Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso
Akulu akumbukire zinthu izi pokonzekera Chikumbutso:
◼ Aonetsetse kuti mkate ndi vinyo zisadzayendetsedwe dzuwa lisanalowe
◼ Apezeretu mkate ndi vinyo woyenera.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2003, mas. 14 ndi 15.
◼ Mbale, matambula, tebulo ndi nsalu za patebulo zoyenerera zibwere ku holo nthawi yabwino n’kuziikiratu pamalo ake.
◼ Nyumba ya Ufumu kapena malo ena alionse ochitirapo mwambowu akonzedweretu bwinobwino.
◼ Ayenera kusankhiratu akalinde ndi operekera mkate ndi vinyo ndipo awauziretu ntchito yawo ndi mmene adzayendetsere zinthu, ndiponso kuti adzavale modzilemekeza ndi kuzikongoletsa bwino.
◼ Akonze zokapereka mkate ndi vinyo kwa wodzozedwa aliyense amene akudwala ndipo sadzatha kupezekapo.
◼ Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mipingoyo iyenera kugwirizana bwino, kuti anthu asadzapanikizane pakhomo, m’tinjira, ndi koimika magalimoto.
◼ Ngati mukagwiritse ntchito malo ena, onetsetsani kuti kuli zokuzira mawu zabwino kuti aliyense amene wabwera akamve nkhani imene ikukambidwa.