Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 May tsamba 5
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Mavuto Azachuma?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Mavuto Azachuma?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana Ndi Zachiwawa?
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 May tsamba 5

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Mavuto Azachuma?

Sitimadabwa kuona zochitika za padzikoli zikuchititsa kuti pakhale mavuto azachuma padziko lonse. N’chifukwa chiyani? Chifukwa tikukhala kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiriza, ndipo Baibulo linatichenjezeratu kuti tisamadalire “chuma chosadalirika.” (1Ti 6:17; 2Ti 3:1) Kodi tingaphunzire chiyani kwa Mfumu Yehosafati pa nkhani ya kukonzekera kukumana ndi mavuto azachuma?

Ataopsezedwa ndi mitundu yodana nawo, Yehosafati anadalira Yehova. (2Mb 20:9-12) Mwamsanga, iye anachitanso zonse zofunika pokonzekera. Anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba, komanso anamanga mizinda ya asilikali. (2Mb 17:1, 2, 12, 13) Mofanana ndi Yehosafati, timafunika kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndipo tizichita zonse zomwe tingathe pokonzekera kukumana ndi mavuto.

KODI MUNGAKONZEKERE BWANJI KUKUMANA NDI MAVUTO AZACHUMA?

Muzikonzekera mwauzimu: Muzikhala okhutira ndipo muzilimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti Yehova adzakupatsani zinthu zofunika pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku. (Mt 6:26; 1Ti 6:8) Muzikhala otsimikiza mtima kuti musanyalanyaze mfundo za m’Baibulo n’cholinga chakuti mupeze zofunika pa moyo. (Aro 2:21) Muzikonzekereratu mmene mungapezere chakudya chauzimu ngati magetsi kapena intaneti zitavuta. Muzikhala ndi mabuku kapena magazini ena ochita kusindikizidwa ndipo ngati n’kotheka, muzipangiratu dawunilodi mabuku a pazipangizo zamakono.

Muzikonzekera mwakuthupi: Muzipewa ngongole komanso musamagule zinthu zosafunika nthawi imene zinthu zilibwino. (Miy 22:7) Ngati n’kotheka, muzisungiratu chakudya chokwanira komanso zinthu zina zofunika. Ena angalime dimba la masamba n’cholinga chakuti asamawononge ndalama.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKA KUKUMANA NDI NGOZI ZOGWA MWADZIDZIDZI?, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi?” Tizithunzi tosonyeza Baibulo, chikwama cha pangozi ndi foni komanso anthu ogwira ntchito yazomangamanga.
  • Kodi tingakonzekere bwanji ngozi zadzidzidzi?

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi?” Abale akugwira ntchito yopereka thandizo lomanga nyumba komanso ena akutsitsa katundu mu galimoto.
  • Kodi tingakonzekere bwanji kuthandiza ena?

CHOLINGA

Pa kulambira kwanu kwa pabanja, kambiranani Galamukani! Na. 1 2022. Mukambirane mfundo zina zokhudza zimene mungachite kuti mukonzekere ngozi zadzidzidzi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena