MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kulimbikitsa Anthu Omwe Amatumikira pa Beteli
Aliyense amakumana ndi mavuto ndipo amafunika kutonthozedwa komanso kuthandizidwa. Ngakhale amene ndi olimba mwauzimu kapena amene ali ndi mwayi wapadera wautumiki, nawonso akhoza kufooka. (Yob 3:1-3; Sl 34:19) Kodi tingaphunzire chiyani pa dongosolo lolimbikitsa anthu amene amatumikira pa Beteli?
ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘TIZIDALIRA MULUNGU,’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi anthu a m’banja la Beteli amakumana ndi mavuto otani?
Kodi abale amachita zinthu 4 ziti kuti alimbikitse atumiki a pa Beteli?
Kodi abale amene amalimbikitsa atumiki a pa Beteli amapindula bwanji?