Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 4/1 tsamba 3-5
  • Ufulu Wowona—Wochokera ku Magwero Otani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufulu Wowona—Wochokera ku Magwero Otani?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsira Ntchito Ufulu Molakwa
  • Ukapolo ku Chipembedzo Chonyenga
  • Anthu Aufulu Koma Oŵerengeredwa Thayo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kuchingamira Dziko Latsopano la Mulungu la Ufulu
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi “Dongosolo Latsopano la Dziko” la Anthu Layandikira?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Ufulu wa Chipembedzo Umatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 4/1 tsamba 3-5

Ufulu Wowona​—Wochokera ku Magwero Otani?

‘Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.’​—YEREMIYA 10:23, 24.

1, 2. Kodi anthu ochuluka amauwona motani ufulu, koma kodi nchiyaninso chiyenera kupendedwa?

MOSAKAIKIRA inuyo mumaufuna ufulu wowona. Mumafuna kukhala waufulu kupereka malingaliro anu, waufulu kudzisankhira kumene ndi mmene mufuna kukhalira ndi moyo. Mumafuna kusankha ntchito imene mungailoŵe, kusankha zakudya, nyimbo, mabwenzi. Muli nazo zosankha pazinthu zambiri, zazikulu ndi zazing’ono zomwe. Palibe munthu wolingalira bwino amene amafuna kukhala kapolo kwa olamulira otsendereza, akukhala wopanda ufulu wa kusankha kapena kukhala ndi wochepa wokha.

2 Komabe, kodi simungakondenso kukhala m’dziko limene ena ndi inuyo mungakhale ndi ufulu wowona? Kodi simungakonde dziko m’limene ufulu ukatetezeredwa kotero kuti moyo wa aliyense ukakhala wokhutiritsa? Ndipo ngati kunali kotheka, kodi simukakondanso kukhala m’dziko lopanda mantha, upandu, njala, umphaŵi, kuipitsa, matenda, ndi nkhondo? Ndithudi maufulu oterowo amakhumbidwa kwambiri.

3. Kodi nchifukwa ninji timawona ufulu kukhala wofunika kwambiri?

3 Kodi nchifukwa ninji anthufe tiri ndi malingaliro amphamvu chotero ponena za ufulu? Baibulo limati: “Pamene pali Mzimu wa [Yehova, NW] pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Chotero Yehova ali Mulungu wa ufulu. Ndipo popeza kuti anatilenga ‘m’chifanizo ndi chikhalidwe’ chake, iye anatipatsa mphatso ya ufulu wa kusankha kotero kuti tiudziŵe bwino ndi kupindula nawo ufuluwo.​—Genesis 1:26.

Kugwiritsira Ntchito Ufulu Molakwa

4, 5. Kodi ndimotani mmene ufulu wagwiritsiridwa ntchito molakwa m’mbiri yonse?

4 M’mbiri yonse mamiliyoni a anthu aikidwa muukapolo, kuzunzidwa, kapena kuphedwa chifukwa chakuti ena anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wa kusankha. Baibulo limanena kuti zaka 3,500 zapitazo, ‘Aigupto anawagwiritsa ana a Israyeli ntchito yosautsa; naŵaŵitsa moyo wawo ndi ntchito yolimba.’ (Eksodo 1:13, 14) The Encyclopedia Americana imanena kuti m’zaka za zana lachinayi B.C.E., chiŵerengero cha akapolo mu Atene ndi mizinda ina iŵiri ya Agiriki chinaposa chiŵerengero cha mfulu ndi 4 kwa 1. Bukhuli limanenanso kuti: “Mu Roma, poyamba kapolo analibe kuyenera kulikonse. Anakhoza kuphedwa kaamba ka kulakwa kwakung’ono.” Compton’s Encyclopedia imati: “Mu Roma, ntchito yachibalo ya akapolo ndiyo inali maziko a boma. . . . Kaŵirikaŵiri akapolo ankagwira ntchito m’minda ali muunyolo. Usiku ankamagwidwa pamodzi ndi kutsekeredwa m’ndende zowopsa, zimene zinaloŵa pansi m’nthaka.” Popeza kuti akapolo ambiri panthaŵi ina adali mfulu, tangoyerekezerani kupweteka kwa miyoyo yozunzidwa imeneyo!

