CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 17-18
Muzitsanzira Mtumwi Paulo pa Nkhani Yolalikira Komanso Kuphunzitsa
Kodi tingatsanzire bwanji Paulo?
Tizigwiritsa ntchito Malemba tikamakambirana ndi anthu komanso kumasintha ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi anthu amene takumana nawo
Tizilalikira kumalo komanso pa nthawi imene tingakumane ndi anthu ambiri
Tizichita zinthu mwaluso poyesetsa kudziwa zimene anthu amakhulupirira n’kugwiritsa ntchito zimenezo poyamba kukambirana nawo