CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Solomo Anapemphera Modzichepetsa Komanso Mochokera Pansi pa Mtima
Pa mwambo wotsegulira kachisi Solomo anapereka pemphero lochokera pansi pa mtima pamaso pa anthu (1Mf 8:22; w09 11/15 9 ¶9-10)
Solomo anatamanda Yehova ndipo sanadzilemekeze yekha (1Mf 8:23, 24)
Solomo anapemphera modzichepetsa (1Mf 8:27; w99 1/15 17 ¶7-8)
Solomo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri makamaka kwa anthu amene amapemphera m’malo mwa anthu ena pagulu. Tiziganizira kwambiri mmene Yehova akumvera pempherolo osati zimene anthu akumva.