5 Kwa zaka mazana ambiri, Chikristu Chadziko chinadziloŵetsa m’malonda otsendereza ogulitsa akapolo. The World Book Encyclopedia ikunena kuti: “Kuyambira m’ma 1500 mpaka m’ma 1800, Azungu anatumiza akapolo achikuda pafupifupi 10 miliyoni kuchokera mu Afirika kumka ku Chigawo cha Kumadzulo kwa Dziko.” M’zaka za zana la 20 lino, mamiliyoni a anthu ogwidwa anagwiritsidwa ntchito m’misasa yachibalo ya Nazi kufikira imfa kapena kuphedwa molamulidwa ndi boma. Mikoleyo inaphatikizapo Mboni za Yehova zambiri zimene zinaponyedwa m’ndende chifukwa chakukana kuchirikiza ulamuliro wambanda Wachinazi.

Ukapolo ku Chipembedzo Chonyenga

6. Kodi ndimotani mmene chipembedzo chonyenga chinamangira anthu muukapolo m’Kanani wakale?

6 Palinso ukapolo wa kulondola chipembedzo chonyenga. Mwachitsanzo, m’Kanani wakale, ana ankaperekedwa nsembe kwa Moleki. Kukunenedwa kuti mkati mwa chifano chachikulu chimenechi cha mulungu wonyenga munali ng’anjo yotentha moto. Ana amoyo ankaponyedwa pamikono yotansidwa ya fanolo, namagwera pansi pake m’malaŵi a moto. Aisrayeli ena nawonso anachitako kulambira konyenga kumeneku. Mulungu amati iwo ‘anapitiriza kumoto ana awo aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene Iye sanawauze, chimene sichinaloŵa m’mtima Mwake, kuti achite chonyansacho.’ (Yeremiya 32:35) Kodi ndimapindu otani amene Moleki anadzetsera olambira ake? Kodi mitundu Yachikanani imeneyo ndi kulambira kwawo Moleki ilikuti lerolino? Yonse inazimiririka. Kunali kulambira konyenga, kulambira kozikidwa pamabodza osati zowona.​—Yesaya 60:12.

7. Kodi ndimachitachita auchiŵanda otani omwe anali mbali ya chipembedzo cha Aaztec?

7 Zaka mazana angapo zapitazo m’Central America, Aaztec anali muukapolo wa chipembedzo chonyenga. Panali milungu yaumwini, mphamvu zachilengedwe zinalambiridwa monga milungu, zochitika zosiyanasiyana m’moyo wa tsiku ndi tsiku zinali ndi mulungu wake, zomera zinali ndi milungu yawo, ngakhale imfa zakudzipha wekha zinali ndi mulungu. Bukhu lakuti The Ancient Sun Kingdoms of the Americas limasimba kuti: “Boma la Aaztec la Mexico linalinganizidwa kuyambira pamwamba kufikira pansi pake kuti likhale lolimba, ndipo motero kutonthoza, mphamvu zosawoneka mwakupereka nsembe mitima ya anthu yochuluka monga mmene kunaliri kotheka kuipatsa. Mwazi unali chakumwa cha milunguyo. Kuti apeze mikole yokwanira yopereka nsembe kwa milunguyo, panali nkhondo zazing’ono zosatha.” Pamene kachisi wamkulu wansanja ankaperekedwa mu 1486, zikwizikwi za mikole “inandandalikitsidwa m’mizera kuyembekezera kugonekedwa motambalitsidwa pamwala woperekerapo nsembe. Mitima yawo inadulidwa ndi kutukuliridwa kwakanthaŵi ku dzuŵa” kukondweretsa mulungu dzuŵa. The World Book Encyclopedia imanena kuti: “Olambirawo nthaŵi zina anadya mbali zina za thupi la mkole.” Chikhalirechobe, machitachita amenewo sanapulumutse Ufumu wa Aaztec kapena chipembedzo chawo chonyenga.

