Kodi Chipembedzo Nchofunikadi?
KODI chipembedzo nchofunika kwa inu? Kodi mwina mwake ndinu membala wa gulu lachipembedzo kapena tchalitchi? Ngati nditero, ndinu wofanana kwambiri ndi anthu amene anakhalako kalelo mu 1844, chaka chimene wanthanthi Wachijeremani, Karl Marx analemba kuti: “Chipembedzo . . . ndicho mankhwala othetsa ululu a anthu.” M’masiku amenewo pafupifupi aliyense anapita kutchalitchi ndipo chipembedzo chinali ndi chisonkhezero champhamvu pa mlingo uliwonse wa chitaganya. Lerolino, zimenezo zasintha kwambiri, ndipo chipembedzo chimachita mbali yochepa kapena sichimachita mbali iriyonse m’miyoyo ya anthu mamiliyoni mazana ambiri. Ngati mumapita kutchalitchi, mwachidziŵikire muli pakati pa anthu ochepa m’mudzi mwanu.
Kodi nchiyani chimene chinapangitsa masinthidwewo? Choyamba, Karl Marx anayambitsa nthanthi yotsutsa chipembedzo imene inakhala yosonkhezera kwambiri. Mwachiwonekere, Marx analingalira chipembedzo kukhala chopinga kupita patsogolo kwa anthu. Iye ananena kuti zosoŵa za anthu zingafikiritsidwe bwino koposa mwa kukondetsa zinthu zakuthupi, nthanthi imene sinasiye mpata kwa Mulungu kapena chipembedzo chamwambo. Ichi chinamtsogolera kunena kuti: “Chofunika choyamba m’kupeza chimwemwe cha anthu ndicho kuchotsedwa kwa chipembedzo.”
Nthanthi ya Marx ya kukondetsa zinthu zakuthupi inakulitsidwa mowonjezereka ndi Friedrich Engels katswiri wamayanjano wa ku Jeremani ndi mtsogoleri wa Chikomyunizimu wa ku Russia Vladimir Lenin. Iyo inadzadziŵika kukhala Marxism-Leninism. Kufikira posachedwapa, anthu oposa mbali imodzi mwa zitatu anakhala pansi pa maulamuliro andale amene anatsatira kumlingo waukulu kapena wochepera nthanthi zokana Mulungu. Amuna ndi akazi ambiri akuterobe.
Kukula kwa Kusalabadira Zaumulungu
Koma kufalikira kwa nthanthi ya Chikomyunizimu sindiko kokha kumene kunafooketsa mphamvu ya chipembedzo pa anthu. Zochitika za m’mbali ya sayansi zinathandizirakonso. Mwachitsanzo, kutchuka kwa nthanthi ya chisinthiko kunatsogolera ambiri kukaikira kukhalapo kwa Mlengi. Ndipo panali mfundo zinanso.
Encyclopædia Britannica ikutchula “kutumbidwa kwa malongosoledwe asayansi a zinthu zomwe kale zinali kulingaliridwa kukhala zochititsidwa ndi mphamvu zosakhala zachibadwa” ndi “kuchotsedwapo kwa chisonkhezero cha chipembedzo cholinganizidwa m’mbali za ntchito monga ngati mankhwala, maphunziro ndi umisiri.” Zochitika zonga zimenezi zinatsogolera kukula kwa kusalabadira zaumulungu. Kodi kusalabadira zaumulungu nchiyani? Kukumasuliridwa monga “lingaliro la moyo . . . lozikidwa pa mfundo yakuti chipembedzo ndi kukambitsirana zachipembedzo ziyenera kunyalanyazidwa kapena kuchotsedwa mwadala.” Kusalabadira zaumulungu kuli ndi chisonkhezero champhamvu m’maiko Achikomyunizimu ndi osakhala Achikomyunizimu.
Koma kusalabadira zaumulungu ndi Marxism-Leninism sizinali zokha m’kufooketsa chisonkhezero cha chipembedzo. Matchalitchi a Chikristu Chadziko ayenera kukhalanso ndi liŵongo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kwa zaka mazana ambiri iwo anagwiritsira ntchito moipa ulamuliro wawo. Ndipo anaphunzitsa ziphunzitso zozikidwa pa miyambo yosakhala yamalemba ndi nthanthi za anthu m’malo mwa Baibulo. Chifukwa chake, ambiri m’magulu awo anafooketsedwa kwambiri mwauzimu kwakuti analephera kulaka chiukiro cha kusalabadira zaumulungu.
Ndiponso, pomalizira pake matchalitchi enieniwo anagonjera ku kusalabadira zaumulungu. M’zaka za zana la 19, akatswiri achipembedzo m’Chikristu Chadziko anapanga chisulizo chachikulu kwambiri chimene chinawonongera ambiri chikhulupiriro chakuti Baibulo liri Mawu ouziridwa a Mulungu. Matchalitchi, kuphatikizapo Tchalitchi cha Roma Katolika, anavomereza nthanthi ya chisinthiko. Inde, iwo anati anakhulupirirabe chilengedwe. Koma anavomereza kuthekera kwakuti thupi la munthu linasinthika, pamene moyo wokha ndiwo unalengedwa ndi Mulungu. Mkati mwa ma 1960, Chiprotestanti chinadza ndi maphunziro azaumulungu amene analengeza “imfa ya Mulungu.” Atsogoleri achipembedzo ambiri Achiprotestanti analekerera njira yamoyo yokondetsa zinthu zakuthupi. Iwo anavomereza kugonana ukwati usanakhale ndipo ngakhale kugonana kwa ofanana ziŵalo. Akatswiri ena a maphunziro azaumulungu Achikatolika anayambitsa nthanthi yaumulungu ya chimasuko, kuphatikiza pamodzi Chikatolika ndi chiphunzitso chachipanduko cha Marx.
