Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/96 tsamba 8
  • Funafunani Aja Ofuna

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Funafunani Aja Ofuna
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Lankhulani Choonadi kwa Mnzanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • “Chikhulupiriro Chidza ndi Mbiri”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini Apanthaŵi Yake a Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Konzekerani Ntchito ya Kugaŵira Sabusikripishoni mu April
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 4/96 tsamba 8

Funafunani Aja Ofuna

1 Chifuno china cha ntchito yolalikira ndicho kupeza aja “ofuna moyo wosatha.” (Mac. 13:48, NW) Kugaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwakhala njira yabwino kwambiri yochitira zimenezi, popeza magazini athu amadziŵitsa anthu za chiyembekezo cha Ufumu. Tidzakhala tikugaŵira magazini m’April. Tikhulupirira kuti kumene tidzapeza anthu amene akufuna, tidzayambitsa maphunziro a Baibulo atsopano m’buku lakuti Knowledge That Leads to Everlasting Life. Nazi njira zina zimene zingagwire ntchito kwa inu:

2 Pogwiritsira ntchito “Nsanja ya Olonda” ya April 1, mungasonyeze nkhani yakuti “Tamandani Mfumu Yamuyaya!,” imene ikufotokoza nkhani yapoyera ya msonkhano wachigawo wa chaka chatha, ndi kunena kuti:

◼ “Anthu ambiri amene timalankhula nawo ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Ena amapeza vuto kukhulupirira mwa iye. Nanga inuyo? [Yembekezerani yankho.] Tazingidwa ndi umboni woonekera bwino wosonyeza kuti Mulungu ayenera kukhalako. [Ŵerengani Salmo 104:24.] Titaona kamera kapena wailesi, timavomereza msanga kuti inapangidwa ndi mlinganizi wina wanzeru. Kodi kungakhale kwanzeru kunena kuti zinthu zocholoŵana koposa, monga dziko lapansi ndi ife anthu, tinakhalako mwangozi?” Gwiritsirani ntchito ndime ya m’nkhaniyo kusonyeza chifukwa chomveka chokhulupirira mwa Mulungu. Gaŵirani magazini ndi sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda.

3 “Nsanja ya Olonda” ya April 15 ili ndi nkhani yakuti “Chifukwa Chake Kulambira Koona Kumakhala ndi Dalitso la Mulungu.” Musanaisonyeze, mukhoza kufunsa kuti:

◼ “Popeza kuti muli zipembedzo mazana ambiri m’dziko, kodi muganiza zonse zingakhale zovomerezeka kwa Mulungu? [Yembekezerani yankho.] Yesu analosera kuti mosasamala kanthu za zonena za anthu ambiri opembedza, aja amene sachita chifuniro cha Mulungu adzakanidwa. [Ŵerengani Mateyu 7:21-23.] Nkofunika kuti tidziŵe chipembedzo choona chimene Yesu anaphunzitsa.” Tsegulani pamutu wakuti “Kodi Chipembedzo Choona Chiyenera Kupatsa Zipatso Zotani?,” kuyambira patsamba 16, ndipo kambitsiranani chitsanzo chimodzi kusonyeza mfundoyo.

4 Posonyeza nkhani yaikulu ya mu “Galamukani!” wa May 8, yakuti “Pamene Sikudzakhalanso Nkhondo,” mungaganize zonena kuti:

◼ “M’zaka za zana lino mwachitika nkhondo zambirimbiri, kuphatikizapo nkhondo zadziko ziŵiri. Komatu atsogoleri onse a dziko amati akufuna mtendere. Aliyense amene ndimadziŵa amanena chimodzimodzi. Ngati aliyense akufuna mtendere, nchifukwa ninji satha kuupeza? [Yembekezerani yankho.] Kodi muganiza nchiyani chimene chikufunika kuti tione mtendere weniweni padziko lapansi?” Pambuyo pa yankho la mwini nyumba, tsegulani pamasamba 8 ndi 9 ndi kuŵerenga malemba onga Salmo 46:8, 9. Mukumagwiritsira ntchito zithunzithunzi ndi malemba ogwidwa mawu, sonyezani mmene Ufumu wa Mulungu udzadzetsera mtendere umene udzakhalako kosatha. Gaŵirani magazini kapena sabusikripishoni, ndipo linganizani ulendo wobwereza.

5 Mukapeza ambiri amene anena kuti ali otanganitsidwa, mungayese zotsatirazi:

◼ “Tikufuna kuthandiza anthu amene ali ndi moyo wotanganidwa ndi amene alibe nthaŵi yochuluka yolingalira pa zinthu zauzimu m’moyo. Magazini athu, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, akonzedwa kupereka chidziŵitso chachidule cha nkhani zofunika zimene zimakukhudzani inu ndi banja lanu. Ndikufuna kukusiyirani makopewa kuti muŵerenge.”

6 Tsimikizirani kugaŵira magaziniwo ndi sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda pampata uliwonse. Anthu adzapinduladi mwa kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, zimene zimadzetsa “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”—Yes. 52:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena