Mbali ya Mafunso
◼ Kodi Maphunziro Abuku Ampingo ayenera kuchititsidwa liti?
Kaŵirikaŵiri kumakhala kothandiza ndi koyenerera kukhala ndi magulu angapo a phunziro labuku okumana m’malo osiyanasiyana m’gawo lonse la mpingo mmalo moti aliyense adzisonkhana pa Nyumba Yaufumu. Maphunziro ameneŵa ayenera kuchititsidwa panthaŵi yoyenera koposa kwa unyinji wogaŵiridwa kufikapo. Kaŵirikaŵiri, limakhalapo madzulo a tsiku la mkati mwa mlungu pamene palibe misonkhano ina kapena ntchito yautumiki yolinganizidwa. Komabe, kungakhale kopindulitsa kukhala ndi phunziro labuku masana kuti padzifika okalamba amene amazengereza kuyenda kutada ndi ogwira ntchito usiku. M’zochitika zochepa, kungakhale kothandiza kukhala ndi phunziro lamasana kumapeto kwa mlungu.
Akulu angafufuze moyenerera kuti asankhe nthaŵi za misonkhano zimene zidzakhala ‘zokomera unyinji wa ofalitsa’ limodzinso ndi okondwerera. (om-CN tsa. 62) Nthaŵi yosankhidwayo iyenera kukhala pa tsiku ndi ola limene silidzasokoneza mosayenerera kapena kutsekereza makonzedwe olinganizidwa a utumiki wakumunda.