Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda October 1
“Anthu ambiri amakayikira ngati Mulungu amakhudzidwa ndi mavuto komanso nkhawa zimene timakhala nazo. Kodi inuyo nkhaniyi mumaiona motani? [Yembekezani kuti ayankhe. Kenako werengani Salimo 34:18.] Nkhani imene ikuyambira patsamba 19 ikufotokoza mmene Mulungu amatithandizira kulimbana ndi zinthu monga kudziona ngati wosafunika, kukhumudwa kwambiri, ndiponso kudziona ngati wolakwa kwambiri.”
Galamukani! October
“Anthu ena amaona Mulungu ndi mphamvu chabe. Pamene ena amaona kuti Mulungu ndi munthu weniweni ndipo amakhudzidwa ndi zinthu zimene zikuchitika, moti amatha kusangalala kapena kukhumudwa nazo. Kodi inuyo maganizo anu ndi otani? [Yembekezani kuti ayankhe.] Taonani mfundo yochititsa chidwi imene ili palemba ili. [Werengani 1 Petulo 5:6, 7.] Nkhani imene ikuyambira patsamba 29 ikuyankha kuchokera m’Baibulo funso lakuti, Kodi Mulungu ndi mphamvu chabe?”
Nsanja ya Olonda November 1
“Aliyense wa ife amafuna kukhala wokhutira ndi zimene ali nazo. Kodi mukuganiza kuti tiyenera kukhala ndi ndalama kuti tikhale okhutira? [Yembekezani kuti ayankhe.] Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anaphunzira kukhala wokhutira ndi zochepa zimene anali nazo. [Werengani Afilipi 4:11, 12.] Magaziniyi ili ndi mfundo 5 zopezeka m’Baibulo zomwe ndi chinsinsi chothandiza munthu kukhala wokhutira.”
Galamukani! November
“Anthu amene amakhulupirira zoti kulibe Mulungu amaona kuti zinthu zikanakhala bwino pakanakhala kuti kulibe chipembedzo chifukwa choona zinthu zoipa zimene anthu ena amachita m’dzina la Mulungu. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani kuti ayankhe.] Lemba ili likufotokoza chifukwa chimodzi chimene chachititsa chipembedzo chonyenga kuyambitsa mavuto. [Werengani 2 Timoteyo 4:3, 4.] Magazini iyi ikufotokoza zinthu zina zimene zikusonyeza kuti mfundo za anthu amenewa ndi zosamveka.”