-
‘Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri’Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 4
‘Yehova Ali Ndi Mphamvu Zambiri’
1, 2. (a) Kodi ndi zinthu zodabwitsa ziti zimene Eliya anali ataonapo kale? (b) Ndi zinthu zodabwitsa kwambiri ziti zimene anaona ali kuphanga m’phiri la Horebe?
ELIYA anali ataonapo kale zinthu zodabwitsa. Anali ataona akhwangwala akumubweretsera chakudya kawiri pa tsiku pa nthawi imene ankabisala. Pa nthawi ya njala yomwe inachitika kwa nthawi yaitali, iye anaona kuti ufa komanso mafuta zomwe zinali m’mitsuko iwiri sizinathe. Analinso ataona moto ukugwa kuchokera kumwamba poyankha pemphero lake. (1 Mafumu, chaputala 17 ndi 18) Koma Eliya anali asanaonepo zinthu zodabwitsa ngati zimene anali atatsala pang’ono kuona pa nthawiyi.
2 Ataima mwamantha pafupi ndi khomo la phanga paphiri la Horebe, anaona zinthu zingapo zodabwitsa kwambiri. Choyamba kunawomba mphepo. Iyenera kuti inali yamphamvu kwambiri chifukwa panali chiphokoso chogonthetsa m’khutu, moti inang’amba mapiri ndi kuphwanya matanthwe. Kenako panachitika chivomerezi champhamvu kwambiri. Ndiyeno panabwera moto. Pamene motowu unkayandikira pamene Eliya anaima, ayenera kuti anamva kutentha kwake koopsa.—1 Mafumu 19:8-12.
3. Kodi Eliya anaona umboni wakuti Mulungu ali ndi khalidwe liti, nanga ifeyo tingapeze kuti umboni woti Mulungu ali ndi khalidweli?
3 Zinthu zonse zimene Eliya anaonazi zinkafanana pa chinthu chimodzi. Zonsezi zinkasonyeza kuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zambiri. Koma sikuti timafunika kuchita kuona zinthu zodabwitsa kuti tidziwe kuti Mulungu ndi wamphamvu. Timatha kuona mphamvu zake mosavuta. Baibulo limatiuza kuti chilengedwe chimapereka umboni wa ‘mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake.’ (Aroma 1:20) Taganizirani za kuwala koopsa kwa mphezi, kugunda kwamphamvu kwa mabingu, mathithi osangalatsa komanso kuchuluka kwa nyenyezi kumwamba. Kodi simuona umboni wakuti Mulungu ali ndi mphamvu zambiri? Komatu ndi anthu ochepa masiku ano amene amazindikira mphamvu za Mulungu ndipo ndi ochepa kwambiri amene amaona mphamvuzo moyenera. Komabe kumvetsa mfundo yoti Yehova ndi wamphamvu kumatithandiza kuti tikhale ndi zifukwa zambiri zoti tizifuna kuti akhale mnzathu. M’chigawochi tiphunzira mwatsatanetsatane mphamvu zopanda malire za Yehova.
“Yehova anadutsa”
Mphamvu Zimachokera kwa Yehova
4, 5. (a) Kodi Baibulo limafotokoza zotani zokhudza dzina la Yehova? (b) N’chifukwa chiyani n’zoyenera kuti Yehova anasankha ng’ombe kuti iziimira mphamvu zake?
4 Palibe amene ali ndi mphamvu zambiri kuposa Yehova. Lemba la Yeremiya 10:6 limati: “Palibe aliyense amene angafanane ndi inu Yehova. Inu ndinu wamkulu ndipo dzina lanu ndi lalikulu komanso lamphamvu.” Monga taonera, lembali likunena kuti dzina la Yehova ndi lalikulu komanso lamphamvu. Paja dzinali limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azitha kupanga chilichonse chimene akufuna ndiponso kukhala chilichonse chimene wasankha? Chifukwa chimodzi n’choti ali ndi mphamvu. Yehova angathe kuchita chilichonse ndipo palibe chimene chingamulepheretse kuchita zimene akufuna. Mphamvu zoterezi ndi limodzi mwa makhalidwe ake ofunika kwambiri.
