Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda October 1
“Masiku ano anthu ambiri asiya kukhulupirira zoti pali Mlengi. Kodi mukuganiza kuti akuchita zimenezi chifukwa chiyani? [Yembekezani ayankhe. ] Chifukwa china chikupezeka pa mavesi awa. [Werengani Habakuku 1:2, 3.] Nkhani iyi ikuthandizani kuyankha mafunso okhudza Mulungu amene achititsa anthu ena kusiya kum’khulupirira.” Asonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 11.
Galamukani! October
“Kodi n’zoona kuti mabanja akukumana ndi mavuto ambiri masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri samadziwa malangizo othandiza amene ali m’Baibulo. Mwachitsanzo, taonani malangizo awa.” [Werengani lemba lililonse lopezeka m’magaziniyi.] Galamukani! yapadera imeneyi ikusonyeza mmene mfundo za m’Baibulo zingathandizire mabanja kuthetsa mavuto osiyanasiyana.”
Nsanja ya Olonda November 1
“Kodi mukuganiza kuti zonse zimene amaphunzitsa m’matchalitchimu zimachokera m’Baibulo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatichenjeza kuti tikhale osamala ndi ziphunzitso zonama. [Werengani Akolose 2:8.] Magazini iyi ikufotokoza ziphunzitso 6 zosagwirizana ndi Mawu a Mulungu zimene amaphunzitsa m’matchalitchi osiyanasiyana.”
Galamukani! November
“Masiku ano anthu ambiri akugwiritsa ntchito zipangizo zamakono monga mafoni am’manja ndi makompyuta. Kodi mukuganiza kuti kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kumatithandiza kuchita zinthu mwamsanga kapena kumatithera nthawi? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri angagwirizane ndi malangizo awa olimbikitsa kugwiritsa ntchito nthawi mwanzeru. [Werengani Aefeso 5:15, 16.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zimene tingatsatire kuti tizigwiritsa ntchito zipangizo zamakono moyenerera.”