Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
Chaka chino Chikumbutso chidzachitika Lamlungu, pa April 4. Akulu asamalire zinthu izi:
◼ Pokonza nthaŵi ya mwambowu, onetsetsani kuti musapereke zizindikiro dzuŵa lisanaloŵe.
◼ Aliyense, ngakhale wokamba nkhani, auzidwe nthaŵi yeniyeni ndi kumene kudzachitikire mwambowu.
◼ Mupezeretu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2003, masamba 14 ndi 15.
◼ Mbale, matambula, thebulo labwino ndi nsalu za pathebulo ziyenera kubwera ku holo ndi kuziikiratu m’malo ake nthaŵi yabwino.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu ayeretsedweretu bwinobwino.
◼ Muyenera kusankhiratu akalinde ndi operekera zizindikiro ndipo muwauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu, ndiponso kuti afunika adzavale zovala zopatsa ulemu ndiponso kudzikonza bwino.
◼ Konzani kukapereka zizindikirozo kwa wodzozedwa aliyense amene akudwala ndipo satha kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kuti anthu asadzapanikizane pakhonde, pakhomo, m’tinjira, ndi koimika galimoto.