CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 21-22
Muzisonyeza Kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonera
Yehova amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali. Kodi tingasonyeze bwanji kuti nafenso timaona moyo mofananamo?
Tizikonda komanso kulemekeza kwambiri anthu ena.—Mt 22:39; 1Yo 3:15
Tizionetsa kuti tili ndi chikondi choterocho pochita khama kwambiri mu utumiki.—1Ak 9:22, 23; 2Pe 3:9
Nthawi zonse tiziganizira zimene tingachite kuti tipewe ngozi.—Miy 22:3
Kodi kuona kuti moyo ndi wamtengo wapatali kumatithandiza bwanji kuti tisakhale ndi mlandu wamagazi?