Anansi Athu Afunikira Kumva Uthenga Wabwino
1 Mulungu akufuna kuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) “Anthu onse” akuphatikizapo anansi athu onse. Powafikira ndi uthenga wabwino tifunikira kukhala ndi maluso ambiri pakulalikira kwathu ndipo tiyenera kufuna kudziŵa zimene zingakondweretse aliyense amene timakumana naye. (1 Akor. 9:19-23) Gulu la Yehova lapereka ziŵiya zimene zingatithandize kufika mitima ya “amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.” (Mac. 13:48) Tiyeni tione mmene tingagwiritsirire ntchito mabrosha osiyanasiyana m’July ndi August, kuti tithandize anansi athu pazimene amasoŵa mwauzimu.
2 Mabrosha Omwe Asankhidwa: Pansipa mupezapo malingaliro amene mwina angathandize pogaŵira mabrosha ena ndi ena. Lingaliro lililonse likuphatikizapo (1) funso lochititsa chidwi loyambitsira kukambitsirana, (2) ndime imene mfundo zokambitsirana zingapezeke m’broshalo, ndiponso (3) lemba loyenera limene mungaŵerenge pokambitsiranapo. Mungatsirize ulalikiwo mwa mawu anuanu, malinga ndi mmene munthuyo akuyankhira. Utumiki Wathu Waufumu wa mwezi wina wa mmbuyo wasonyezedwa mmene mungapezemo maulaliki ofotokozedwa bwino a mmene tingagawirire mabrosha ena ochuluka.
Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
Kodi mukuganiza kuti pali chiyembekezo chotani chothandizira anthu amene amachitiridwa nkhanza?—Masamba 27-8, ndime 23-7; Yes. 65:17, 18; km-CN 7/97 tsa. 4.
Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?
Kodi nchifukwa chiyani anthu ambiri lero akuoneka kuti moyo wawo sukuwakondweretsa?—Masamba 29-30, ndime 2, 25-6; Sal. 145:16; km-CN 7/97 tsa. 4.
Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
Kodi mukudziŵa kuti Yesu Kristu akutani pakali pano?—Zithunzi 41-2; Chiv.11:15. km-CN 8/96 tsa. 8.
Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso.
Kodi mungakonde kudziŵa za Ufumu umene Yesu anatiphunzitsa kuti tiziupempherera?—Tsamba 3; Mat. 6:9, 10; km-CN 8/96 tsa. 8.
Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
Kodi munalingalirako za mmene mungatonthozere munthu yemwe wafedwa wokondedwa wake?—Tsamba 26, ndime 2-5; Yoh. 5:28, 29; km-CN 7/97 tsa. 4.
Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?
Kodi tifunikira kudziŵa mmene Mulungu alilidi kuti tikhale ndi tsogolo labwino?—Tsamba 3, ndime 3, 7-8; Yoh. 17:3.
3 Brosha linanso linakonzedwa kuti lithandize anthu amene angakhale ophunzira kwambiri koma amene sadziŵa zambiri za m’Baibulo. Linakonzedwa mwa njira yowasonkhezera kufuna kuŵerenga Mawu a Mulungu. Pamene kuli koyenera, mungasankhe kugaŵira otsatirawa:
Buku la Anthu Onse.
Kodi simungavomereze kuti kuphunzira bwino kumatanthauzanso kudziŵa zimene Baibulo limanena?—Tsamba 3, ndime 1-3 ndi tsamba 30, ndime 2; Mlal. 12:9, 10.
4 Brosha Lochititsira Phunziro la Baibulo: Cholinga chathu mu utumiki chiyenera kukhala chakuyamba phunziro la Baibulo, kaya paulendo woyamba kapena paulendo wobwereza. Kuti tithe kutero, tili ndi brosha lotsatirali, losavuta kugwiritsira ntchito ncholinga chakuyamba maphunziro a Baibulo ndi kuwachititsa:
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Kodi mukudziŵa kuti pamphindi 30 kapena kucheperapo, kwa milungu 16, mungayambe kulimvetsa Baibulo?—Phunziro 2, ndime 6; 2 Tim. 3:16, 17; km-CN 3/97 tsa. 4.
5 Yesu, m’fanizo lake la Msamariya wachifundo, anasonyeza kuti mnansi weniweni ndiye uja amene amasonyeza chikondi ndi chifundo pothandiza wina m’nsautso yake. (Luka 10:27-37) Abale athu ali m’nsautso yauzimu. Afunikira kumva uthenga wabwino. Tiyeni tichite ntchitoyi yowauza, kuti tidzisonyeze kuti ndifedi ophunzira oona a Yesu Kristu.—Mat. 24:14; Agal. 5:14.