Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa May
“Chinthu chimodzi chimene anthufe timafanana ndi chakuti tonse timalakwitsa zinthu nthawi zina. Koma kodi munadzifunsapo ngati Mulungu angathe kutikhululukira ngati titachita tchimo linalake lalikulu?” [Yembekezani ayankhe.] Musonyezeni nkhani imene ili patsamba 15 mu Nsanja ya Olonda ya May 1, ndipo kambiranani funso loyambirira komanso lemba limodzi limene likupezeka pa ndime zimenezi. Mugawireni magaziniyo ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda May 1
“Tikufuna kumva maganizo anu pa zimene lemba ili likunena. [Werengani 1 Yohane 4:8.] Anthu ambiri amagwirizana ndi mawu amenewa, koma anthu ena amaganiza kuti Mulungu ndi wankhanza chifukwa ndi amene amachititsa kuti pakhale masoka achilengedwe, kapena kulola kuti masoka achilengedwe azichitika. Inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Magazini imeneyi ikufotokoza zifukwa zomveka bwino zotithandiza kuti tisamamuone Mulungu ngati wankhanza.”
Galamukani! May
“Tikulankhula ndi anthu za vuto la umbava ndi kugwiririra limene likusowetsa mtendere anthu ambiri. Anthu ena amaganiza kuti vutoli lingathe ngati apolisi atachuluka. Inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Kodi mukudziwa kuti Baibulo limalonjeza kuti vutoli lidzatha? [Werengani Salimo 37:10, 11.] Magazini iyi ikufotokoza za kutha kwa umbava ndi kugwiririra ndiponso zimene tingachite kuti tizidziteteza kwa anthu ochita zimenezi.”