MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Tingaphunzire Chiyani Kuchokera mu Nyimbo za Broadcasting?
Kodi pa nyimbo zomwe zimatuluka pa JW Broadcasting, ndi nyimbo iti imene mumaikonda kwambiri, nanga n’chifukwa chiyani? Kodi mumaona kuti zimene zimasonyezedwa m’mavidiyo a nyimbozi ndi zofanana ndi zimene zimakuchitikirani? Aliyense akhoza kusangalala ndi nyimbozi chifukwa zili ndi mitu yosiyanasiyana komanso zimaimbidwa m’zamba zambiri. Komabe sikuti nyimbozi komanso mavidiyo ake zimakonzedwa n’cholinga choti zizingotisangalatsa basi.
Nyimbo iliyonse ili ndi mfundo zothandiza zimene tingazigwiritse ntchito pa moyo wathu komanso mu utumiki. Nyimbo zina zimanena za kuchereza alendo, mgwirizano, mabwenzi, kulimba mtima, chikondi komanso chikhulupiriro. Zinanso zimakhala ndi uthenga wothandiza munthu kubwerera kwa Yehova, kukhululukira ena, kukhalabe okhulupirika kwa Yehova komanso kukhala ndi zolinga zauzimu. Palinso nyimbo ina yomwe imatithandiza kuona kufunika kogwiritsa ntchito bwino mafoni athu. Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza m’nyimbo zathu?
ONERANI VIDIYO YA NYIMBO YAKUTI DZIKO LATSOPANO LILI PAFUPI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi m’vidiyoyi, m’bale ndi mlongo wachikulireyu akuganizira za madalitso ati a m’tsogolo?—Gen. 12:3
Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu choti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake?
Kodi tikuyembekezera chiyani m’tsogolomu?
Kodi zimene tikuyembekezera kutsogoloku zimatithandiza bwanji kupirira mavuto amene tikukumana nawo?—Aroma 8:25