Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 10/15 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kuona Miyambo Yotchuka M’njira Yoyenera
    Galamukani!—2000
  • Kodi Akufa Ayenera Kulemekezedwa?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Mumakumbukira?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 10/15 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Pamene munthu wina amwalira, kodi kuli koyenera kwa Akristu kupatsa banja lake maluŵa kapena kutumiza maluŵa kunyumba ya maliro?

M’maiko ena kuteroko kuli mwambo. Koma kugwiritsira ntchito maluŵa pa maliro panthaŵi zina kwakhala ndi lingaliro lachipembedzo. Chotero tiyenitu tipende nkhaniyi mosamalitsa, makamaka popeza kuti pali miyambo ina imene ingawonekere kukhala ndi kugwirizana kofanana ndi chipembedzo chonyenga. Tamverani ndemanga zina kuchokera mu The Encyclopedia of Religion (1987):

“Maluŵa amagwirizanitsidwa ku malo opatulika kudzera mwa kugwirizanitsidwa kwawo ndi milungu ndi milungu yachikazi. Flora, mulungu wachikazi wa Roma wanyengo yangululu ndi maluŵa, amadzetsa kukongola ndi mnunkho wabwino ku maluŵa . . . Milungu ingatonthozedwe ndi kulambiridwa . . . kudzera mwakuperekedwa kwa chakudya ndi maluŵa.

“Kugwirizana kwa maluŵa ndi madzoma a imfa kumachitika kuzungulira dziko lonse. Agiriki ndi Aroma anaphimba akufa ndi manda awo ndi maluŵa. Miyoyo ya Abuddha omafa ku Japan imanyamulidwa pamwamba pa lotus, ndipo miyala ya pamanda kumanda ingakhale pa ma lotus osemedwa . . . Nzika za Tahiti zimasiya maphukusi amaluŵa okutidwa m’zisamba pandunji pa mtembo pambuyo pa imfa ndiyeno zimatsanulira pefyumu yochokera kumaluŵa pa mtembowo kukhweketsa kulowa kwake m’moyo wopatulika wapambuyo pa imfa . . . Maluŵa angapezekenso pa nthaŵi zopatulika mumpangidwe wa chofukiza kapena pefyumu.”

Pozindikira kuti maluŵa akhala akugwiritsidwa ntchito mogwirizana ndi chipembedzo chonyenga, Akristu ena alingalira kuti sayenera kupereka kapena kutumiza maluŵa ku maliro. Lingaliro lawo lingasonyezenso chikhumbo chawo chakupewa miyambo yadziko, popeza kuti otsatira a Yesu ayenera kukhala ‘osati a mbali ya dziko.’ (Yohane 15:19) Komabe, malemba a Baibulo oyenerera ndi zikhulupiriro za kumaloko ziri ndi chiyambukiro pa nkhaniyi.

Maluŵa ali mbali ya mphatso zabwino za Mulungu zoti amoyo asangalale nazo. (Machitidwe 14:15-17; Yakobo 1:17) Kukongola kwa maluŵa ake olengedwa kwagwiritsidwa ntchito m’kulambira kowona. Choikapo nyali m’hema chinakometseredwa ndi “katungulume . . . ndi maluŵa.” (Eksodo 25:31-34) Zozokotedwa m’kachisi zinaphatikizapo nkhata za maluŵa ndi migwalangwa. (1 Mafumu 6:18, 29, 32) Mwachiwonekere, kugwiritsidwa ntchito kwachikunja kwa maluŵa kapena nkhata za maluŵa sikunatanthauze kuti olambira owona nthaŵi zonse akapewa kuwagwiritsira ntchito.​—Machitidwe 14:13.

