Gwiritsirani Ntchito Magazini Kuuza Ena Choonadi
1 Kufunika kwa chidziŵitso choona, chenicheni, kumaluluzidwa m’chitaganya lerolino chifukwa cha kusatsa malonda kokuza zinthu ndi pakamwa, malonjezo onyenga andale, ndi manenanena onyenga apadziko lonse. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! n’ngapadera kwambiri m’njira yakuti ndi okhawo amene amalengeza choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu ndi kufotokoza zimene onse ayenera kuchita kuti akalandire madalitso osatha amene uzadzetsa.
2 M’dziko lina mkulu wa unduna wofalitsa nkhani amene anayamikira kufunika kwa magazini aŵiri ameneŵa anathandiza mosazengereza popeza chilolezo chakuti azigaŵiridwa. Iye anati: “Ndimalingalira Nsanja ya Olonda kukhala amodzi a magazini abwino koposa; ndili wokondwa kwambiri kuthandiza.” Ndi mwaŵi wathu kuthandiza ena mwa kugaŵira magazini ameneŵa amene angapereke chidziŵitso chopatsa moyo. (Yoh. 17:3) Kodi mudzagaŵira motani magazini amtengo wapatali ameneŵa m’May? Mwinamwake malingaliro otsatirawa adzakhala othandiza.
3 Ngati mukusonyeza nkhani zoyamba mu “Nsanja ya Olonda” ya May 15, munganene kuti:
◼ “Tikulankhula ndi anthu ponena za buku logulitsidwa koposa mabuku onse padziko. Kodi mukulidziŵa? [Yembekezerani yankho.] Tikunena za Baibulo. Payenera kukhala chifukwa chabwino kwambiri chimene chachititsa anthu ambirimbiri kugula Baibulo. Chifukwacho chikupezeka pa 2 Timoteo 3:16.” Mutaŵerenga lembalo, sonyezani mfundo zoyenera mu imodzi ya nkhanizo.
4 Kapena pambuyo pa kudzidziŵikitsa kwachidule, munganene motere:
◼ “Mwinamwake inu mwamva anthu ena akunena kuti: ‘Ngati ndiŵerenga Baibulo, zimenezo nzokwanira.’ N’zoonadi kuti anthu ambiri angathe kuphunzira zambiri mwa kudziŵerengera Baibulo. Ngati cholinga chawo chili cha kuphunzira choonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake, zimene akuchitazo nzoyamikirika kwambiri. [Ŵerengani Machitidwe 17:11.] Komatu, kuti tinene zoona, kodi tingapeze tanthauzo lake lonse popanda chithandizo?” Yembekezerani yankho. Ndiyeno sonyezani zina za ziphunzitso za Baibulo zimene munthu afunikira kuzidziŵa mu nkhani za chipembedzo monga momwe zafotokozedwera m’nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda ya May 1 ndipo sonyezani kufunika kwa kulembetsa sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda.
5 Pa zolembapo zanu za maulendo obwereza, mwina muli ndi mpambo wa awo amene anakondwerera pang’ono poyamba, komano palibe chilichonse chimene chinachitika. Popeza kuti panangokhala chikondwerero chochepa, mwina simungafune kupitirizabe kufikira anthuwo. Komanso mukhoza kugwiritsira ntchito mpambo umenewu kuyambitsira njira ya magazini. Pamene muona nkhani ina imene mukulingalira kuti ingakope munthu wakutiwakuti, tsimikizirani kukafikira munthuyo ndi kukamgaŵira magaziniwo ndi kumlimbikitsa kuti alembetse sabusikripishoni.
6 Umboni Wamwamwaŵi: Imeneyi ili njira yabwino kwambiri yokulitsira chikondwerero m’magazini. Kusonyeza mwanzeru zikuto zokongola kungakhale kokwanira kuyambitsira makambitsirano. Mlongo wina anayala makope pa desiki lake kotero kuti antchito anzake athe kuwaona pamene anali kudutsa; iye anakhoza kugaŵira ochulukirapo. Tsimikizirani kunyamula makope angapo, ndipo yambani kuwagaŵira mwezi uno pamene mumka kokagula zinthu, kusukulu, pokwera basi, kapena pamene mukumana ndi anthu ena kwina kulikonse.
7 Tapeza mayankho a mafunso ofunika ponena za Yehova ndi kulambira kwake mothandizidwa ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tikufuna kugwiritsira ntchito magazini ameneŵa m’njira iliyonse yothekera kuthandiza ena kuti adziŵe “Yehova, Mulungu wa choonadi.”—Salmo 31:5.