Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira November 8
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Mu November, tidzagaŵira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Longosolani mwachidule zitsanzo za maulaliki amene ali mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2004 pa tsamba 3.
Mph. 15: Pindulani Mokwanira ndi Msonkhano wa Utumiki. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Utumiki Wathu, masamba 71 ndi 72. Ndi mbali zisanu ziti zimene Msonkhano wa Utumiki umatithandiza kuwongolera monga atumiki achikristu? Tchulani mfundo zina za m’pulogalamu ya mwezi uno. Kodi kukonzekera pasadakhale kuli ndi phindu lotani? N’chifukwa chiyani tiyenera kupezekapo nthaŵi zonse? Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Malemba chofanana ndi msonkhano umenewu?
Mph. 20: “Pitirizanibe Kukhala Achangu!” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2000, masamba 12 ndi 13.
Nyimbo Na. 19 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 15
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Ngati mfundo zimene zili patsamba 4 zingathandize m’gawo la mpingo wanu, zigwiritseni ntchito posonyeza chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi Galamukani! ya December 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Kodi Munayamba Mwadalitsidwapo Chifukwa Chopatsa? Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2004, masamba 19 mpaka 23.
Mph. 20: Kodi Tingatani Kuti Tipitirizebe Kukhala Olimba? Nkhani yokhala ndi mbali yofunsa ena mafunso. Isonyeze kufunika kopitirizabe kukhala olimba ndi osatopa. (1) Funsani anthu aŵiri kapena atatu amene atumikira kwa zaka zambiri amenenso ali zitsanzo zabwino. Kodi akumana ndi mavuto otani amene akanawaletsa kulalikira ndipo apirira motani? N’chiyani chawathandiza kupitirizabe osatopa? (Angatchule pemphero, kupezeka pa misonkhano nthaŵi zonse, phunziro laumwini, chilimbikitso chochokera kwa anthu ena, ndi zina zotero.) N’chiyani chimene achita kuti apewe kubwerera m’mbuyo kapena kusiya kumene? (Angatchule kufunika kopezeka pa misonkhano nthaŵi zonse ndi macheza abwino amene amakhalapo, kukhala ndi phunziro laumwini lokhazikika, kuyamikira ubwenzi wawo ndi Mulungu, ndi zina zotero.) Kodi atha bwanji kukhalabe olimba mwauzimu? (Angatchule mmene akulu kapena anthu ena awathandizira, kuika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo, kupemphera kwa Yehova, ndi zina zotero.) (2) Funsani ana ena amene ndi ofalitsa okhazikika amenenso ali zitsanzo zabwino. N’chiyani chawathandiza kuti aziloŵa mu utumiki nthaŵi zonse? Kodi makolo awo awathandiza motani? Kodi ofalitsa ena amalimbikitsa ndi kuthandiza anawo mu utumiki wa kumunda? Kodi ali ndi zolinga zotani zokhudza kutumikira Yehova? Pomaliza bwerezani mwachidule mfundo zimene zatchulidwa mu nkhaniyi.
Nyimbo Na. 66 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 22
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: Kufunika kwa Moyo Wauzimu m’Banja. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2002, tsamba 8, ya mutu wakuti “Kodi Tingatani Kuti Mabanja Athu Akhale Olimba Mwauzimu?” Fotokozaninso kufunika koti banja lizichita lemba la tsiku, mmene lingamachitire zimenezo malinga ndi mmene zinthu zilili pabanjapo ndi ndandanda yawo. Tsindikani kufunika kopempherera pamodzi monga banja ngakhale kamodzi patsiku. Mungachite zimenezi panthaŵi yokagona. Mfundo zomwezi zingagwire ntchito m’mabanja oti mwamuna kapena mkazi si Mboni, mabanja a kholo limodzi, ndi mabanja amene alibe ana. Kukonzekera pamodzi monga banja n’kothandizanso kwambiri kuti muzipindula mokwanira bwino mlungu uliwonse pamisonkhano ya mpingo ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro cha ena.—Aheb. 10:23-25.
Nyimbo Na. 58 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 29
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a November. Sonyezani chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya December 8. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 25: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 3.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Mukamaliza kukambirana ndime yachitatu, sonyezani chitsanzo chachidule cha phunziro la Baibulo kuchokera mu bulosha la Mulungu Amafunanji phunziro 5, ndime 1. Achite ngati kuti ndimeyo yaŵerengedwa ndipo yayankhidwa kale. Wochititsa phunziro ndi wophunzirayo aŵerenge ndi kukambirana Yesaya 45:18 ndi Mlaliki 1:4. Wochititsa phunziroyo agwiritse ntchito mafunso osavuta olimbikitsa wophunzirayo kuti afotokoze mmene lemba lililonselo likugwirizanirana ndi nkhani imene akukambiranayo.
Nyimbo Na. 178 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 6
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Tchulani mabuku ogaŵira mu December. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zimene tikhoza kugwiritsa ntchito pogaŵira buku la Munthu Wamkulu.
Mph. 20: “Kodi Mungathandizeko Ena?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri amene amayamikira chithandizo kapena chilimbikitso chimene ena anawapatsa.
Mph. 15: Mmene Tingayambitsire Maphunziro a Baibulo. Funsani ofalitsa aŵiri kapena atatu amene amatha kuyambitsa maphunziro mosavuta. Kodi n’chiyani chimene achiona kukhala chothandiza? Kodi amatani kuti chidwi chimene apeza koyamba chisazirale? Sonyezani zitsanzo zachidule za mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba ndi pa ulendo wobwereza.
Nyimbo Na. 101 ndi pemphero lomaliza.