Inu Achinyamata, Khalani Ndi Mtima Wofuna Kutumikira Yehova
ZAKA 3,500 zapitazo, mneneri wa Yehova Mose, analamula ansembe ndi akulu a mu Isiraeli kuti: ‘Sonkhanitsani anthu, amuna, akazi ndi ana . . . , kuti amvetsere ndi kuphunzira, pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’chilamulo ichi.’ (Deut. 31:12) Kodi palembali, ndani amene analamulidwa kuti azipezeka pamisonkhano? Likuti amuna, akazi ndi ana. N’zochititsa chidwi kuti ngakhale ana ankafunika kumvetsera, kuphunzira ndiponso kutsatira malamulo a Yehova.
Kodi masiku ano ana nawonso amafunika kukhala nawo pamisonkhano yolambira Yehova? Inde! Anthu onse a Mulungu amasangalala akamaona ana ambirimbiri padziko lonse omwe akutumikira Mulungu. Anawa amatsatira mawu a Paulo akuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:24, 25) N’zosangalatsanso kuti ana ambiri amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi makolo awo. (Mat. 24:14) Komanso chaka chilichonse, ana ambirimbiri amabatizidwa. Izi zikusonyeza kuti iwo amakonda kwambiri Yehova. Akabatizidwa amapeza madalitso chifukwa chokhala ophunzira a Khristu.—Mat. 16:24; Maliko 10:29, 30.
Lemba la Mlaliki 12:1 limati: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” Apatu Yehova akukuitanani inu achinyamata mwachikondi kuti muzimulambira ndi kumutumikira. Ndiye kodi mukufuna kuti mukwanitse kaye zaka zingati kuti mudzayambe kuchita zimenezi? Malemba sanena kuti munthu ayenera kufika zaka mwakuti kuti ayambe kutumikira Yehova. Choncho musamazengereze poganiza kuti mukadali mwana ndipo simungathe kumvera Mulungu ndi kum’tumikira. Kaya muli ndi zaka zingati, lembali likukulimbikitsani kuti muyambe kutumikira Mulungu panopo.
Ambirinu muli ndi makolo amene akukuthandizani kuti muzikonda Yehova. Ngati ndi choncho, ndiye kuti muli ngati mnyamata wina wakalekale dzina lake Timoteyo. Agogo ake a mnyamata ameneyu a Loisi ndiponso amayi ake a Yunike anamuphunzitsa malemba oyera kuyambira ali wakhanda. (2 Tim. 3:14, 15) Tikukhulupirira kuti inunso makolo anu amakuphunzitsani ngati mmene anachitira makolo a Timoteyo. Mwina amakuphunzitsani Baibulo, kupemphera nanu, kupita nanu kumisonkhano ya mpingo ndi kumisonkhano ikuluikulu ya anthu a Mulungu ndiponso kupita nanu kolalikira. Dziwani kuti Yehova anapatsa makolo anu ntchito yofunika kwambiri yokuphunzitsani njira zake. Kodi mumawathokoza kuti amakukondani ndiponso kukufunirani zabwino?—Miy. 23:22.
Komatu mukamakula, Yehova amafuna kuti “muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro,” ngati mmene Timoteyo anachitira. (Aroma 12:2) Mukazindikira chifuniro cha Mulungu, muzichita zinthu mumpingo pofuna kukondweretsa Mulungu osati pofuna kukondweretsa makolo anu ayi. Mukamatumikira Yehova mwakufuna kwanu, iye azisangalala nanu.—Sal. 110:3.