Khalani ndi Mtima Wosangalala Pokonzekera Chikumbutso
1. Kodi tidzakhala ndi mwayi wotani pa nyengo ya Chikumbutso?
1 Chikumbutso chidzachitika Lachiwiri pa March 26. Pa nthawi imeneyi, tidzakhala ndi mwayi wosonyeza kuti tikusangalala ndi njira yotipulumutsira imene Mulungu wapereka. (Yes. 61:10) Ngakhale panopa, chisangalalo chimenechi chikhoza kutilimbikitsa kuyamba kukonzekera bwino mwambowu. N’chifukwa chiyani tikutero?
2. N’chiyani chimatilimbikitsa kukonzekera Chikumbutso?
2 Konzekerani Mwambowu: Mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi wofunika kwambiri koma wosavuta kuuchita. Ngakhale zili choncho, tiyenera kuukonzekera bwino kuti zinthu zina zofunika zisaiwalike. (Miy. 21:5) Mwachitsanzo, tiyenera kusankhiratu nthawi ndiponso malo abwino. Tiyenera kupezeratu mkate ndi vinyo zoyenerera. Malo ake ayenera kukhala okonzedwa bwino ndiponso aukhondo. Komanso m’bale amene wasankhidwa kuti akambe nkhani ayenera kuikonzekera bwino. Nawonso akalinde ndiponso operekera vinyo ndi mkate ayenera kuuzidwa bwinobwino mmene adzachitire zinthu mwadongosolo. Tikukhulupirira kuti mwachita kale zinthu zambiri pokonzekera. Kuyamikira dipo kudzatithandiza kukonzera bwino mwambo wapadera umenewu.—1 Pet. 1:8, 9.
3. Kodi tingakonzekeretse bwanji mitima yathu?
3 Konzekeretsani Mtima Wanu: Tifunika kukonzekeretsanso mtima wathu kuti timvetse bwino kufunika kwa mwambo wa Chikumbutso. (Ezara 7:10) Choncho tiyenera kupeza nthawi yowerenga mavesi amene tapatsidwa pa nyengo ya Chikumbutso. Tiyeneranso kuganizira mozama zimene zinachitika masiku omaliza a moyo wa Yesu padzikoli. Kuganizira mozama mtima wodzipereka umene Yesu anali nawo kudzatithandiza kuti tizimutsanzira.—Agal. 2:20.
4. Kodi ndi ubwino uti wa dipo umene umakusangalatsani kwambiri?
4 Imfa ya Yesu imapereka umboni woti Yehova ndi woyenera kulamulira. Dipo limatimasula ku uchimo ndi imfa. (1 Yoh. 2:2) Limathandizanso kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kuti tidzapeze moyo wosatha. (Akol. 1:21, 22) Dipo limatithandizanso kuti tipitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Yehova ndiponso kuti tikhalebe ophunzira a Khristu. (Mat. 16:24) Choncho sangalalani kwambiri pamene mukukonzekera Chikumbutso komanso pamene mudzapezekapo.