Kulengeza Choonadi Tsiku ndi Tsiku Motsanzira Yesu
1 Yesu anali ndi ntchito yapadera yochita pamene anadza ku dziko lapansi. Inali yapadera kwambiri: ‘Kukachita umboni ndi choonadi.’ (Yoh. 18:37) Analengeza choonadi cha mikhalidwe ndi zifuno zodabwitsa za Atate wake. Ntchito imeneyi inali ngati chakudya kwa iye; moyo wake wonse unali pantchitoyo. (Yoh. 4:34) Luka anasimba kuti Yesu anapitiriza ‘kuphunzitsa m’kachisi tsiku ndi tsiku.’ (Luka 19:47) Yesu anagwiritsira ntchito nthaŵi yonse imene inalipo. (Yoh. 9:4) Atatsala pang’ono kufa, anatha kunena kwa Atate wake kuti: “Ine ndalemekeza inu padziko lapansi, mmene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.”—Yoh. 17:4.
2 Pamene mitima yathu idzala ndi chiyamikiro chifukwa cha zonse zimene Yehova wachita, nafenso timasonkhezeredwa kunena za iye tsiku ndi tsiku. Timakhala monga momwe analili ophunzira a Yesu amene ananena molimba mtima kuti: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Kulankhula kwawo za Yehova kunali kopitiriza, pakuti mbiri imafotokoza kuti ‘masiku onse, . . . sanaleka.’ (Mac. 5:42) Tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wotsanzira Mphunzitsi wanga, Yesu?’
3 Kulalikira Mwachangu: Yesu ananeneratu kuti pamene uthenga wa Ufumu udzalengezedwa padziko lonse lapansi, “pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mat. 24:14) Zimenezi ziyenera kukhomereza mwa ife kufunika ndi kufulumira kwa ntchito yathu. Pokhala ndi miyoyo ya mamiliyoni enieni ambiri imene ili pachiswe, palibe ntchito yofunika koposa ndi yopindulitsa kuposa imeneyi. Popeza kuti dongosolo lino la zinthu likuyandikira mapeto ake, nthaŵi imene yatsala yomalizira ntchitoyi yafinimpha!
4 Malipoti akusonyeza kuti Yehova akufulumiza kusonkhanitsidwa kwa anthu onga nkhosa. (Yes. 60:22) Ku mbali zambiri za dziko, anthu akuloŵa kwenikweni m’choonadi, akumalengeza pamenepo mwachisangalalo kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu”! (Zek. 8:23) Mawu a Yesu akuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. . . . Pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake,” ali oonadi kuposa kale lonse. (Mat. 9:37, 38) Kodi zimenezo sizimatisonkhezera kukhala achangu monga momwe analili ophunzira a Yesu amene “anakhala chikhalire m’kachisi, nalikuyamika Mulungu”?—Luka 24:53.
5 Dziŵikitsani Choonadi Tsiku ndi Tsiku: Tsiku lililonse, tiyenera kufunafuna njira zoperekera choonadi kwa ena. Mipata imapezeka mosavuta. Kodi mungapatule nthaŵi ya kuimbira foni bwenzi kapena mnansi wina amene mukulingalira kuti angamvetsere? Kapena bwanji za kulembera kalata munthu wina amene simunathe kumpeza panyumba? Kodi mwalingalirapo za kugaŵira trakiti kwa wogulitsa m’sitolo pamene mukugula zinthu? Mosakayikira, mungalingalire za mipata ina yambiri imene mumakhala nayo tsiku lililonse kuti muuze ena za chiyembekezo chanu. Ngati mupanga kuyesayesa ndi kuwonjezera kulimba mtima pang’ono, Yehova adzakuthandizani.—1 Ates. 2:2.
6 Chotero, pamene tiyamba ntchito za tsiku lililonse, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzachitapo kanthu kuuza munthu wina za chiyembekezo changa ngati lero mpata utseguka?’ Tsanzirani mkhalidwe wa Yesu, amene anafotokoza chifukwa chimene anatumidwira ku dziko lapansi: ‘Kundiyenera ine ndilalikire uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 4:43) Ngati tikufuna kukhala ngati Mphunzitsi wathu, tidzachita chimodzimodzi.—Luka 6:40.