MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Makolo, Muziphunzitsa Ana Anu Kudziwa Mmene Angasangalatsire Mulungu
Yehova amaona kuti ana ndi amtengo wapatali. Iye amawaona akamakula mwauzimu komanso akamapirira. (1Sa 2:26; Lu 2:52) Ngakhale atakhala ang’ono, akhoza kumasangalatsa Yehova ngati ali ndi makhalidwe abwino. (Miy 27:11) Kudzera m’gulu lake, Yehova wapereka zinthu zabwino kwambiri zothandiza makolo kuphunzitsa ana awo kuti azimukonda komanso kumumvera.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ANANU, YEHOVA AMASANGALALA MUKAMAPIRIRA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Yehova wakhala akuthandiza komanso kutsogolera bwanji achinyamata kwa zaka zambiri?
Kodi pali zinthu ziti zomwe zingathandize makolo?
Ngati ndinu wachinyamata, kodi Yehova wakupatsani zinthu ziti zomwe zakuthandizani, nanga n’chifukwa chiyani?