Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/04 tsamba 1
  • Kodi Mungathandizeko Ena?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungathandizeko Ena?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ‘Mukufuna’ Kuthandiza Anthu Ena?
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Ganizirani Okalamba Omwe Ali Okhulupirika
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Amenewanso Muziwaganizira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kodi N’chiyani Chimene Chingatithandize Kukhala Ochilimika M’chikhulupiriro?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 11/04 tsamba 1

Kodi Mungathandizeko Ena?

1 Yehova, nthaŵi zonse amafunafuna njira zoti athandizire atumiki ake okhulupirika. (2 Mbiri 16:9; Yes. 41:10, 13) Pomuyerekezera ndi mbusa wabwino, Yesaya analemba kuti: ‘Adzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.’ (Yes. 40:11) Tiyeni tione njira zina zoonetsa mmene tingatsanzirire Yehova pokhala ndi mtima wachikondi ndi woganizira ena.

2 Thandizani Atsopano: Tikhoza kuthandiza ena mwa kuitana atsopano kuti tidzasangalale nawo limodzi pa macheza olimbikitsa. (Miy. 13:20) Pokumbukira mmene ena anam’thandizira pamene anayamba kusonkhana ndi mpingo, mbale wina ananena kuti: “Kwa nthaŵi zambiri banja lina linali kundiphatikiza pa phunziro lawo la banja. Pamene ndinali kupita patsogolo, banja lina la apainiya nthaŵi zambiri linali kundipempha kuti ndipite nawo limodzi mu utumiki kwa tsiku lonse. Nthaŵi zonse tinkakambirana zinthu zauzimu zolimbikitsa kwambiri.” Anawonjezeranso kuti: “Ndisanakhale Mkristu, ndinkakonda kupita kwina kokasangalala kapena kokacheza Lachisanu ndi Loŵeruka usiku. Koma nthaŵi imene ndinali kucheza ndi abale inandithandiza kuti ndisamasoŵe ocheza nawo.” Chikondi chimene anthu mu mpingo anamuonetsa mbaleyu chinamuthandiza kukhala wolimba ndi wosasunthika m’chikhulupiriro, ndipo pano ndi mmodzi mwa amene akutumikira pabanja la Beteli.—Akol. 2:6, 7.

3 Limbikitsanani Wina ndi Mnzake: Pamene abale athu akumana ndi mavuto, m’pofunika kuzindikira kuti umenewo ndi mpata woti tithandize ena. Kodi simungakonze zochita ulaliki wa patelefoni limodzi ndi amene thanzi lake lili lofooka kapena kum’pempha kuti mudzapite naye limodzi ku phunziro la Baibulo, mwina ngakhale kukam’tenga wophunzira wanuyo n’kupita naye kunyumba kwa wokalambayo? Kodi n’kutheka kuti kholo limene lili ndi ana aang’ono lingafune kuti mulithandize pamene likupita mu utumiki? Kodi pali ena amanyazi amene angasangalale kuti mupite nawo limodzi ku maulendo obwereza kapena pamene mukuchita maulaliki a mitundu ina? Chikondi cha pa abale athu chidzatithandiza kuti tipeze njira zowalimbikitsira.—Aroma 14:19.

4 Pamene tikutengera mtima wachifundo umene Yehova alinawo pa atumiki ake, timalimbikitsana wina ndi mnzake, timathandiza mpingo kukhala wokondanadi, ndipo timalemekeza Atate wathu wakumwamba.—Aef. 4:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena