Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/99 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kodi Tingathandize Bwanji Kuti Nyumba Yathu ya Ufumu Izioneka Bwino?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 11/99 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi kuyeretsa Nyumba ya Ufumu ndi ntchito ya ndani?

Nyumba ya Ufumu imene ili yaudongo ndi yooneka bwino imalemekeza uthenga umene timalalikira. (Yerekezani ndi 1 Petro 2:12.) N’kofunika kuti Nyumba ya Ufumu izikhala yoyera ndi yaudongo, ndipo aliyense angathandize poisamalira. Sitiyenera kulingalira kuti ntchito yonseyo ndi ya anthu ena ochepa basi. Nthaŵi zambiri, kuyeretsa Nyumba ya Ufumu kumachitika malinga ndi magulu a Phunziro la Buku la Mpingo, ndipo wochititsa phunziro kapena wothandizira wake ndiye amatsogolera ntchitoyi. M’Nyumba za Ufumu zimene zimagwiritsidwa ntchito ndi mipingo ingapo, akulu adzalinganiza nkhaniyi kuti mipingo yonse izisamalira Nyumba ya Ufumuyo.

Kodi tingagwire bwino motani ntchito imeneyi? Nyumba ya Ufumu iyenera kuyeretsedwa malinga ndi ndandanda yanthaŵi zonse. Zida zogwirira ntchito poyeretsa komanso zoyeretserazo ziyenera kukhalapo. Zinthu zofunika kuchitidwa ziyenera kulembedwa n’kukhomedwa pamene anthu ogwira ntchito angamaone kuti adziŵe zoti achite. Pangakhale ndandanda ziŵiri, imodzi ya zimene ziyenera kuchitidwa pa kuyeretsa kwa apo ndi apo pamapeto a msonkhano uliwonse ndi ina ya zochita pa kuyeretsa mwachifatse mlungu uliwonse. Wochititsa phunziro la buku ayenera kuika tsiku ndi nthaŵi yoyeretsa mwachifatse imene ili yabwino kwa onse ogwira ntchitoyo. Kapinga, maluŵa, ndi timitengo ziyeneranso kusamalidwa kaŵirikaŵiri. Njira za anthu oyenda pansi ndi malo oimikapo galimoto ayenera kukhala opanda zinyalala. Chaka chilichonse kuyeretsa malo onse mwachifatse kuyenera kuchitika, mwina Chikumbutso chisanachitike. Izi zingaphatikizepo kutsuka mawindo, makoma, ndi kuyeretsa pansi.

Inde, tonsefe tingapeputse ntchitoyi mwa kupeŵa kutaya chingamu kapena zinyalala zina mkati mwa Nyumba ya Ufumu kapena kunja. Tingakonze chimbudzi nthaŵi iliyonse imene tachigwiritsa ntchito, ndi kuchisiya chili choyera kuti mnzathu achipeze chili bwino. Samalani kuti mupeŵe kuphwanya zinthu kapena kuwononga mipando. Onani mipando yothyoka, mipopi yowonongeka, magolobo akupsa a magetsi, ndi zina zotero, ndipo mwamsanga kaneneni kwa mbale woyang’anira ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu.

Tiyeni tonse tikhale ofunitsitsa kuchita mbali yathu. Izi zimapangitsa nyumba yolambiriramo kukhala yosangalatsa ndipo zimatisiyanitsa monga anthu oyera amene amalemekeza Yehova Mulungu.—1 Pet. 1:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena