Kodi Mwayamba Kukonzekera Chikumbutso?
Pa Nisani 13, mu 33 C.E., Yesu ankadziwa kuti wangotsala ndi usiku umodzi wokha woti akhale ndi atumwi ake. Ankafunika kuchita Pasika womaliza, kenako n’kuyambitsa mwambo wofunika kwambiri, wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Kuti zonsezi zitheke, ankafunika kukonzekera. Choncho anatumiza Petulo ndi Yohane kuti akakonze zonse zofunika pa mwambowu. (Luka 22:7-13) Kuyambira nthawi imeneyo, chaka chilichonse Akhristu amachita mwambo umenewu, koma amafunika kukonzekera. (Luka 22:19) Kodi tingakonzekere bwanji mwambo wa Chikumbutso wachaka chino, womwe udzachitike pa 3 April?
Zimene Ofalitsa Angachite
Konzani zoti mudzagwire nawo mwakhama ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso.
Lembani mayina a ophunzira Baibulo, achibale, anzanu akusukulu, akuntchito komanso anthu ena omwe mukufuna kudzawaitanira ku Chikumbutso.
Werengani malemba a pa nthawi ya Chikumbutso ndi kuwaganizira mozama.
Mudzafike mofulumira kuti mudzalandire alendo obwera ku mwambowu.