Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Mar. 15
“Tikufuna kukuitanirani ku mwambo wa Mgonero wa Ambuye Lamlungu, pa April 4. [Fotokozani zimenezi pogwiritsa ntchito chikuto chakumapeto cha magaziniyi kapena timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Ndiyeno ŵerengani Luka 22:19.] Nkhani zoyambirira m’magazini ya Nsanja ya Olonda iyi zikufotokoza tanthauzo la mwambo umenewu ndiponso mmene uyenera kuchitikira.”
Galamukani! Mar. 8
“Anthu ambiri amasangalala kuphunzira za nyama, ndipo ena amakonda kusunga nyama monga zoseŵera nazo. [M’loleni akambepo.] Magazini iyi ikufotokoza mavuto ena osunga nyama monga zoseŵera nazo. Ikufotokozanso za nthaŵi imene Mulungu walonjeza pamene nyama zonse zidzakhala mwamtendere ndipo zidzakhala pamtendere ndi anthu.” Ŵerengani Yesaya 11:6-9.
Nsanja ya Olonda Apr. 1
“Ndi nkhani zochepa chabe m’Baibulo zimene zapatsa anthu maganizo kwambiri ngati mmene yachitira nkhani yovuta kuimvetsa yofotokoza chizindikiro cha chirombo. Kodi munaimvapo nkhani imeneyi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Chivumbulutso 13:16-18.] M’Baibulo momwemo mumapezeka mfundo zimene zingathandize kumvetsa tanthauzo la nkhani yovuta imeneyi. Magazini iyi ikufotokoza mfundozo.”
Galamukani! Mar. 8
“M’mbuyomu, anthu ambiri anali kuopa nkhondo ya zida za nyukiliya. Kodi mukuganiza kuti nkhondo ya zida zimenezi ingakhaleko masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zinthu zodetsa nkhaŵa zimene zikuchitika panopa. Ikufotokozanso zimene Baibulo lalonjeza kuti kudzakhala dziko lopanda mantha.” Ŵerengani Zefaniya 3:13.