Komabe, bwanji ponena za nkhani yaikulu kwambiri ya kutsatira miyambo, yonga ngati miyambo yamaliro? Baibulo limatchula miyambo yambiri, ina yosayenera kwa olambira owona, ina yotsatiridwa ndi anthu a Mulungu. Mafumu Woyamba 18:28 amatchula “makhalidwe” a olambira Baala a ‘kukwezadi mawu ndi kudzitema’​—mwambo umene olambira owona sakanatsatira. Kumbali ina, Rute 4:7 sakupereka lingaliro lakutsutsa “mwambo wa nthaŵi zakale mu Israyeli wokhudza [njira yakulondolera] kuyenera kwa chiwombolo.”

Miyambo yovomerezedwa ndi Mulungu ingafikire kukhala kwakukulukulu nkhani zachipembedzo. Pamene Mulungu analongosola phwando la Paskha, sanatchule kugwiritsidwa ntchito kwa vinyo, koma podzafika zaka za zana loyamba, kunali kwachizoloŵezi kugwiritsira ntchito zikho za vinyo. Yesu ndi atumwi ake sanaukane mwambo wachipembedzo umenewu. Anaupeza kukhala wosatsutsika, ndipo anautsatira.​—Eksodo 12:6-18; Luka 22:15-18; 1 Akorinto 11:25.

Kuli kofanana ndi miyambo ina ya maliro. Aigupto mwamwambo anaumika akufa. Kholo lokhulupirika Yosefe sanangonena kuti, ‘Uwu ndimwambo wachikunja, chotero ife Ahebri tiyenera kuupewa.’ Mmalomwake, iye “anauza akapolo ake, asing’anga, kuti akonze atate ake ndi mankhwala osungira thupi,” mwachiwonekere kotero kuti Yakobo akakhoza kuikidwa m’manda a Dziko Lolonjezedwa. (Genesis 49:29-50:3) Pambuyo pake Ayuda anayambitsa miyambo yosiyanasiyana ya maliro, yonga ngati kusambitsa mtembo ndi kuuika m’manda patsiku la kumwalira. Akristu oyambirira anavomereza miyambo yotero Yachiyuda.​—Machitidwe 9:37.

Komabe, bwanji ngati mwambo wamaliro ukuwonedwa kukhala ndi tanthauzo lozikidwa pa cholakwa cha chipembedzo, monga ngati kukhulupirira kuti moyo uli wosakhoza kufa? Musaiwale zotchulidwa m’bukhu lanazonse kuti ena “amasiya maphukusi okutidwa m’zisamba pandunji pa mtembo pambuyo pa imfa ndiyeno amatsanulira pefyumu yochokera ku maluŵa pamtembowo kukhweketsa kulowa kwake m’moyo wopatulika wapambuyo pa imfa.” Zenizeni zakuti pangakhale mwambo wotero sizitanthauza kuti atumiki a Mulungu ayenera kupeŵa chirichonse chofanana. Pamene kuli kwakuti Ayuda sanakhulupirire mu “kulowa m’moyo wopatulika wapambuyo pa imfa,” Baibulo limati: “Anatenga mtembo wa Yesu nauzenenga ndi nsalu za bafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.”​—Yohane 12:2-8; 19:40.

Akristu ayenera kupeŵa zizoloŵezi zimene zimatsutsana ndi chowonadi cha Baibulo. (2 Akorinto 6:14-18) Chikhalirechobe, zinthu za mtundu wonse, zojambulidwa, ndi zizoloŵezi, panthaŵi ina kapena malo ena, zamasuliridwa molakwa kapena zakhala zikugwirizanitsidwa ndi ziphunzitso zosakhala zamalemba. Mitengo yakhala ikulambiridwa, chifaniziro cha mtima chakhala chikulingaliridwa kukhala chopatulika, ndipo zofukiza zagwiritsidwa ntchito m’madzoma achikunja. Kodi zimenezi zimatanthauza kuti Mkristu sayenera konse kugwiritsira ntchito zofukiza, kukhala ndi mitengo yakukometsera kulikonse, kapena kuvala majuwelo opangidwa m’chifaniziro cha mtima?a Chimenecho sichiri chosankha choyenerera.

