Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda May 15
“Kodi mukuganiza kuti tidzalionadi dziko lopanda umphawi? [Yembekezani ayankhe.] Tamvani zimene Mulungu akulonjeza. [Werengani Yesaya 65:21.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza momwe lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwire.” Konzani zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lakuti: Kodi lonjezo la kusintha kumeneku lidzakwaniritsidwa liti?
Galamukani! June 8
“Anthu ambiri amvapo kuti masewera olimbitsa thupi ndi ofunika kuti munthu akhale ndi thanzi labwino, koma ambiri amati sachita masewerawa mokwanira. Kodi si zoona kuti anthu ambiri sachita masewera olimbitsa thupi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza phindu lochita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse ndiponso njira zina zotithandiza mmene tingachitire zimenezi ngakhale kuti ndife otanganidwa.”
Nsanja ya Olonda June 1
“Ngakhale kuti pafupifupi aliyense amakamba za mtendere, anthu alephera kugwirizana padziko lonse. Kodi mukuganiza kuti zoti anthu padziko lonse angagwirizane ndi nkhambakamwa chabe? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikukamba za boma limene lidzagwirizanitsa anthu padziko lonse.” Werengani Salmo 72:7, 8, ndi kukonza zodzabweranso kuti mudzafotokoze kuti zimenezi zidzachitika bwanji.
Galamukani! June 8
“Kodi mwaona kuti anthu ambiri akuda nkhawa ndi mmene khansa yapakhungu ikuchulukira? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza chifukwa chake ifeyo masiku ano tili pangozi yaikulu yodwala matenda amenewa komanso zimene tingachite kuti tidziteteze.” Pomaliza werengani lonjezo lotonthoza mtima lomwe lili pa Yobu 33:25.