Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.

  • Salimo 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+

      Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+

  • Yesaya 30:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Munthu adzaugwetsa ngati mmene amaphwanyira mtsuko waukulu wadothi,+ mtsukowo n’kuphwanyikiratu wonse n’kungokhala tizidutswatizidutswa, ndipo patizidutswapo osapezeka ngakhale phale loti n’kupalira moto kapena kutungira madzi padambo.”+

  • Maliro 4:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Ana okondedwa a Ziyoni+ amene anali amtengo wapatali ngati golide woyengeka bwino,

      Tsopano ayamba kuonedwa ngati mitsuko ikuluikulu yadothi, ntchito ya manja a munthu woumba mbiya.+

  • Chivumbulutso 2:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo,+ ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena