Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda June 15
“Anthu ena amaona kuti Yesu anali munthu wamkulu m’mbiri ya anthu. Ena amakayikira zoti anakhalako. Kodi mukuganiza kuti zimene timakhulupirira pankhani ya Yesu zili ndi ntchito? [Akayankha, ŵerengani Machitidwe 4:12.] Kodi pali umboni wanji wosonyeza kuti Yesu anakhalakodi padziko lapansi? Magazini iyi ikuyankha funso limeneli.”
Galamukani! June 8
“Masiku ano, matenda oyamba chifukwa cholumidwa ndi tizilombo ndi amodzi a zinthu zambiri zimene zikuika thanzi lathu pangozi. Kodi mukudziŵa kuti pali zimene tingachite kuti tidziteteze? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene tingachite, komanso lonjezo lopezeka m’Baibulo la nthaŵi imene sipadzakhalanso matenda.” Pomaliza ŵerengani lemba la Yesaya 33:24.
Nsanja ya Olonda July 1
“Chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pamoyo wa munthu ndi kusonyeza chikondi ndiponso kukondedwa. [Ŵerengani mawu a pachithunzi cha patsamba 4.] Komabe, kodi mwaona kuti anthu masiku ano amakonda kwambiri zinthu zina? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kuti chikondi chenicheni n’chiyani ndipo tingakhale nacho bwanji.” Ŵerengani 1 Akorinto 13:2.
Galamukani! June 8
“Zikuoneka kuti masiku ano anthu ambiri amaganiza kuti makhalidwe abwino ndi opanda phindu kusiyana ndi mmene ankaganizira kale. Kodi nanunso mukuona choncho? [Yembekezani ayankhe.] Mochititsa chidwi, Baibulo linalosera izi. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:1-5.] Magazini ya Galamukani! iyi ikufotokoza chifukwa chake makhalidwe a anthu akusintha ndiponso zimene zili m’tsogolo.”