5 Popeza sitingamvetse zonse zokhudza mphamvu za Yehova, iye amagwiritsa ntchito mafanizo potithandiza kuti timvetse. Monga taonera, amanena kuti ng’ombe imaimira mphamvu zake. (Ezekieli 1:4-10) Pamenepa anasankha nyama yoyenera chifukwa ng’ombe, ngakhalenso zoweta, ndi nyama zikuluzikulu komanso zamphamvu. Kale anthu amene ankakhala ku Palestina nthawi zambiri sankaona nyama zina zamphamvu kuposa ng’ombe. Koma ankadziwa ng’ombe zinazake zoopsa kwambiri zam’tchire zotchedwa aurochs, zimene panopa zinatha. (Yobu 39:9-12) Juliasi Kaisara, yemwe anali mfumu ya Roma, ananena kuti ng’ombe zimenezi kukula kwake sizinkasiyana kwenikweni ndi njovu. Iye analemba kuti: “N’gombezi ndi zamphamvu komanso zimathamanga kwambiri.” Mutaima pafupi ndi nyama imeneyi mukhozatu kudziona kuti ndinu kamunthu kakang’ono komanso kopanda mphamvu.
6. N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene amatchedwa kuti “Wamphamvuyonse”?
6 Mofanana ndi zimenezi, munthu ndi wamng’ono kwambiri komanso wopanda mphamvu tikamuyerekezera ndi Yehova yemwe ndi Mulungu wa mphamvu. Kwa iye, ngakhale mitundu yamphamvu ya anthu ili ngati fumbi pasikelo. (Yesaya 40:15) Mosiyana ndi cholengedwa chilichonse, Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, chifukwa iye yekha ndi amene amatchedwa kuti “Wamphamvuyonse.”a (Chivumbulutso 15:3) Yehova ali ndi ‘mphamvu zoopsa komanso ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu.’ (Yesaya 40:26) Kwa iye kumachokera mphamvu zambiri ndipo sizichepa kapena kutha. Sadalira aliyense kuti amupatse mphamvu, chifukwa “mphamvu ndi za Mulungu.” (Salimo 62:11) Koma kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake?
Mmene Yehova Amagwiritsira Ntchito Mphamvu Zake
7. Kodi mzimu woyera wa Yehova n’chiyani, nanga mawu a zilankhulo zoyambirira omwe anawagwiritsa ntchito m’Baibulo amanena za chiyani?
7 Mphamvu ya mzimu woyera imene imachokera kwa Yehova ndi yopanda malire. Mzimuwu ndi mphamvu ya Mulungu imene imagwira ntchito. Ndipotu pa Genesis 1:2, Baibulo limautchula kuti “mphamvu ya Mulungu.” Mawu a Chiheberi ndi a Chigiriki amene anawamasulira kuti “mzimu” m’mavesi ena anawamasulira kuti “mphepo,” “mpweya” ndiponso “nthunzi.” Mogwirizana ndi zimene akatswiri a Baibulo ananena, mawu a zilankhulo zoyambirirawa amanena za mphamvu yosaoneka yomwe ikugwira ntchito. Mofanana ndi mphepo, mzimu wa Mulungu sitingauone ndi maso, koma zinthu zimene umachita tingathe kuzizindikira.
8. M’Baibulo, kodi mzimu wa Mulungu umatchedwa kuti chiyani mophiphiritsa, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenera?
8 Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera m’njira zosiyanasiyana kuti achite chilichonse chimene akufuna. Choncho m’pake kuti m’Baibulo mzimu wa Mulungu umatchulidwa mophiphiritsa kuti “chala” chake, ‘dzanja lake lamphamvu’ kapenanso ‘mkono wake wotambasula.’ (Luka 11:20; Deuteronomo 5:15; Salimo 8:3) Munthu amagwiritsa ntchito manja ake pochita zinthu zosiyanasiyana zofuna mphamvu kapenanso luso. Mofanana ndi zimenezi Mulungu nayenso amagwiritsa ntchito mzimu wake kukwaniritsa cholinga chake chilichonse. Mwachitsanzo, anagwiritsa ntchito mzimuwo kulenga maatomu omwe ndi aang’ono kwambiri, kugawa madzi pa Nyanja Yofiira komanso kuchititsa Akhristu oyambirira kuti alankhule zilankhulo zina.
9. Fotokozani njira ina imene Yehova amasonyezera mphamvu zake.
9 Yehova amasonyezanso mphamvu zake pogwiritsa ntchito udindo wake monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Taganizirani mfundo iyi: Iye amalamulira angelo mamiliyoni ambirimbiri omwe amakhala ofunitsitsa kuchita zimene wanena. Palinso anthu omwe ndi atumiki ake ndipo m’Malemba nthawi zambiri amawatchula kuti ndi gulu lalikulu. (Salimo 68:11; 110:3) Komabe anthu ndi ochepa mphamvu poyerekezera ndi angelo. Mwachitsanzo, pamene gulu la nkhondo la Asuri linaukira anthu a Mulungu, mngelo mmodzi yekha anapha asilikali a Asuri 185,000 usiku umodzi wokha. (2 Mafumu 19:35) Angelo a Mulungu ndi “amphamvu” kwambiri.—Salimo 103:19, 20.
10. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu Wamphamvuyonse amatchedwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba? (b) Pa zinthu zonse zomwe Yehova analenga, kodi ndi ndani amene ndi wamphamvu kwambiri?
10 Kodi angelo alipo angati? M’masomphenya akumwamba, mneneri Danieli anaona angelo oposa 100 miliyoni ataimirira kumpando wachifumu wa Yehova, koma palibe umboni wosonyeza kuti iye anaona angelo onse. (Danieli 7:10) Choncho n’kutheka kuti angelo alipo mamiliyoni mahandiredi mahandiredi. N’chifukwa chake Mulungu amatchedwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Dzina la udindo limeneli limatithandiza kumvetsa kuti iye ndi Mtsogoleri wa gulu lalikulu la angelo komanso lochita zinthu mwadongosolo. Iye anaika Mwana wake wokondedwa, “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” kuti aziyang’anira angelo onsewa. (Akolose 1:15) Pokhala mkulu wa angelo, yemwe amayang’anira angelo, aserafi ndi akerubi onse, Yesu ndi wamphamvu kwambiri kuposa zinthu zonse zimene Yehova analenga.
11, 12. (a) Kodi mawu a Mulungu amasonyeza kuti ndi amphamvu m’njira zotani? (b) Kodi Yesu ananena chiyani zokhudza mphamvu za Yehova?
11 Pali njira inanso imene Yehova amasonyezera mphamvu zake. Lemba la Aheberi 4:12 limati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu.” Kodi inuyo mwaonapo umboni wosonyeza kuti mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga wouziridwa ndi mzimu umene uli m’Baibulo, ndi amphamvu? Mawuwa angatilimbikitse ndiponso angatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kusintha kwambiri moyo wathu. Mtumwi Paulo anachenjeza okhulupirira anzake zokhudza anthu a makhalidwe oipa kwambiri. Kenako anawonjezera kuti: “Ndipo ena a inu munali otero.” (1 Akorinto 6:9-11) Inde, “mawu a Mulungu” anasonyeza kuti ndi amphamvu ndipo anathandiza anthuwo kuti asinthe.
12 Mphamvu za Yehova n’zambiri ndiponso amazigwiritsa ntchito m’njira yabwino kwambiri moti palibe chilichonse chimene chingamulepheretse kuzigwiritsa ntchito. Yesu ananena kuti: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Mateyu 19:26) Koma kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pa zolinga ziti?
Mulungu Amagwiritsa Ntchito Mphamvu Zake ndi Cholinga
13, 14. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti sikuti Yehova wangokhala malo enaake kumene kumachokera mphamvu? (b) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira ziti?
13 Mzimu wa Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa mphamvu ina iliyonse. Sikuti Yehova wangokhala malo enaake kumene kumachokera mphamvu, koma ndi Mulungu amene amaganiza ndipo amasangalala kapenanso kukhumudwa ndi zinthu. Komanso iye amatha kulamulira bwinobwino mphamvu zake. Koma kodi n’chiyani chimamuchititsa kuti azigwiritsa ntchito mphamvu zakezo?
14 Monga mmene tionere, Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake polenga, powononga, poteteza komanso pobwezeretsa zinthu. Mwachidule tingoti pochita chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse zolinga zake. (Yesaya 46:10) Pa zochitika zina, Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kutiphunzitsa zinthu zofunika zokhudza iyeyo komanso mfundo zake. Chofunika kwambiri n’chakuti iye amagwiritsa ntchito mphamvu zake pofuna kukwaniritsa chifuniro chake, chomwe ndi kuyeretsa dzina lake pogwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya. Zimenezi zimasonyeza kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Ndipotu palibe chimene chingalepheretse cholinga chakechi.
15. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake pothandiza atumiki ake, nanga anasonyeza bwanji zimenezi kwa Eliya?
15 Yehova amagwiritsanso ntchito mphamvu zake potithandiza aliyense payekha. Taonani zimene lemba la 2 Mbiri 16:9 limanena: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.” Chitsanzo cha zimenezi ndi zomwe zinachitikira Eliya, zimene zatchulidwa koyambirira kwa mutuwu. N’chifukwa chiyani Yehova anamuonetsa mphamvu zake mochititsa mantha choncho? Yezebeli yemwe anali mfumukazi yoipa anali atalumbira kuti apha Eliya. Mneneriyu ankathawa pofuna kupulumutsa moyo wake. Iye ankaona kuti ali yekhayekha, ankachita mantha komanso ankaganiza kuti ntchito yaikulu yomwe anagwira siinaphule kanthu. Kuti alimbikitse Eliya, yemwe anali ndi nkhawa, Yehova anamukumbutsa kuti iye ndi wamphamvu kwambiri. Mphepo, chivomerezi ndiponso moto zinasonyeza kuti Mulungu yemwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse anali naye. Panalibe chifukwa choti aziopera Yezebeli popeza Mulungu wamphamvuyonse anali kumbali yake.—1 Mafumu 19:1-12.b
