Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 4/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 4/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi nchifukwa ninji asilikali a Sauli sanaphedwe pamene anadya nyama yokhala ndi mwazi, popeza kuti chimenecho ndicho chinali chilango chonenedwa m’Chilamulo cha Mulungu?

Amuna ameneŵa anaswadi lamulo la Mulungu lonena za mwazi, koma iwo angakhale atachitiridwa chifundo chifukwa chakuti anali kulemekeza mwazi, ngakhale kuti anafunikira kukhala osamala kwambiri ponena za kusonyeza ulemu umenewo.

Talingalirani za mkhalidwewo. Aisrayeli pansi pa Mfumu Sauli ndi mwana wake Jonatani anali pankhondo ndi Afilisti. Atafika pamkhalidwe umene “Aisrayeli anasauka” m’nkhondoyo, Sauli mofulumira anachita lumbiro lakuti amuna ake ankhondo sayenera kudya kufikira mdaniyo atagonjetsedwa. (1 Samueli 14:24) Lumbiro lakelo linadzetsa vuto posapita nthaŵi.

Amuna akewo anali kupambana m’nkhondo yovutayo, koma zoyesayesazo zamphamvuzo zinali ndi ziyambukiro zoipa. Anakanthidwa ndi njala ndi kutopa. Kodi iwo anachitanji mumkhalidwe wovuta kwambiri umenewo? “Anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng’ombe, ndi ana a ng’ombe, naziphera pansi; anthu nazidya zili ndi mwazi wawo.”​—1 Samueli 14:32.

Kumeneko kunali kuswa lamulo la Mulungu lonena za mwazi, monga momwe anthu ena a Sauli anamuuzira, kuti: “Onani anthu alikuchimwira Yehova, umo akudya zamwazi.” (1 Samueli 14:33) Inde, Chilamulo chinanena kuti pamene nyama zinaphedwa, mwazi unafunikira kukhetsedwa nyamayo isanadyedwe. Mulungu sanalamulire kuti pakhale njira zina zomkitsa zokhetsera mwazi. Mwa kutsatira masitepe oyenera okhetsera mwazi, atumiki ake akasonyeza ulemu patanthauzo la mwazi. (Deuteronomo 12:15, 16, 21-25) Mwazi wa nyama ukagwiritsiridwa ntchito monga nsembe paguwa, koma sunayenere kudyedwa. Kuswa dala lamulolo kunali ndi chilango cha imfa, pakuti anthu a Mulungu anauzidwa kuti: “Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama iliyonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzasadzidwa.”​—Levitiko 17:10-14.

Kodi asilikali a Mfumu Sauli anali kuswa mwadala Iamulolo? Kodi iwo anali kusonyeza kunyalanyaza kotheratu lamulo laumulungu lonena za mwazi?​—Yerekezerani ndi Numeri 15:30.

Sitiyenera kugamula motero. Cholembedwacho chimanena kuti iwo ‘anaphera nyamazo pansi nazidya zili ndi mwazi wawo.’ Chotero iwo angakhale atayesayesa kukhetsa mwaziwo. (Deuteronomo 15:23) Komabe, mumkhalidwe wawo wotopa ndi wanjalawo, sanalenjeke nyama zophedwazo ndi kulola nthaŵi yoyenera kuti mwazi ukhe moyenerera. Iwo anaphera “pansi” nkhosa ndi ng’ombe, kumene kunaletsa kukha kwa mwazi wonse. Ndipo anacheka nyamayo mofulumira imene mwina inali m’mwazi. Chifukwa chake, ngakhale ngati iwo anali kukumbukira za kumvera lamulo la Mulungu, sanatsatire njira zoyenera kapena kufikira kumlingo woyenera.

Chotulukapo chake chinali chakuti ‘anthu anazidya zili ndi mwazi wawo,’ kumene kunali kuchimwa. Sauli anazindikira zimenezi ndipo analamula kuti akunkhunize mwala waukulu kwa iye. Iye analamula asilikaliwo kuti: “Abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng’ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi.” (1 Samueli 14:33, 34) Asilikali aliwongowo anamvera, ndipo “Sauli anamangira Yehova guwa la nsembe.”​—1 Samueli 14:35.

Mwinamwake kuphera nyama pamwalapo kunachititsa kukhetsedwa kwa mwazi koyenerera. Nyama ya ng’ombe kapena ya nkhosa ikadyedwera patali ndi pamalo opherawo. Sauli angakhale atagwiritsira ntchito wina wa mwazi wokhetsedwawo paguwa la nsembe pofunafuna chifundo cha Mulungu kwa awo amene anachimwa. Yehova anasonyeza chifundocho, mwachionekere chifukwa chakuti anadziŵa zoyesayesa zimene asilikaliwo anapanga ngakhale kuti iwo anali otopa ndi anjala. Mulungu angakhalenso atalingalira kuti lumbiro lochitidwa mofulumira la Sauli linaloŵetsa amuna ake ankhondo mumkhalidwe wovuta.

Chochitika chimenechi chimasonyeza kuti mkhalidwe wangozi suli chodzikhululukira nacho chonyalanyazira lamulo la Mulungu. Chiyeneranso kutithandiza kuona kufunika kwa kulingalira mosamala tisanapange lumbiro, pakuti kuwinda kofulumira kukhoza kudzetsa mavuto kwa ife enife ndi ena.​—Mlaliki 5:4-6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena