Tizinyamuka Tikangomaliza
Pa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda, timakumana ndi abale ndi alongo athu ndipo n’zosadabwitsa kuti timafuna kucheza nawo. Koma msonkhanowu ukangotha m’malo moyamba kucheza, tiyenera kunyamuka nthawi yomweyo n’kupita mu utumiki. Zili choncho chifukwa ntchito yathu ndi yofunika kuigwira mwamsanga. (2 Tim. 4:2) Ndi bwino kunyamuka nthawi yomweyo, kuti tisawononge nthawi yomwe tikanakhala tikulalikira. Timakhala ndi nthawi yambiri yokambirana zolimbikitsa ndi munthu amene tayenda naye, tikamachoka panyumba ina kupita panyumba ina. Tikamanyamuka msonkhano wokonzekera utumiki utangotha, zimasonyeza kuti timafunitsitsa kutumikira Yehova ndi Yesu mwakhama komanso monga akapolo.—Aroma 12:11.