Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda May 15
“Tsiku lililonse timamva malipoti a zachiwawa. Kodi mukuganiza kuti moyo unali wotero kale? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena. [Ŵerengani Mateyu 24:37.] Masiku a Nowa anali oipa kwambiri moti Mulungu anawononga anthu onse koma anasiya Nowa ndi banja lake. Magazini iyi ikufotokoza tanthauzo la zimene zinachitikazo kwa ife masiku ano.”
Galamukani! May 8
“M’dziko losintha mofulumira lino, anthu ambiri amada nkhaŵa kuti mwina ana akukula mofulumira kwambiri. Kodi inunso zimakudetsani nkhaŵa? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Mlaliki 3:1, 4.] Paubwana sinthaŵi yosamalira maudindo amene amasamalira akuluakulu. Galamukani! iyi ikufotokoza mmene makolo angatetezere ubwana wa ana awo.”
Nsanja ya Olonda June 1
“Malipoti onena za kusakaza ndalama zosonkhedwa kuti zithandize ovutika akuchititsa anthu ena kukayikira ngati chili chinthu chanzeru kupereka ndalama ku mabungwe othandiza anthu ovutika. Komabe, pali anthu ambiri ofunika thandizo. Kodi mukuganiza kuti m’pofunika kutani? [Yembekezani ayankhe. Akayankha ŵerengani Ahebri 13:16.] Magazini iyi ikufotokoza za kuthandiza kumene kumakondweretsa Mulungu.”
Galamukani! May 8
Ambirife tikudziŵa wina amene amadwala nthenda ya shuga. Kodi mumadziŵa zambiri za nthenda imeneyi? [Muonetseni chikuto cha magaziniyi, ndipo yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zimayambitsa nthendayi ndiponso mankhwala ake. Ikufotokozanso zimene Baibulo limalonjeza zothetseratu matenda onse.” Malizani ndi kuŵerenga Yesaya 33:24.