Yoswa
16 Gawo limene ana a Yosefe+ anapatsidwa+ linayambira kumtsinje wa Yorodano kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi akumʼmawa kwa Yeriko, kudutsa kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+ 2 Kuchokera ku Beteli wa ku Luzi, malire ake anakadutsa kumalire a Aareki ku Ataroti. 3 Kenako anatsetserekera kumadzulo kumalire a Ayafeleti, mpaka kukafika kumalire a Beti-horoni Wakumunsi+ kupita ku Gezeri,+ nʼkukathera kunyanja.
4 Choncho mbadwa za Yosefe,+ omwe ndi Manase ndi Efuraimu, analandira gawo lawo.+ 5 Malire akumʼmawa a gawo la ana a Efuraimu motsatira mabanja awo anali awa: Kuchokera ku Ataroti-adara+ mpaka kukafika ku Beti-horoni Wakumtunda+ 6 nʼkukathera kunyanja. Kumpoto kwake kunali Mikametatu,+ ndipo malirewo anazungulira chakumʼmawa kukafika ku Taanatu-silo, nʼkupitirirabe chakumʼmawa mpaka ku Yanoa. 7 Ndiyeno anatsetsereka kuchokera ku Yanoa kukafika ku Ataroti ndi ku Naara mpaka ku Yeriko,+ nʼkupitirirabe mpaka ku Yorodano. 8 Kuchokera ku Tapuwa,+ malirewo analowera chakumadzulo kuchigwa cha Kana nʼkukathera kunyanja.+ Chimenechi ndi cholowa cha fuko la Efuraimu motsatira mabanja awo. 9 Cholowa cha ana a Efuraimu chinaphatikizapo mizinda imene inali mkati mwa cholowa cha Manase,+ mizinda yonse ndi midzi yake.
10 Koma Aefuraimu sanathamangitse Akanani amene ankakhala ku Gezeri.+ Choncho Akananiwo akukhalabe pakati pa Aefuraimu mpaka lero,+ ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo.+