Mkristu weniweni ayenera kudzifunsa kuti: Kodi mwambowo ukasonyeza kwa ena kuti ndavomereza zikhulupiriro kapena zizoloŵezi zosakhala zamalemba? Nyengo ya nthaŵi ndi malo zingasonkhezere yankho. Mwambo (kapena chojambulidwa) chingakhale chinali ndi tanthauzo lachipembedzo chonyenga zaka zikwi zambiri zapitazo kapena chingakhale ndi lotero lerolino kudziko lakutali. Koma popanda kulowa m’kufufuza kodya nthaŵi, dzifunseni kuti: ‘Kodi lingaliro lofala kumene ndikhala nlotani?’​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:25-29.

Ngati kuli kodziŵika bwino lomwe kuti mwambo (kapena chojambulidwa, chonga ngati mtanda) chiri ndi tanthauzo lachipembedzo chonyenga, chipeweni. Chotero Akristu sakatumiza maluŵa mumpangidwe wa mtanda, kapena mpangidwe wa mtima ngati zimenezo zimawonedwa kukhala ndi tanthauzo lachipembedzo. Kapena pangakhale njira ina yanthaŵi zonse mwa imene maluŵa amagwiritsidwa ntchito pa maliro kapena kumanda imene iri ndi tanthauzo lachipembedzo kumaloko. Mkristu ayeneranso kupeŵa zimenezo. Komabe, kumeneko sindiko kunena kuti kungopereka nkhata ya maluŵa pa maliro kapena kupatsa maluŵa kwa bwenzi limene liri m’chipatala ziyenera kulingaliridwa kukhala kachitidwe kachipembedzo kamene kayenera kupeŵedwa.b

Mosiyana, m’maiko ambiri mwambo wakupereka maluŵa uli wofala ndipo umawonedwa kukhala kukoma mtima koyenerera. Maluŵa angawonjezere kukongola ndipo angapangitse chochitika chomvetsa chisoni kukhala chosangulutsa koposa. Iwo angakhalenso chizindikiro cha chifundo ndi nkhaŵa. Kwinakwake mwambo uwu ungakhale kusonyeza malingaliro otero mwa kachitidwe kowolowa manja, konga ngati kupereka chakudya kwa odwala kapena olira. (Kumbukirani chikondi chosonyezedwa pa Dorika chifukwa chakuti iye anasonyeza chikondwerero chake ndi nkhaŵa kwa ena. [Machitidwe 9:36-39]) Pamene kutero sikumagwirizanitsidwa kotheratu ndi zikhulupiriro zonyenga, ena a Mboni za Yehova ali ndi chizoloŵezi chakupereka maluŵa okongola kwa bwenzi loikidwa m’chipatala kapena pachochitika cha imfa. Ndipo mwaumwini iwo angasonyeze mowonjezereka chikondwerero chawo ndi malingaliro mwa ntchito zopindulitsa.​—Yakobo 1:27; 2:14-17.

[Mawu a M’munsi]

a Akunja akhala akugwiritsira ntchito zofukiza zochokera kumaluŵa kwanthaŵi yaitali m’madzoma awo, koma sikunali kolakwa kuti anthu a Mulungu agwiritsire ntchito zofukiza m’kulambira kowona. (Eksodo 30:1, 7, 8; 37:29; Chivumbulutso 5:8) Onaninso mutu wakuti “Kodi Ndizo Zokometsera Zakulambira Mafano?” mu Galamukani! Yachingelezi ya December 22, 1976.

b Zofuna zabanja ziyenera kulingaliridwa, popeza kuti ena amadziŵitsa kuti aliyense wofuna kutumiza maluŵa ayenera mmalomwake kupanga zopereka ku mpingo kapena kugulu lakutilakuti lothandiza osoŵa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena