Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
Chaka chino Chikumbutso chidzachitika Lachitatu, April 16. Akulu asamalire zinthu izi:
◼ Pokonza nthaŵi ya msonkhano, onetsetsani kuti musapereke zizindikiro dzuŵa lisanaloŵe.
◼ Aliyense, ngakhale wokamba nkhani, auzidwe nthaŵi yeniyeni ndi kumene kudzachitikire mwambowu.
◼ Mupezeretu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17.
◼ Mbale, matambula, thebulo labwino ndi nsalu za pathebulo ziyenera kubwera ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake nthaŵi yabwino.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu ayeretsedweretu bwinobwino.
◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi operekera zizindikiro ndipo muwauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu, ndiponso kuti afunika adzavale zovala zopatsa ulemu ndiponso kudzikonza bwino.
◼ Konzani kukapereka zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense amene akudwala ndipo satha kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kuti anthu asadzapanikizane pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika galimoto. Ngati kuli kotheka ndi bwino kuti pazipita mphindi 45 ena asanayambe mwambowu.