Chitani Umboni Kulikonse Kumene Kuli Anthu
1 Povomereza mbali imene mzimu wa Mulungu unachita mu utumiki wake, mtumwi Paulo anati: “Mulungu anakulitsa.” Anavomerezanso kuti: “Ife ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:5-9) Umenewu ndi mwaŵi wabwino kopambana. Kodi tingasonyeze motani poyera kuti tikuyamikira kukhala antchito anzake a Mulungu? Mwa kubukitsa uthenga wabwino kwa onse amene tikumana nawo pantchito ya kunyumba ndi nyumba ndi kwina kulikonse.
2 Tikulamulidwa ‘kuphunzitsa anthu.’ (Mat. 28:19) Ngati tionana ndi anthu ochepa okha pamene tili mu utumiki, tingalefuke msanga ndi kuona monga palibe zenizeni zimene tapanga. Komabe, utumiki wathu umatisangalatsa zedi ngati tapeza anthu ambiri ndi kulankhula nawo. Zimenezi zingakhale zovuta, popeza zimafuna kuti ifeyo tichitepo nzeru inayake yopita kulikonse kumene anthu ali kuti tionane nawo.
3 Zitsanzo Zothandiza: Tingachitire umboni kwa anthu m’misika, m’mapaki, poima basi, ndi poima zoyendera zina. Pamene muli pazoyendera za onse, kodi mumakhala wokonzeka kuchita umboni paulendowo? Mboni zina ziŵiri paulendo wa pabasi yodzaza pokakumana kuti apite mu utumiki zinali kukambitsirana za chithunzi cha Paradaiso cha m’buku la Chidziŵitso, kukambitsirana malonjezo a Mulungu ponena za mtsogolo. Monga momwe anafunira kuti zichitike, mnyamata wina yemwe anaima pafupi anamvetsera ndipo zimene anamva zinamsangalatsa. Asanatsike m’basimo, analandira buku ndi kupempha kuti wina akamchezere kunyumba kwake.
4 Ofalitsa ambiri asangalala ndi kuchita umboni wamwamwaŵi. Mlongo wina anapita pamasitolo a kwawoko masana ena ndi kufikira anthu amene anali atagula kale zogula zawo koma amene anaoneka kuti sakufulumira. Anagaŵira mabuku onse amene anali nawo m’chola chake. Mwamuna wina amene anali kuyembekezera m’galimoto lake anakondwera kulandira magazini kwa iye. Anali atapezekapo pamisonkhano kumbuyoku, ndipo kukambitsirana kwawo kunadzutsanso chidwi chake.
5 Kukweza dzina la Yehova ndi mwaŵi. Mwa kusonyeza changu chathu pantchito yolalikira, timasonyeza kuti sitinaphonye chifuno cha chisomo cha Mulungu kwa ife. Popeza “tsopano ndiyo nyengo yabwino” yothandiza ena, tiyeni tipite kulikonse kumene kuli anthu ndi kuchita umboni kwa iwo za “tsiku la chipulumutso” la Yehova.—2 Akor. 6:1, 2.