Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/1 tsamba 3-4
  • Kodi Zinthu Ziridi Bwino?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zinthu Ziridi Bwino?
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezerako Njira Yatsopano
  • Kodi Pali Chichirikizo Chaumulungu?
  • ‘Ndipo Khoma Linagwa Pansi’
    Galamukani!—1991
  • Mgwirizano wa Ulaya—N’chifukwa Chiyani Ungakhale Wofunika?
    Galamukani!—2000
  • Mboni za Yehova Kum’mawa kwa Yuropu
    Galamukani!—1991
  • Kum’mawa kwa Yuropu—Kodi Kukuvomerezanso Chipembedzo?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/1 tsamba 3-4

Kodi Zinthu Ziridi Bwino?

“Khoma [la Berlin] lingakhale lofeŵerapo pamene zigwirizano za Kum’maŵa ndi Kumadzulo zikuwonjezereka. Koma padzapita zaka zambiri, ngakhale mibadwo, ilo lisanagweretu. Majeremani aŵiriwo sadzakhalanso imodzi.” Anatero magazini anyuzi otchuka a ku Amereka m’March 1989.

Masiku 250 asanathe​—sizaka ayi, osatinso mibadwo​—khomalo linayamba kugumuka. M’milungu yokha, zikwi za zidutswa zake, tsopano zokhala m’mkhalidwe wa zikumbukiro, zinangokhala zokometsera padziko lonse.

KHOMA lotchedwa Iron Curtain lonyonyotsoka kotheratu limenelo linagaŵikana potsirizira pake, zikukulitsa ziyembekezo zakuti pambuyo panthaŵi yaitali mtendere wadziko lonse ndi chisungiko zinayandikira. Ngakhale Nkhondo ya ku Gulf m’Middle East siinazime chiyembekezo chakuti udani wakalekale pakati pa Kum’maŵa ndi Kumadzulo unatha, ndipo dongosolo ladziko latsopano linali pafupi.

Kuwonjezerako Njira Yatsopano

Chiyambire nkhondo yadziko yachiŵiri, ulendo wofikira Yuropu wogwirizana wakhala wowonekera. Mu 1951, maiko a Kumadzulo kwa Yuropu anakhazikitsa bungwe lotchedwa European Coal and Steel Community. Linatsatiridwa ndi bungwe lotchedwa European Common Market mu 1957. Mu 1987 maiko 12 omwe ndimamembala achitaganya chamitundu yonse chimenechi (gulu la anthu 342 miliyoni tsopano) anaika chonulirapo cha umodzi m’zachuma podzafika mu 1992. Ngakhale umodzi weniweni wa ndale zadziko tsopano ukuwonekera kukhala wothekera kwambiri. Kumeneku kuli kusintha kotsitsimula maganizo chotani nanga ku mbiri yokhathamira ndi mwazi ya Yuropu wadzulo!

Komabe, polingalira zochitika zandale zadziko zaposachedwapa, 1992 ikukhala yofunika koposapo. Pakhala zonenanena zowonjezereka zakuti maiko omwe anali a Chikomyunizimu a Kum’maŵa kwa Yuropu nawonso angaphatikizidwe mu Yuropu wogwirizana.

Kodi Pali Chichirikizo Chaumulungu?

Magulu achipembedzo ena, ponyalanyaza lamulo lamakhalidwe abwino Lachikristu lauchete, analola chididikizo pa chipembedzo chotha zaka makumi ambiri cha Kum’maŵa kwa Yuropu kuwakakamiza kudziloŵetsa m’ndale zadziko mokangalika. Pothirira ndemanga pa zimenezi, nyuzipepala ya Chijeremani ya tsiku ndi tsiku yotchedwa Frankfurter Allgemeine Zeitung inanena kuti “chithandizo cha Akristu chakudzetsa masinthidwe Kum’maŵa nchosatsutsika,” ikuwonjezera kuti “ndithudi kukhalamo kwawo ndi phande sikuyenera kunyalanyazidwa.” Iyo ikulongosola kuti: “Mwachitsanzo, m’Poland, chipembedzo chinagwirizana ndi dzikolo, ndipo tchalitchi chinakhala mdani wouma khosi wa chipani cholamulira; mu GDR [Jeremani Wakum’maŵa wakale] tchalitchi chinapatsa otsutsawo malo a zochita zawo ndi kuwalola kugwiritsira ntchito nyumba za tchalitchi kaamba ka kulinganiza zifuno zawo; m’Chekosolovakiya, Akristu ndi ochirikiza demokrase anakumana m’ndende, anayamikirana, ndipo pomalizira pake anagwirizana.” Ngakhale m’Romania, kumene “matchalitchi anatsimikizira kukhala atumiki okhulupirika a boma la Ceauşescu,” chiopsezo chakuponya m’ndende Laszlo Tökes, mtsogoleri wachipembedzo, ndicho chimene chinabutsa mkupiti woukira boma.

Vatikani nayonso inaloŵetsedwamo. Magazini a Time anathirira ndemanga m’December 1989 kuti: “Pamene kuli kwakuti kupereka malamulo kwachindunji kwa Gorbachev ndiko kunali chochititsa chachikulu cha chimasuko chotsatanatsatana chamwadzidzidzi ku Yuropu Wakum’maŵa m’miyezi yapita yoŵerengeka, John Paul ndiye woyenerera chitamando cha nthaŵi yaitali. . . . Mkati mwa ma 1980 nkhani zake zinagogomezera pa lingaliro la Yuropu wogwirizana kuyambira ku Atlantic mpaka ku mapiri a Ural ndipo zinasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro Chachikristu.” Monga chitsanzo, pamene ankachezera Chekosolovakiya m’April 1990, papa anasonyeza chiyembekezo chakuti kuchezetsa kwake kukatsegula njira zatsopano pakati pa Kum’maŵa ndi Kumadzulo. Iye analengeza kuti bungwe la abishopu a ku Yuropu linasankhidwa kuti lilinganize njira yokwaniritsira chiyembekezo chake cha “Yuropu wogwirizana pamaziko ake Achikristu.”

Kodi Jeremani wogwirizana mkati mwa makonzedwe a Yuropu wogwirizana sadzatsimikizira kukhala kalambula bwalo wa Yuropu wogwirizana kotheratu, ndiyeno ngakhale wa dziko logwirizana? Kodi kudziloŵetsamo kwachipembedzo sikumasonyeza kuti izi nzimene Baibulo likulonjeza? Ndithudi, pokhala ndi atsogoleri achipembedzo ponse paŵiri Kum’maŵa ndi Kumadzulo tsopano akugwirira ntchito m’makonzedwe a ndale zadziko kaamba ka mtendere ndi chisungiko, kodi sitingayembekezere zimenezi kukwaniritsidwa posachedwapa? Tiyeni tiwone.

[Mapu/Chithunzi patsamba 4]

Tchalitchi Chachiprotestanti cha Nikolai mu Leipzig​—chizindikiro cha kusintha kwa ndale zadziko m’Jeremani

Maiko omwe ndimamembala a European Common Market

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena