Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/95 tsamba 1
  • Uthenga wa Ufumu Wapadera wa Aliyense

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uthenga wa Ufumu Wapadera wa Aliyense
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • “Akuchuluka m’Ntchito ya Ambuye”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Gaŵirani Uthenga wa Ufumu Na. 35 Kulikonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Bwererani kwa Amene Anachita Chidwi ndi Uthenga Wa Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 5/95 tsamba 1

Uthenga wa Ufumu Wapadera wa Aliyense

1 Kuyambira pa April 24, tinayamba kugaŵira anthu onse Uthenga wa Ufumu wapadera umene wasonkhezera chidwi cha anthu ofuna kudziŵa kulikonse! Uthenga wake suli kokha wapanthaŵi yake komanso uli wofulumira. Ofalitsa mumpingo uliwonse asonyeza chichirikizo cha mtima wonse, akumafuna kupereka uthenga umenewu kwa anthu zikwi zambiri. Kodi inu mukuyesetsa kukhala ndi phande lokwanira?

2 Mtokoma wa Uthenga wa Ufumu unatumizidwa ku mpingo uliwonse, ukumapereka pafupifupi matrakiti 30 kwa wofalitsa aliyense ndipo 100 kwa mpainiya aliyense. Kodi inu mwagaŵira angati? Ngati simunakhoze kuchita zambiri monga momwe munayembekezerera, kodi mwalingalirapo njira zochitira zambiri kugaŵirako kusanathe pa May 14? Bwanji za kulembetsa monga mpainiya wothandiza? Kodi mungagwiritsire ntchito mwaŵi wa misonkhano ina yokonzekera utumiki mkati mwa mlungu, monga ija ya umboni wa madzulo?

3 Akulu adzapenda mosamalitsa kufoledwa kwa gawo. Ngati mpingo wina sukhoza kugwira ntchito m’magawo ake ena, akulu ayenera kupempha thandizo ku mipingo yoyandikana nawo. Kuyesayesa kwathu kwa mtima wonse, limodzi ndi kuchita bwino zinthu mogwirizana kwa mipingo, kudzathandizira ntchitoyo kuchitidwa.

4 Mwinamwake inu mwapeza chisangalalo chinanso mu ntchito imeneyi chifukwa chakuti ambiri akhoza kukhalamo ndi phande, kuphatikizapo ofalitsa atsopano ndi achichepere. Tikhulupirira kuti, mzimu umenewu wa chisangalalo udzapitiriza, ukumalimbikitsa onse kubwerera kukaonana ndi awo amene asonyeza chidwi. Tinalimbikitsidwa kusunga zolembapo zolondola za kunyumba ndi nyumba, tikumalemba awo amene ali okondwerera. Mbali yotsirizira ya May idzakhala nthaŵi yabwino ya kuika mtima pa maulendo obwereza ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro atsopano.

5 Kodi tinganenenji pamene tibwererako? Mwina mungapeze kukhala kogwira mtima kunena kuti: “Mwina mukukumbukira mawu osindikizidwa aja amene ndinakusiyirani posachedwapa; ndikhulupirira kuti munali ndi mpata wa kuwaŵerenga ndi kusinkhasinkha za nkhaniyo. Uthenga wake wasonkhezeradi anthu ambiri kukambitsirana za nkhaniyo mwathu muno, popeza kuti ukukhudza nkhani zofunika zimene zikuvutitsa anthu onse.” Sonyezani mawu ena osonkhezera malingaliro patsamba lachiŵiri, ndiyeno funsani kuti: “Kodi muganiza kuti nchiyani chimene tifunikira kuchita kuti titsimikizire kuti tili okonzekera zimene ziti zidze mtsogolomu?” Yembekezerani yankho. Ngati akusonyeza chikondwerero, fotokozani mfundo zina pa masamba 2-4 za Uthenga wa Ufumu, ndi kumpempha kuchita naye phunziro la Baibulo kapena kumgaŵira sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda.

6 Ngati mugwira ntchito m’gawo la mpingo wina, tsimikizirani kupereka maina alionse a anthu okondwerera amene mupeza kotero kuti ofalitsa a mpingowo apange maulendo obwereza. Mofananamo, ngati mwapatsidwa maina a anthu oti mukawafikire, musalephere kufikako mofulumira.

7 Kugaŵira kwapadera kwa Uthenga wa Ufumu umenewu kwadzutsa chidwi ndipo kwasonkhezera ife tonse kukulitsa zoyesayesa zathu m’ntchito yolalikira Ufumu. Tili ndi chidaliro chakuti kudzakhala ndi chipambano chachikulu, kukumawonjezera kuzindikira kwa anthu kulikonse za dzina lalikulu la Yehova ndi chifuno chake. (Yes. 12:4, 5) Pamene tili okhoza kuchita zambiri, mpamenenso chisangalalo chathu chidzakhala chachikulu.—Sal. 126:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena