11 Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ndidzaswa anthu awa ndi mzinda uwu ngati mmene munthu amaswera botolo lopangidwa ndi woumba mbiya moti sangathe kulikonzanso.+ Ndipo adzaika maliro ku Tofeti+ mpaka sipadzapezekanso malo oika maliro kumeneko.”’+