8. Kodi wowonetsa alendo ocheza ananenanji ponena za kupha anthu kwamakono kwakukulu koposa kuja kochitidwa ndi Aaztec?

8 Panthaŵi ina, alendo ena anali kuyenda m’myuziyamu m’mene munali chisonyezero cha ansembe Achiaztec akudula mtima wa mnyamata wina. Pamene wowawonetsayo anafotokoza chisonyezerocho, ena m’kagulu ka alendowo anachita kakasi. Wowawonetsayo anati: “Ndikuwona kuti mwasokonezeka maganizo ndi mchitidwe wa Aaztec wa kupereka nsembe anyamata kwa milungu yachikunja. Komabe, m’zaka za zana la 20 lino, anyamata mamiliyoni ambiri aperekedwa nsembe kwa mulungu wa nkhondo. Kodi zimenezo zakhalako bwino?” Nzowona kuti m’nkhondo atsogoleri achipembedzo a mitundu yonse amapempherera chilakiko ndi kudalitsa magulu ankhondo ngakhale kuti anthu achipembedzo chimodzimodzicho kaŵirikaŵiri amapezeka kumbali zonse ziŵiri zomenyanazo akumaphana.​—1 Yohane 3:10-12; 4:8, 20, 21; 5:3.

9. Kodi ndimchitidwe wotani umene umawononga miyoyo ya ana kuposa chochitika chirichonse cha m’mbiri?

9 Kupereka nsembe ana kwa Moleki, kwa milungu ya Aaztec, kapena ku nkhondo kukupambanidwa ndi kuphedwa kwa makanda osabadwa mwakutaya mimba, makanda pafupifupi 40 kapena 50 miliyoni pachaka padziko lonse. Chiŵerengero cha mimba zotaidwa m’zaka zitatu zapita zokha chimaposa anthu mamiliyoni zana limodzi ophedwa m’nkhondo zonse za m’zaka za zana lino. Chaka ndi chaka, makanda amataidwa ochuluka kuposa anthu onse ophedwa m’zaka 12 za ulamuliro Wachinazi. M’zaka makumi zaposachedwapa zikwizikwi zowonjezereka za makanda ataidwa kuposa ana onse operekedwa nsembe kwa Moleki kapena kwa milungu ya Aaztec. Chikhalirechobe, ambiri (ngati sindiwo ochuluka) amene amataya mimba, kapena amene amataitsa, amadzinenera kukhala opembedza.

10. Kodi ndinjira ina iti imene anthu akhalira akapolo ku chipembedzo chonyenga?

10 Chipembedzo chonyenga chimaika anthu muukapolo mwanjira zinanso. Mwachitsanzo, anthu ambiri amakhulupirira kuti akufa ali amoyo m’dziko la mizimu. Chimodzi cha zotulukapo za chikhulupiriro chonyenga chimenecho ndicho kuwopa ndi kulambira makolo akufa kuti apeze mapindu amene amawalingalira kuti amabwera kuchokera kwa iwo. Izi zimaika anthu muukapolo kwa asing’anga, obwebweta, ndi atsogoleri achipembedzo amene amapemphedwa kuthandiza amoyo kukondweretsa akufa. Pamenepa tikhoza kufunsa kuti, Kodi pali njira iriyonse yotulukira muukapolo woterowo?​—Deuteronomo 18:10-12; Mlaliki 9:5, 10.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

M’mbiri yonse anthu ena agwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo wa kusankha namaika ena muukapolo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena