale kuli tero, ziri koposa gulu lolalikira chabe. Izo zirinso gulu lophunzitsa. Yesu anauza atsatiri ake “kupanga ophunzira a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa iwo kusunga zinthu zonse ndakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20) Tingakonde kukudziŵitsani inu kwa anthu ena omwe apindula kuchokera ku ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa.

Mexico

Kumanani ndi Virginia. Iye ali ndi zaka za kubadwa 110 ndipo akufuna kukuuzani kuti “sikukhala nkomwe kuchedwa kufika ku kudziŵa ndi kutumikira Yehova.” Monga mkazi wachichepere, iye anali wodzipereka kotero kuti kwa zaka zinayi anavala zovala zapadera za chipembedzo. “Koma chinachake chinali kusoweka,” iye akutero. Kulibe kwina kulikonse kumene anapeza mayankho okhutiritsa ku mafunso ake a Baibulo. Mwachitsanzo, pamene anafunsa aphunzitsi mu tchalitchi chake, “Kodi dzina la Mulungu ndani?,” iwo anayankha, “Dzina la Mulungu ndi Mulungu.”

Koma zinthu zinasintha mu 1983 pamene mdzukulu wake wamkazi anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mdzukulu wa Virginia anayankha funso la Virginia mwakunena kuti Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Masalmo 83:18) Ichi chinamusonkhezera Virginia kukhala ndi phunziro lakelake la Baibulo ndi Mboni. Zaka ziŵiri pambuyo pake, pa June 2, 1985, iye anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 108.

“Ndimakumbukira tsiku limenelo ndi chiyamikiro,” iye akutero, “chifukwa pa tsiku limenelo ndinayamba kukhala ndi moyo. Pa msinkhu wanga, ndimalalikira maora asanu kapena asanu ndi limodzi pa mwezi ndipo ndimagwiritsira ntchito ndodo kaamba ka chichirikizo poyenda. Ndimakonda kuyenda ndi miyendo kuposa kuyenda pa galimoto. Mwanjirayi ndimakhala m’mkhalidwe wa kuthupi wabwino.”

India

“Ndinali munthu wovutitsa wa kumaloko ndi munthu wopanda pake,” akutero munthu yemwe anali mkaidi pa milandu yosiyanasiyana. “Ndinali kuba anamgoneka, kuseŵera mutka (njuga), ndi kusuta ndudu zaulere zoperekedwa ndi makasitomala anga a chinsinsi. Panalinso chizoloŵezi cha zoledzeretsa​—zonsezi mosasamala kanthu za chenicheni chakuti ndinali chiwalo chokangalika cha tchalitchi.” Koma pamene mmodzi wa Mboni za Yehova anafika panyumba pake ndi kuyamba kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsira ntchito uphungu wake, moyo wake unasintha. (Miyambo 2:1-22; 2 Timoteo 3:16) Tsopano iye, mkazi wake, ndi ana ake aŵiri a akazi akuthandiza ena kuchoka ku maupandu oterowo.

Belgium

Okwatirana aŵiri achichepere anakwiya kwambiri ndi Mulungu. Nchifukwa ninji? Mwana wawo woyamba, wamkazi, anafa masiku khumi pambuyo pa kubadwa. Mwana wawo wachiŵiri anabadwa wopunduka. Ndipo mwana wawo wachitatu, yemwe anawoneka kukhala wamphamvu ndi waumoyo wabwino, anafa mosayembekezereka pambuyo pa miyezi isanu. Mayiyo sanakhulupirire kuti Mulungu wachikondi akanavomereza matsoka oterowo kuchitika kwa iwo pamene anthu ambiri amene anali kukhala ndi mkhalidwe wa moyo woipa, anali ndi ana a umoyo wabwino.

Mwamsanga pambuyo pake, mmodzi wa Mboni za Yehova anali kulalikira kuchokera kunyumba ndi nyumba m’malowo ndipo anaitanira pa nyumba yake. Pamene Mboniyo inalankhula ponena za malonjezo a Mulungu kaamba ka mtsogolo mwachimwemwe kaamba ka mtundu wa anthu, mkaziyo anayankha motsutsana ndi lingaliro la Mulungu yemwe anali Tate wachikondi wa kumwamba. (Masalmo 37:10, 11) Koma iye anavomereza kulandira mabukhu ena a Baibulo. Mwapang’onopang’ono, pambuyo pa maulendo obwerezabwereza ochitidwa ndi Mboniyo, uthenga wa Baibulo wa mbiri yabwino unafewetsa mtima wake ndi kumangilira chidaliro chake mwa Mulungu. Tsopano onse aŵiri iye ndi mwamuna wake ali ndi chiyembekezo champhamvu osati kokha kuti Yehova adzachiritsa mnyamata wawo wopunduka mtsogolo m’Paradaiso pa dziko lapansi komanso kuti Iye adzaukitsa ana awo ena aŵiri.​—Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:1-4.

Portugal

M’mawa wina pa Sande, mkazi wonyamula chola chodzaza ndi zinthu za ku golosale anaima kuti alankhule ndi okwatirana aŵiri. Iyi inali nthaŵi yoyamba koma osati yomaliza imene iwo akanakumana. Okwatiranawo, Mboni za Yehova, anali m’ntchito yolengeza. Iwo anayamikira wogulayo kaamba ka kuyang’ana kaamba ka zosowa zakuthupi za banja lake. Koma ndani, iwo anafunsa, amene angapereke zosowa za mtundu wa anthu? Iwo anayankha funsolo iwo eni mwakunena kuti Mulungu angatero. (Masalmo 107:8, 9; Yesaya 33:24) “Kodi iye ali ndi yankho ku vuto langa?” mkaziyo anadabwa mofuula. Mbonizo zinayankha movomereza ndipo zinaitanidwa kunyumba yake, kumene phunziro la Baibulo linayambika. Mwamuna wake, akumawona masinthidwe ku ubwino wa mkhalidwe wa mkazi wake, analowamo m’phunziro la Baibulo ndipo m’kupita kwa nthaŵi iyenso anapanga masinthidwe m’njira yake ya moyo.

Pambuyo pake, mkaziyo anauza Mbonizo kuti asanalankhule ndi iwo m’mawa wa Sande limene lija, iye anali atayesera kudzipha kaŵiri. Iye anakhumudwitsidwa kwambiri chifukwa chakuti iye ndi mwamuna wake anagamulapo kulekana. Tsopano, ngakhale kuli tero, iye, mwamuna wake, ndi ana awo agwirizana m’kupanga kupita patsogolo m’kuphunzira ponena za mbiri yabwino.

Thailand

Kwa mbali yaikulu ya moyo wake, mkazi wokhala m’mbali ya kumpoto kwa dzikoli anali kuvutitsidwa ndi ziwanda. Pamene iye anakumana ndi mmodzi wa Mboni za Yehova m’ntchito yawo yolengeza, anapeza mabukhu ena a Baibulo ndi kuvomereza ku phunziro la Baibulo la panyumba. Pambuyo pa miyezi iŵiri ya kuphunzira, iye anafika kukuyamikira zifukwa za Malemba kaamba ka kuchotsa m’nyumba mwake zinthu zonse zogwirizana ndi kulambira konama, monga ngati mafano, ndi kugwetsa nyumba yake yokondedwa ya mizimu yomangidwa kuchinjiriza banja lake ku mizimu yoipa. (Machitidwe 19:19; 1 Akorinto 10:21; 1 Yohane 5:21) Tsopano iye savutitsidwanso ndi ziwanda ndipo ali wokhoza kusumika pa kuthandiza ena kuphunzira ponena za Mulungu wowona, Yehova.

Kenya

Pamene mtsogoleri wa gulu la aupandu anauzidwa kuti analingaliridwa kukhala wowopsya kotero kuti apolisi analamulidwa kumuwombera ndi mfuti pamene amuwona, ananyalanyaza icho mwa kungoseka. Komabe, mwamsanga pambuyo pake umodzi wa ulendo wa gulu lake sunachite mogwirizana ndi makonzedwe. Iye anadzipeza ali yekha, atazingidwa ndi khamu lokwiitsidwa lomwe linali lokonzekera kumukantha monga gulu. Panthaŵi imeneyo, apolisi anabwera kumupulumutsa, kumchotsa ndi kum’tsekera m’ndende kuti adikire kaamba ka mlandu m’bwalo la milandu.

Loya wake anamlangiza iye pa njira zosiyanasiyana za kukanira thayolo. Koma pamene iye anali m’ndende, anakumbukira maulendo opangidwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova zaka zingapo zapita. Iye anayamba kumvera chisoni njira zake zosaweruzika ndi kupemphera kwa Mulungu kaamba ka thandizo. M’chenicheni, iye anapemphera kwa Yehova ndi dzina. (Yerekezani ndi Machitidwe 10:1, 2.) Ku kudabwitsidwa kwa woweruza, mpandu ameneyu anavomereza kulakwa kwake pamaso pa bwalo la milandu. Chotero woweruzayo anapereka chiweruzo chabwinoko; m’malo mwa imfa, chiweruzo chake chinali zaka khumi m’ndende yaikulu ya chisungiko chotheratu.

Pamene anali m’ndende, iye mofunitsitsa anaŵerenga mabukhu a Baibulo ndipo mobwerezabwereza anapemphera kwa Mulungu, akumafunsa kuti, ngati nkotheka, nthaŵi yake m’ndende ichepetsedwe kotero kuti iye akamtumikire Iye. Mosayembekezera, iye anauzidwa kuti chilango chake chachepetsedwa ndi theka. Chotero, pambuyo pa kuikidwa m’ndende kwa zaka zisanu, iye anamasulidwa ndipo mwamsanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mwamsanga pambuyo pake iye anabatizidwa, ndipo tsopano ali ndi kulengeza kwa nthaŵi zonse monga chonulirapo chake.

Zapamwambazi ziri kokha zitsanzo zochepa za mmene Mboni za Yehova zikukwaniritsira ntchito yawo ndi thayo lawo la kulengeza “ku malekezero a dziko lapansi.” Zokumana nazo zimenezi zingachulukitsidwe kuwirikiza nthaŵi chikwi. Kodi mumakaikira, chotero, kuti Mboni za Yehova ziri alengezi owona lerolino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena