Lankhulani Choonadi kwa Mnzanu
1 Limodzi la malamulo aŵiri aakulu koposa ndilo lakuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mat. 22:39) Chikondi chotere chidzatisonkhezera kugaŵana ndi mnzathu chinthu chabwino kwambiri chimene tili nacho—choonadi chimene tapeza m’Mawu a Mulungu. Popeza kuti magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amafotokoza mwatsatanetsatane uthenga wa Baibulo wa choonadi, kugaŵira magazini ameneŵa m’mwezi wa May ndiko njira ina yakuti ‘tilankhule zoona ndi anzathu.’—Aef. 4:25.
2 “Galamukani!” wa May 8 ayenera kugaŵiridwa mpaka pamene mtokoma wanu utha. Mungayambe ulaliki wanu mwa kufunsa kuti:
◼ “Kodi mukulingalirapo bwanji ponena za dziko lopanda nkhondo? [Yembekezerani yankho.] Kodi mumadziŵa kuti zipembedzo za dziko kwenikweni zimasonkhezera nkhondo ndi kuphana? [Yembekezerani yankho.] Komabe, taonani zimene Baibulo limanena zimene alambiri oona a Mulungu adzachita.” Ŵerengani Yesaya 2:2-4 kuyambira pamwamba patsamba 4 ya magaziniwo, ndiyeno patsamba 10 ŵerengani ndime yoyamba pansi pa kamutu kakuti “Chiitano kwa Okonda Mtendere.” Ndiyeno, funsani kuti: “Kodi mukudziŵa mmene Mulungu adzachitira zimenezo? Yankho likupezeka m’magazini awa, ndipo limeneli ndi kope lanu kuti muliŵerenge.”
3 Pogaŵira “Nsanja ya Olonda” ya May 15, yesani kutchula za nkhani ya panyuzi imene yachititsa anthu kumva kukhala osasungika, ndiyeno funsani kuti:
◼ “Kodi mukulingalira kuti tiyenera kuchita chiyani kuti timve kukhala osungikadi m’moyo uno? [Yembekezerani yankho.] Kunena mosabisa, kodi tingadaliredi anthu kuti ndiwo adzathetsa mavuto amene ife anthu tikukumana nawo? [Yembekezerani yankho; ndiyeno ŵerengani Salmo 146:3.] Ndiyeno wamasalmo akutipatsa chifukwa choyembekezera zabwino mtsogolo. [Ŵerengani Salmo 146:5, 6.] Nkhani iyi yakuti ‘Chisungiko Chenicheni, Tsopano Ndiponso Kosatha,’ ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kudalira Yehova Mulungu kuti adzabweretsa mikhalidwe yabwino koposa padziko lapansi.” Gaŵirani magazini angapo ndipo linganizani kudzabweranso kudzakambitsirana mmene kulili kotheka kukhala ndi moyo wosungika tsopano lino.
4 Nkhani yapachikuto ya “Galamukani!” wa June 8 idzakopa chikondwerero cha anthu kukhomo ndi khomo ndi m’gawo lamalonda lomwe. Mungaisonyeze mwa kunena kuti:
◼ “Akazi ambiri akumana ndi vuto la kuvutitsidwa ndi amuna kumalo antchito. Mkhalidwewo wakula kwambiri kwakuti makhoti ayamba kulanga olakwa ndi kulipira olakwiridwa. Pofuna kuthandiza anthu, tafalitsa nkhani iyi, imene ikutsutsa mabodza ofala ponena za nkhaniyi. Ikuperekanso malingaliro ogwira ntchito kwa akazi ndi amuna ponena za mmene angadzitetezerere pa kuukiridwa kapena kunenezedwa kukhala wovutitsa akazi kapena amuna. Kodi mungakonde kuŵerenga kopeli la magazini a Galamukani!?”
5 Ngati mungakonde ulaliki wachidule, mungayese izi:
◼ “Ambiri amalingalira kuti magazini ambiri otchuka a masiku ano amasonyeza kwambiri zamalonda, kugonana, kapena chiwawa. [Sonyezani Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!] Tikugaŵira magazini abwino awa amene ali ozikidwa pa Baibulo. Amaphunzitsa zambiri ndipo amatiphunzitsa kulambira Mulungu, kukonda mnzathu, ndi kukhala ndi khalidwe lowongoka. Ngati mumakonda zoŵerenga zamtundu umenewu, ndikudziŵa kuti mudzasangalala ndi zimene mudzapeza m’magazini awa.”
6 Ngati tili achangu pa kulankhula choonadi kwa anzathu, tingabweretse chisangalalo chachikulu kwa ambiri.—Mac. 8:4, 8.