Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
Yehova ndi woyenera kulandira ulemerero. Kodi tingam’lemekeze bwanji? Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena amavutika kulemekeza Yehova? Kodi anthu omwe amalemekeza Mulungu amakhala ndi madalitso otani? Pulogalamu ya msonkhano wadera wa chaka chautumiki cha 2008 idzayankha bwino mafunso amenewa. Ndipo mutu wa msonkhano umenewu ndi woti, “Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) Taonani malangizo ochuluka auzimu omwe tidzalandire pa msonkhano wa masiku awiriwu.
Woyang’anira chigawo adzakamba nkhani yakuti, “N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupatsa Mulungu Ulemerero?” ndiponso yakuti, “Khalani Chitsanzo Chabwino Pomvera Mulungu.” Iye adzakambanso nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Ndani Akupatsa Mulungu Ulemerero?” ndi nkhani yomaliza yonena kuti “Kulemekeza Mulungu Mogwirizana Padziko Lonse.” Adzachititsanso Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Woyang’anira dera adzakamba nkhani zakuti “Khalani Osangalala Posonyeza Ulemerero wa Mulungu,” “Kusamalira Zosowa za Dera,” ndiponso yakuti “Khalanibe ‘Okhazikika Molimba M’choonadi,’” yochokera pa 2 Petulo 1:12. Ndiponso tidzamvetsera nkhani yomwe idzasonyeza kuti, “Utumiki Waupainiya Umalemekeza Mulungu.” Padzakhalanso nkhani ziwiri zosiyirana zomwe zidzatilimbikitsa kwambiri. Ndipo imodzi mwa nkhani zimenezi ili ndi mutu wakuti, “Kulemekeza Mulungu M’mbali Zonse za Moyo Wathu.” Nkhani imeneyi idzafotokoza tanthauzo la mawu ouziridwa opezeka pa 1 Akorinto 10:31. Ndiyeno nkhani yosiyirana ya mutu wakuti, “Kuchita Utumiki Wopatulika Ndi Cholinga Chotamanda Yehova” idzafotokoza mbali zosiyanasiyana za kulambira kwathu. Kenako, Lamlungu tidzakhala ndi chidule cha Nsanja ya Olonda ndiponso kukambirana lemba la tsiku. Padzakhalanso mwayi wobatizidwa.
Anthu ambiri savomereza zoti kuli Mulungu. Ambiri amalephera kuganizira za ulemerero wa Yehova chifukwa cha zochita za anthu. (Yoh. 5:44) Koma ndife otsimikiza kuti ndi bwino kukhala ndi nthawi yoganizira mfundo yakuti, “Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu.” Konzekerani kudzapezeka pa zigawo zonse zinayi ndi kupindula mokwanira.