16. N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kuganizira mozama mphamvu za Yehova zomwe ndi zambiri?
16 Ngakhale kuti masiku ano Yehova sachita zodabwitsa, kuchokera mu nthawi ya Eliya mpaka pano iye sanasinthe. (1 Akorinto 13:8) Amafunitsitsabe kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuti athandize anthu amene amamukonda. N’zoona kuti iye amakhala kumwamba, koma sikuti ali nafe kutali. Mphamvu zake n’zopanda malire choncho zikhoza kufika kulikonse. Ndipotu “Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana.” (Salimo 145:18) Pamene mneneri Danieli ankapempha Yehova kuti amuthandize, mngelo anafika kwa iye asanamalize n’komwe kupemphera. (Danieli 9:20-23) Palibe chomwe chingalepheretse Yehova kuti athandize komanso kulimbikitsa anthu amene amawakonda.—Salimo 118:6.
Kodi Tizichita Mantha Kuyandikira Mulungu Chifukwa Ndi Wamphamvu?
17. Kodi mphamvu za Yehova zimatithandiza kuti tizimuopa mwanjira iti, nanga sitiyenera kukhala ndi mantha ati?
17 Kodi tiyenera kumaopa Mulungu chifukwa choti ali ndi mphamvu? Tingayankhe kuti inde komanso ayi. Tinganene kuti inde chifukwa khalidweli limatichititsa kuti tizimuopa moyenera komanso tizimulemekeza kwambiri monga taonera m’mutu wapitawu. Baibulo limatiuza kuti mantha amenewa, ndi “chiyambi cha nzeru.” (Salimo 111:10) Koma tingayankhenso kuti ayi chifukwa palibe chifukwa chilichonse choti tizinjenjemera ndi mantha kapena tizilephera kumuyandikira chifukwa choti iye ali ndi mphamvu.
18. (a) N’chifukwa chiyani ambiri sakhulupirira anthu amene ali ndi mphamvu? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova sangakhale ndi makhalidwe oipa ngakhale kuti ali ndi mphamvu?
18 Mu 1887 wolemba mbiri wina wa ku England, dzina lake Acton analemba kuti: “Mphamvu zimapangitsa munthu kukhala ndi makhalidwe oipa ndipo mphamvu zambiri zimapangitsa munthu kukhala ndi makhalidwe oipa kwambiri.” Mawu amenewa akhala akubwerezedwa ndi anthu ambiri mwina chifukwa choti amaona kuti mfundo imeneyi ndi yosatsutsika. Popeza anthu si angwiro, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika ndipo zimenezi n’zimene zakhaladi zikuchitika kuyambira kalekale. (Mlaliki 4:1; 8:9) Chifukwa cha zimenezi, ambiri sakhulupirira anthu omwe ali ndi mphamvu ndipo safuna kukhala nawo pafupi. Yehova ali ndi mphamvu kuposa aliyense. Koma kodi mphamvu zimenezi zimamuchititsa kukhala ndi makhalidwe oipa? Ayi ndithu. Paja taona kuti iye ndi woyera ndipo sangakhale ndi makhalidwe oipa. Yehova ndi wosiyana ndi amuna ndi akazi omwe si angwiro amene ali ndi mphamvu m’dziko loipali. Iye sanagwiritsepo ntchito molakwika mphamvu zake, ndipo sangachite zimenezi.
19, 20. (a) Kodi nthawi zonse Yehova akamasonyeza mphamvu zake amasonyezanso makhalidwe ena ati, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa? (b) Fotokozani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova ndi wodziletsa, nanga n’chifukwa chiyani mukuona kuti zimenezi n’zosangalatsa?
19 Kumbukirani kuti mphamvu si khalidwe lokhalo limene Yehova ali nalo. Kutsogoloku tiphunziranso za chilungamo, nzeru ndiponso chikondi chake. Koma tisaganize kuti Yehova amasonyeza khalidwe lililonse palokhapalokha. Monga mmene tionere m’mitu yotsatirayi, nthawi zonse Yehova akamasonyeza mphamvu zake, amasonyezanso chilungamo, nzeru ndiponso chikondi. Komanso taganizirani za khalidwe lina limene Mulungu ali nalo, limene atsogoleri ambiri a m’dzikoli alibe. Khalidwe limeneli ndi kudziletsa.
