Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 October tsamba 1
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • GALAMUKANI!
  • KUPHUNZITSA CHOONADI
  • KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KUMISONKHANO (inv)
  • LEMBANI ULALIKI WANUWANU
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 October tsamba 1
A Mboni za Yehova akupatsa munthu kapepala koitanira anthu kumisonkhano

Akuitanira anthu kumisonkhano

Zitsanzo za Ulaliki

GALAMUKANI!

Galamukani! Na. 5 2016 | Kodi Nkhani Yonena za Yesu Ndi Yongopeka?

Funso: Anthu ena amakayikira zoti nkhani yonena za Yesu ndi yoona, pomwe ena sakayikira n’komwe. Koma pali ena amene amanena kuti n’zosatheka kudziwa kuti zoona ndi ziti. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Perekani magaziniyo: Galamukani! iyi ikufotokoza mfundo zomwe zingatithandize kudziwa zoona zake.

KUPHUNZITSA CHOONADI

Baibulo lotsegula

Funso: Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

Lemba: Yoh. 11:11-14

Zoona Zake: Munthu akamwalira, moyo wake umathera pomwepo. Choncho sitiyenera kuopa kuti pali zinazake zomwe zidzatichitikire tikadzafa. Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Mofanana ndi zimene anachita ndi Lazaro, Yesu adzaukitsa anthu amene anamwalira kuti adzakhalenso ndi moyo padzikoli.—Yobu 14:14.

KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KUMISONKHANO (inv)

Kapepala Koitanira Anthu Kumisonkhano

Perekani kapepalako: Ndikufuna kukuitanani kuti mudzamvetsere nkhani yochokera m’Baibulo. Idzakambidwa ku Nyumba ya Ufumu, kapena kuti malo athu olambirira. [Perekani kapepalako ndipo musonyezeni nthawi komanso malo a misonkhanoyo. Muuzeninso mutu wa nkhani ya mlungu umenewo.]

Funso: Kodi munayamba mwapitapo ku Nyumba ya Ufumu? [Ngati n’zotheka muonetseni vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?]

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena