Gwirani Ntchito m’Gawo Lanu Mosamala
1 M’madera a nyumba zokhalamo anthu nthaŵi zina timapeza malo aang’ono a malonda, monga golosale, lesitiranti kapena sitolo wamba. Kuti malo ameneŵa afoledwe pamodzi ndi gawo lonse limeneli, muyenera kufikapo monga momwe mumafikira panyumba.
2 Mungagwiritsire ntchito ulaliki wosavuta ndipo wachidule, mwinamwake mukumanena kuti: “Ndili ndi kanthu kena kamene ndifuna kukusonyezani.” Ngati mwini malo akuoneka kukhala wotanganitsidwa panthaŵiyo, mungangompatsa trakiti ndi kunena kuti: “Ndidzabweranso pamene simudzakhala wotanganitsidwa kwambiri. Ndidzafuna kudziŵa zimene muganiza ponena za izi.”
3 Sitiyenera kuchita mantha ponena za kuchita ntchito imeneyi. Wofalitsa wina anati: “Ndinayembekezera kuti adzakana. Komabe, zinandidabwitsa kuti anamvetsera uthenga wa Ufumu mosiyana kwambiri ndi zimene ndinaganiza. Iwo analidi aulemu ndi aubwenzi ndipo analandira magazini pafupifupi nthaŵi zonse.”
4 Mkazi wina wogwira ntchito pakampani yogulitsa malo anauza Mboni kuloŵa mu ofesi mwake. Analandira magazini nafotokoza kuti anafuna kukhala ndi phunziro la Baibulo. Anamsonyeza buku la Chidziŵitso, ndipo nthaŵi yomweyo phunziro linayambidwa, mu ofesi mwakemo!
5 Ntchito ya kugwira ntchito m’gawo lanu mosamala imaphatikizapo kufikira anthu amene akuchita malonda chapafupi nalo. (Mac. 10:42) Linganizani kufika pamakomo ameneŵa monganso mumafika panyumba. Zimenezi sizidzangokuchititsani kulifola bwino gawo lanu komanso mudzafupidwa ndi zokumana nazo zokondweretsa!