20 Tiyerekeze kuti mwakumana ndi chimunthu chachikulu ndiponso champhamvu moti mukuchita mantha. Koma kenako mukuzindikira kuti munthu wake ndi wodekha. Iye ndi wofunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo pothandiza ndiponso kuteteza anthu, makamaka amene alibe wowathandiza. Munthuyo sagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika. Anthu akumunenera zoipa pa zifukwa zosamveka, koma iye sakutekeseka ndipo akukhalabe wodekha. Mukuyamba kukayikira ngati inuyo mukanakwanitsa kuchita zimenezi, makamaka mukanakhala wamphamvu ngati iyeyo. Pamene mukupitiriza kumudziwa bwino, n’zosachita kufunsa kuti mungayambenso kufuna kuti akhale mnzanu. Tili ndi chifukwa chomveka chotichititsa kuti tizifuna kuti Yehova wamphamvuyonse akhale mnzathu. Taganizirani chiganizo chonse pamene pachokera mutu wa nkhaniyi: “Yehova sakwiya msanga ndipo ali ndi mphamvu zambiri.” (Nahumu 1:3) Yehova safulumira kugwiritsa ntchito mphamvu zake polanga anthu, ngakhale anthu oipa. Iye safulumira kukwiya ndipo ndi wokoma mtima. Ngakhale kuti nthawi zambiri anthu amamukhumudwitsa, iye wasonyeza kuti “sakwiya msanga.”—Salimo 78:37-41.
21. N’chifukwa chiyani Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani zokhudza iyeyo?
21 Yehova amasonyeza kudziletsa m’njira inanso. Kodi inuyo mukanakhala ndi mphamvu zambiri, bwenzi nthawi zina mukufuna kuti anthu achite zinthu m’njira imene inuyo mukuganiza? Yehova ali ndi mphamvu zonse, koma sakakamiza anthu kuti azimutumikira. Ngakhale kuti kutumikira Mulungu n’kumene kudzachititse kuti tidzapeze moyo wosatha, Yehova satikakamiza kumutumikira. M’malomwake, iye amalemekeza munthu aliyense pomupatsa ufulu wosankha. Amatichenjeza kuti ngati munthu sanasankhe bwino, amakumana ndi mavuto ndipo amatiuzanso kuti munthu akasankha mwanzeru, zotsatira zake zimakhala zabwino. Koma amatisiya kuti tisankhe tokha. (Deuteronomo 30:19, 20) Yehova safuna kuti anthu azimutumikira chifukwa chokakamizika kapena chifukwa choopa kuti iye ali ndi mphamvu zambiri. Amafuna kuti anthu omwe amamutumikira mwa kufuna kwawo chifukwa choti amamukonda.—2 Akorinto 9:7.
22, 23. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amasangalala kupatsa ena mphamvu? (b) Kodi tiphunzira chiyani m’mutu wotsatira?
22 Tiyeni tione chifukwa chomaliza chotichititsa kuti tisamachite mantha ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Anthu omwe ali ndi mphamvu amaopa kugawirako ena mphamvu zawo. Komatu Yehova amasangalala kupereka mphamvu kwa atumiki ake okhulupirika. Amapatsakonso ena mphamvu zake. Mwachitsanzo, anapereka mphamvu zambiri ndithu kwa Mwana wake. (Mateyu 28:18) Yehova amapatsa mphamvu atumiki ake m’njira inanso. Baibulo limati: “Inu Yehova, ukulu, mphamvu, kukongola, ulemerero ndi ulemu ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi ndi zanu. . . . M’dzanja lanu muli mphamvu ndi nyonga ndipo dzanja lanu limatha kukweza ndiponso kupereka mphamvu kwa onse. “—1 Mbiri 29:11, 12.
23 Izitu zikusonyeza kuti Yehova amasangalala kukupatsani mphamvu. Iye amaperekanso “mphamvu yoposa yachibadwa” kwa anthu amene akufuna kumutumikira. (2 Akorinto 4:7) Kodi kudziwa zimenezi sikukukuchititsani kufuna kuti Mulungu ameneyu, yemwe amagwiritsa ntchito mphamvu zake mokoma mtima ndi mwachikondi, akhale mnzanu? M’mutu wotsatira, tiona mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake polenga zinthu.
a Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “Wamphamvuyonse” amatanthauza kuti “Wolamulira Zinthu Zonse; Amene Ali ndi Mphamvu Zonse.”
b Baibulo limati ‘Yehova sanali mumphepoyo, m’chivomerezicho ndiponso m’motowo.’ Atumiki a Yehova sali ngati anthu amene amalambira mphamvu zam’chilengedwe. Yehova ndi wamkulu kwambiri moti sangakwane m’chilichonse chimene analenga.—1 Mafumu 8:27.
-
-
Mphamvu za Kulenga—“Amene Anapanga Kumwamba Komanso Dziko Lapansi”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 5
Mphamvu za Kulenga—‘Anapanga Kumwamba Komanso Dziko Lapansi’
1, 2. Kodi dzuwa limasonyeza bwanji kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kulenga zinthu mwadongosolo?
