Maulendo Obwereza Achipambano Amafuna Kuphunzitsa Kogwira Mtima
1 Maulendo obwereza ali mbali yofunika ndi yosangalatsa ya utumiki wathu wakumunda. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi khama la kubwereranso kwa okondwerera? Dzina la Yehova limadziŵikitsidwa ndi kulemekezedwa mwa ntchito yopanga ophunzira imeneyi, ndipo anthu owopa Mulungu amathandizidwa kupeza njira ya ku moyo. (2 Akor. 2:17–3:3) Kuzindikira kuti zimenezi zimaloŵetsamo kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi miyoyo ya ena kuyenera kutisonkhezera kukonzekera bwino tisanabwerereko.
2 Mphunzitsi wabwino amathandiza wophunzira wake kumanga pamaziko okhazikitsidwa kale. Monga momwe mphunzitsi wa kusukulu amamangira pa chidziŵitso chimene ana a sukulu amapeza tsiku ndi tsiku, ifenso tiyenera kupitiriza ulendo wathu woyamba ndi ndemanga zowonjezera pankhani imodzimodziyo. Zimenezi zimapitiriza nkhaniyo ndi kuwonjezera chidziŵitso.
3 Pamene mubwerera kumene munagaŵira brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” mungapeze izi kukhala zogwira mtima:
◼ “Paulendo wanga uja, tinakambitsirana za ‘masiku otsiriza’ otchulidwa m’Baibulo ndi zimene amatanthauza kwa ife. Mungadabwe kuti kodi timadziŵa motani kuti tikukhala m’masiku otsiriza. (2 Tim. 3:1) Ophunzira a Yesu analakalaka kudziŵa yankho la funso limenelo. [Ŵerengani Mateyu 24:3.] Yesu poyankha, anafotokoza mikhalidwe imene tikuona lerolino. Imeneyi imaphatikizapo nsautso ndi chiwawa zimene sizinaonekepo ndi kale lonse.” Tchulani mbali ya chizindikiro yolongosoledwa m’ndime 3 ndi 4 patsamba 19. Tchulani mbali zina za chizindikiro m’ndime 5 mpaka 8 patsamba 20. Lonjezani kubweranso kuti mudzayankhe mafunso ofunsidwa pachikuto cha broshalo.
4 Kuti mupitirize chikondwerero cha munthu m’brosha lakuti “Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?” munganene kuti:
◼ “Ndakhala wofunitsitsa kupitiriza kukambitsirana kwathu ponena za chifuno chathu cha kukhala ndi moyo. Ndiganiza kuti tonse timavomereza kuti Mulungu anafuna kuti tikhale pa dziko lapansi m’mikhalidwe yachimwemwe ndi yamtendere m’malo mwa chipwirikiti chimene tili nacho lerolino. Kodi muganiza kuti adzakwaniritsa lonjezo lake?” Yembekezerani yankho. Ŵerengani Yesaya 55:11, ndiyeno kambitsiranani malingaliro a m’ndime 25 mpaka 27 patsamba 30. Mulangizeni kuti phunziro laumwini la Baibulo ndilo njira yabwino koposa yopezera chifuno chopindulitsa cha moyo.
5 Kuti tipitirize chikondwerero chimene chinasonyezedwa m’brosha lakuti “Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!” mungalitambasulenso ndi kunena kuti:
◼ “Tinakambitsirana za dziko lokongola losonyezedwa pano pachikuto cha brosha ili. Ndikufuna kukuuzani chifukwa chake chikhulupiriro mwa Yesu chili chofunika kwa anthu ofuna kukhala mmenemu.” Pitani pa chithunzithunzi 41, ndi kuŵerenga Yesaya 9:6. Sonyezani chithunzithunzi 62, ndiyeno ŵerengani Yohane 3:16, ndi kugogomezera kufunika kwa kumvera. Fotokozani kuti Mboni za Yehova zikuthandiza anthu kuphunzira mmene angasonyezere chikhulupiriro mwa kuphunzira Baibulo ndi kuyesa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi uphungu wake.
6 Pambuyo pa ulendo wobwereza uliwonse, upendeni ndi cholinga cha kufuna kuwonjezera kugwira mtima kwanu. Dzifunseni kuti: Kodi ndinali ndi kanthu kena kotsimikizirika m’maganizo konena? Kodi ndinali ndasumika makambitsirano athu pa Baibulo? Kodi ndamanga pamaziko okhazikitsidwa paulendo woyamba? Kodi ulaliki wanga unali ndi cholinga chotsogolera ku phunziro la Baibulo? Mayankho otsimikizirika amapatsa chidaliro chakuti mukuyesayesa kukhala mphunzitsi wabwino wa Mawu a Mulungu.