Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
Chikumbutso cha chaka chino chidzachitika Lolemba, pa April 2. Akulu akumbukire zinthu izi.
◼ Pokonza nthawi ya mwambowu, aonetsetse kuti asadzayendetse mkate ndi vinyo dzuwa lisanalowe.
◼ Aliyense, ngakhale wokamba nkhani, auzidwe nthawi yeniyeni ya mwambowu ndiponso kumene udzachitikire.
◼ Apezeretu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2003, mas. 14 ndi 15.
◼ Mbale, matambula, tebulo ndi nsalu za patebulo zoyenerera zibwere ku holo nthawi yabwino n’kuziikiratu pamalo ake.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu akonzedweretu bwinobwino.
◼ Ayenera kusankhiratu akalinde ndi operekera mkate ndi vinyo ndipo awauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu, ndiponso kuti afunika adzavale zovala zaulemu ndiponso kudzikonza bwino.
◼ Akonze zokapereka mkate ndi vinyo kwa wodzozedwa aliyense amene akudwala ndipo satha kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kuti anthu asadzapanikizane pakhomo, m’tinjira, ndi koimika magalimoto.