Kutha kwa Kusalabadira Zaumulungu
Chotero, kusalabadira zaumulungu kunakhala kotchuka, makamaka m’ma 1960 mpaka pakati pa ma 1970. Kenaka zinthu zinasinthanso. Chipembedzo chinawonekera kukhala chikubweranso koma, osati kwenikweni matchalitchi aakulu. Kuzungulira padziko lonse, chakumapeto kwa ma 1970 ndi ma 1980 panali kuwonjezereka kwa magulu atsopano achipembedzo.
Kodi nchifukwa ninji chipembedzo chinadzukanso? Katswiri wazamayanjano wa ku Falansa Gilles Kepel ananena kuti “anthu wamba amene anaphunzira . . . amanena kuti mwambo wakudziko ndiwo unawatsogolera kunjira yopanda phindu ndikuti mwakuchoka kwa Mulungu, anthu akututa zimene anafesa mwa kunyada kwawo ndi uchabe, ndizo, kupulupudza, kusudzulana, AIDS, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, [ndi] kudzipha.”
Kutha kwa kusalabadira zaumulungu kwayambikanso mwamphamvu chiyambire kugwa kwaposachedwapa kwa Marxism-Leninism. Kwa anthu ambiri nthanthi yosakhulupirira Mulungu imeneyi inakhala chipembedzo chotsimikizirika. Pamenepo, tangoyerekezerani kudabwitsidwa kwa awo amene anaikhulupirira! Nyuzipepala ya Washington Post ya ku Moscow inagwira mawu yemwe kale anali mtsogoleri wa Communist Party Higher School amene ananena kuti: “Dziko silingadalire kokha pa chuma chake ndi ziungwe zake, komanso pa nthanthi za abambo ake oliyambitsa. Chiri chinthu chosakaza kwa chitaganya chirichonse kupeza kuti nthanthi zawo zazikulu koposa sizinazikidwe pa chowonadi koma kufalitsidwa kwa malingaliro aumwini ndi maloto. Koma zimenezo ndizo zimene tikuchita nazo tsopano m’nkhani ya Lenin ndi chipandukocho.”
Polankhula za ponse paŵiri maiko Achikomyunizimu ndi achikapitalizimu, katswiri wazamayanjano yemwenso ndi wanthanthi wa ku Falansa Edgar Morin anavomereza kuti: “Sitinawone kokha kulephera kwa mtsogolo mowala molonjezedwa kwa anthu wamba koma tawonanso kulephera kwa kupita patsogolo kwachibadwa kwa chitaganya chosalabadira zaumulungu, mmene sayansi, kulingalira, ndi demokrase zinayenera kupita patsogolo zokha. . . . Palibe kupita patsogolo komwe kukutsimikiziridwa tsopano. Mtsogolo mmene tinkayembekezera mwalepherekeratu.” Amenewo ndiwo malingaliro osapindulitsa a ambiri amene amakhulupirira zoyesayesa za anthu zakupanga dziko labwinopo popanda Mulungu.
Chikondwerero Chatsopanonso m’Chipembedzo
Lingaliro la kusakhutiritsidwa kwapadziko lonse limeneli likupangitsa anthu ambiri owona mtima kuzindikira kufunika kwa mbali yauzimu m’miyoyo yawo. Iwo amawona kufunika kwa chipembedzo. Koma samakhutiritsidwa ndi matchalitchi aakulu, ndipo ena amakaikiranso zipembedzo zatsopano—kuphatikizapo madzoma akuchiritsa, magulu odzitcha kukhala ndi mphamvu zachilendo, mipatuko yachinsinsi, ndiponso ngakhale magulu olambira Satana. Kutenthedwa maganizo kwachipembedzo kukutulutsanso zotulukapo zake zoipa. Chotero, inde, chipembedzo chikubweranso mosiyanasiyana. Koma kodi kubwereranso ku chipembedzo kumeneko kuli chinthu chabwino kwa anthu? Ndithudi, kodi chipembedzo chirichonse chimayankhadi zosoŵa zauzimu za anthu?
[Chithunzi patsamba 3]
“Chipembedzo ndicho kuusa moyo kwa cholengedwa chotsenderezedwa, malingaliro a dziko lopanda chifundo, ndi moyo wa mkhalidwe wopanda moyo. Ndicho mankhwala othetsa ululu a anthu”
[Mawu a Chithunzi]
Photo: New York Times, Berlin—33225115
[Chithunzi patsamba 4]
Vladimir Lenin (pamwambapa) ndi Karl Marx anawona chipembedzo monga chopinga kupita patsogolo kwa anthu
[Mawu a Chithunzi]
Musée d’Histoire Contemperaine—BDIC (Universitiés de Paris)
[Chithunzi patsamba 5]
Nthanthi ya Marx ndi Lenin inadzutsa ziyembekezo zazikulu m’mitima ya anthu mamiliyoni ambiri
[Mawu a Chithunzi]
Musée d’Histoire Contemperaine—BDIC (Universitiés de Paris)
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Cover photo: Garo Nalbandian