KODI chimachitika n’chiyani mukamawotha moto madzulo kukuzizira? Mwina mumakhala chapataliko kuti muzimva kutenthera bwino. Mukasendera pafupi kwambiri ndi motowo, mumamva kuwotcha. Mukasunthira kutali kwambiri, mumayamba kumva kuzizira.
2 Dzuwa tingaliyerekezere ndi “moto” umene umatithandiza kuti tizimva kutentha. Kuchokera padziko pano kukafika pamene pali dzuwa pali mtunda wa makilomita 150 miliyoni.a Ndiye kuti dzuwa ndi lamphamvu kwambiri chifukwa timamva kutentha kwake tili padziko pano ngakhale kuti lili kutali chonchi. Koma dziko lapansi limazungulira dzuwa ndipo lili pa mtunda wabwino kwambiri kuchokera pamene pali dzuwalo. Likanayandikira kwambiri, madzi onse padzikoli akanauma, ndipo likanatalikira kwambiri madzi onse akanaundana. Kuyandikira kwambiri kapena kutalikira kwambiri kukanachititsa kuti padzikoli pasakhale chamoyo chilichonse. Kuwala kwa dzuwa n’kofunika kwambiri kuti padziko lapansi pakhale zinthu zamoyo. Kumathandizanso kuti dzikoli likhale laukhondo komanso lokongola.—Mlaliki 11:7.
3. Kodi dzuwa limatiphunzitsa chiyani?
3 Komabe, anthu ambiri saganizira kwambiri kuti dzuwa ndi lofunika ngakhale kuti moyo wathu umadalira dzuwalo. Choncho sadziwa zimene dzuwa lingatiphunzitse. Ponena za Yehova, Baibulo limati: “Munapanga kuwala komanso dzuwa.” (Salimo 74:16) Zoonadi, dzuwa limalemekeza Yehova “amene anapanga kumwamba komanso dziko lapansi.” (Salimo 19:1; 146:6) Dzuwa ndi chimodzi mwa zinthu zambirimbiri zakumwamba zimene zimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kulenga zinthu. Tiyeni tikambirane mozamirapo zinthu zina zakumwamba ndipo kenako tikambirana zokhudza dziko lapansi komanso zamoyo zimene zili padzikoli.
Yehova ‘anapanga kuwala komanso dzuwa’
“Kwezani Maso Anu Kumwamba Ndipo Muone”
4, 5. Kodi dzuwa lili ndi mphamvu zochuluka bwanji, nanga ndi lalikulu bwanji? Kodi dzuwa ndiye nyenyezi yaikulu kwambiri? Fotokozani.
4 Mwina mukudziwa kuti dzuwa lathuli ndi nyenyezi. Limaoneka lalikulu kuposa nyenyezi zomwe timaona usiku chifukwa lili pafupi kwambiri poyerekezera ndi nyenyezizo. Kodi dzuwa ndi lamphamvu bwanji? Pakatikati pake m’potentha pafupifupi madigiri seshasi 15 miliyoni. Mutatenga kachibenthu ka pakati pa dzuwa kangati njere ya therere lobala n’kukaika padziko lapansi pano, kuti musapse mungafunike kuima pa mtunda wa makilomita 140 kuchokera pamene mwakaikapo. Pa sekondi iliyonse, dzuwa limatulutsa mphamvu zofanana ndi zimene zimatuluka pakaphulika mabomba a nyukiliya mamiliyoni mahandiredi mahandiredi.
5 Dzuwa ndi lalikulu kwambiri moti mukhoza kulowa mapulaneti aakulu ngati dziko lapansili okwanira 1,300,000. Kodi ndiye kuti nyenyezi yaikulu kwambiri ndi dzuwa? Ayi, asayansi amanena kuti dzuwa ndi nyenyezi yaing’ono kwambiri poyerekeza ndi nyenyezi zina. Mtumwi Paulo analemba kuti “ulemerero wa nyenyezi ina, umasiyananso ndi wa nyenyezi ina.” (1 Akorinto 15:41) Mzimu woyera ndi umene unathandiza Paulo kuti alembe mawu oonawa. Pali nyenyezi ina yaikulu imene ataiika pamalo pamene pali dzuwa, dziko lapansili likhoza kukhala m’kati mwa nyenyeziyo. Palinso nyenyezi ina yaikulu kwambiri yomwe ataiika pamalo omwewo ikhoza kudutsa dziko lapansi n’kukafika kupulaneti yotchedwa Saturn. Pulaneti imeneyi ili kutali kwambiri ndi dziko lapansili. Moti chombo cha mumlengalenga chinatenga zaka 4 kuti chikafike papulaneti imeneyo, komatu chinkathamanga pa liwiro loposa kuwirikiza maulendo 40 liwiro la chipolopolo cha mfuti yamphamvu kwambiri.
6. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti nyenyezi n’zochuluka kwambiri?
6 Chochititsa chidwi kwambiri kuposa kukula kwa nyenyezi ndi kuchuluka kwake. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti nyenyezi zilipo zambirimbiri ngati “mchenga” wakunyanja moti n’zosatheka kuziwerenga. (Yeremiya 33:22) Mawu amenewa akusonyeza kuti nyenyezi zilipo zambiri kuposa zimene maso athu angaone popanda kugwiritsa ntchito chipangizo chilichonse. Wolemba Baibulo ngati Yeremiya akanayang’ana kumwamba usiku kuti awerenge nyenyezi, akanangowerenga 3,000 zokha kapena kuposerapo, chifukwa ndi zimene munthu angathe kuona usiku kopanda mitambo. Tingayerekeze nambala imeneyi ndi mchenga wongodzaza dzanja. Koma zoona zake n’zakuti nyenyezi ndi zambiri ngati mchenga wakunyanja.b Ndiye ndani angathe kuziwerenga?
“Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake”
7. Kodi mlalang’amba wa Milky Way uli ndi nyenyezi zingati, nanga pali milalang’amba ingati?
7 Lemba la Yesaya 40:26 limati: “Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone. Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi? Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwerenga. Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake.” Lemba la Salimo 147:4 limati: “Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi zonse.” Kodi “chiwerengero cha nyenyezi zonse” n’chochuluka bwanji? Limeneli ndi funso lovuta kuyankha. Asayansi amati mumlalang’amba wathu wokhawu, womwe amautchula kuti Milky Way, muli nyenyezi zoposa 100 biliyoni.c Ena amati mumlalang’ambawu muli nyenyezi zoposa pamenepa. Komatu umenewu ndi umodzi mwa milalang’amba yambirimbiri yomwe ilipo ndipo yambiri ili ndi nyenyezi zoposa pamenepa. Ndiye kodi milalang’amba ilipo ingati? Asayansi ena amati ilipo mabiliyoni mahandiredi mahandiredi, mwinanso mathiriliyoni. Pofika pano zaoneka kuti anthu sangathe kudziwa kuchuluka kwa milalang’amba, ngakhalenso chiwerengero chenicheni cha nyenyezi mabiliyoni zomwe zili mumilalang’ambayi. Komatu Yehova amadziwa chiwerengero chake. Ndiponso nyenyezi iliyonse amaipatsa dzina.
8. (a) Kodi mlalang’amba wa Milky Way ndi waukulu bwanji? (b) Kodi Yehova amalamulira bwanji zinthu zakumwamba?
8 Timagoma kwambiri tikaganizira kukula kwa milalang’amba. Anthu amati kuchokera mbali ina kukafika mbali ina ya mlalang’amba wa Milky Way kutalika kwake n’kofanana ndi mtunda umene kuwala kumayenda pa zaka 100,000. Kuwala kumayenda mothamanga kwambiri pa liwiro la makilomita 300,000 pa sekondi imodzi. Ndiyeno taganizirani, kuwala kungatenge zaka 100,000 kuti kuyende kuchoka mbali ina ya mlalang’amba wathuwu kukafika mbali ina. Ndipo milalang’amba ina ndi yaikulu kwambiri kuposa mlalang’amba wathuwu. Baibulo limati Yehova amatambasula “kumwamba” ngati mmene munthu angatambasulire nsalu. (Salimo 104:2) Komanso iye anakonza mmene nyenyezi ndiponso milalang’amba iyenera kuyendera. Kuyambira pa tinthu ting’onoting’ono mpaka milalang’amba ikuluikulu, chilichonse chimayenda mogwirizana ndi malamulo a m’chilengedwe amene Mulungu anakhazikitsa. (Yobu 38:31-33) Choncho akatswiri asayansi amati mmene zinthu zakumwamba zimayendera mwadongosolo n’zofanana ndi kuvina gule amene masitepe ake ndi ovuta kwambiri. Ndiyeno taganizani za amene analenga zinthu zimenezi. Kunena zoona, timasowa chonena tikaganizira mphamvu zochuluka kwambiri zotha kulenga zinthu zimene Mulungu ali nazo.
“Amene Anapanga Dziko Lapansi Pogwiritsa Ntchito Mphamvu Zake”
9, 10. Kodi n’chifukwa chiyani tinanganene kuti Yehova anaika dzikoli pamalo abwino kwambiri, nanga zimenezi zimatiuza chiyani zokhudza iyeyo?
9 Mphamvu za Yehova zotha kulenga zinthu zimaonekeranso bwino tikaganizira mmene analengera dziko lapansili. Analiika pamalo abwino kwambiri m’chilengedwe chachikuluchi. Asayansi ena amakhulupirira kuti mwina m’milalang’amba yambiri mulibe pulaneti lokhala ndi zamoyo ngati pulaneti lathuli. Zikuonekanso kuti mbali yaikulu ya mlalang’amba wa Milky Way sinakonzedwe kuti kuzikhala zamoyo. Pakatikati pa mlalang’ambawu ndi podzaza ndi nyenyezi, pamatuluka mpweya wambiri wapoizoni ndipo nthawi zambiri nyenyezi zimatsala pang’ono kuwombana. M’mbali mwa mlalang’ambawu mulibe zinthu zambiri zothandiza kuti moyo ukhalepo. Koma dzuwa komanso zinthu zonse zimene zimayenda molizungulira zinaikidwa pamalo abwino a pakati pa mbali ziwirizi.
10 Dziko lapansi limatetezedwa ndi pulaneti lina lotchedwa Jupita lomwe lili kutali komanso n’lalikulu kwambiri. Chifukwa chakuti ndi lalikulu maulendo oposa 1,000 kuposa dziko lapansi, pulaneti la Jupita limakoka zinthu mwamphamvu kwambiri. Limakoka zinthu zimene zikuyenda mumlengalenga kuti zizipita kumene kuli pulanetili. Ndiye kodi zotsatira zake zimakhala zotani? Asayansi anapeza kuti zikanakhala kuti pulanetili palibe, zinthu zochokera mumlengalenga zomwe zimagwera padzikoli, bwenzi zikugwa mwamphamvu kwambiri kuwirikiza nthawi 10,000 poyerekeza ndi mmene zimagwera panopa. Komanso dziko lathuli lili ndi setilaiti yapadera kwambiri yomwe ndi mwezi. Mwezi umathandiza kuti padzikoli pazikongola komanso umatiunikira usiku. Koma kuwonjezera pamenepo umachititsanso kuti nthawi zonse dziko liziima mopendekeka pamalo amodzi. Kupendekeka kumeneku n’kumene kumachititsa kuti padzikoli pazikhala nyengo zodziwika bwino, chinthu china chofunika kwambiri kuti padzikoli pakhale zamoyo.
11. Kodi mpweya wamumlengalenga unakonzedwa bwanji kuti uzititeteza?
11 Mphamvu za Yehova zotha kulenga zinthu zimaonekeranso pa chilichonse chimene anapanga chokhudza dziko lapansi. Chitsanzo cha zimenezi ndi mpweya wina wamumlengalenga umene umatiteteza. Dzuwa limatulutsa kuwala kwabwino ndiponso kwakupha. Kuwala kwakupha kukafika mlengalenga kumasintha mpweya wa okosijeni kuti ukhale mpweya wotchedwa ozoni. Kenako mpweya wa ozoni umayamwa gawo lalikulu la kuwala kwakupha kuja. Choncho tinganene kuti, dziko lapansili analipanga m’njira yoti lizidziteteza lokha.
12. Kodi kayendedwe ka madzi kamasonyeza bwanji kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kulenga?
12 Imeneyi ndi mbali imodzi yokha yokhudza mumlengalenga mmene muli mpweya wamitundumitundu wothandiza kuti padzikoli pakhale zinthu zamoyo. Chinthu chinanso chodabwitsa chimene chimachitika mumlengalenga ndi kayendedwe ka madzi. Chaka chilichonse dzuwa limachititsa madzi oposa makiyubiki kilomita 400,000 ochokera m’nyanja komanso nyanja zikuluzikulu kuti akhale nthunzi yomwe imapita mumlengalenga. Madziwo amapanga mitambo yomwe imamwazidwa ndi mphepo. Kenako madzi amenewa, amene tsopano amakhala osefedwa bwino komanso oyera, amagwa pansi ngati mvula, sinowo ndiponso madzi oundana n’kudzazanso m’mitsinje ndi m’nyanja. Zimachitika mogwirizana ndi zimene lemba la Mlaliki 1:7 limanena, kuti: “Mitsinje yonse imakathira m’nyanja koma nyanjayo sidzaza. Imabwerera kumalo kumene ikuchokera kuti ikayambirenso kuyenda.” Yehova yekha ndi amene anachititsa kuti madzi azizungulira chonchi.
13. Kodi zomera ndiponso dothi zimatiphunzitsa chiyani zokhudza mphamvu za Mlengi wathu?
13 Kulikonse kumene timaona zinthu zamoyo, timaona umboni wakuti Mlengi wathu ali ndi mphamvu zolenga zinthu. Kungoyambira mitengo yaikulu kwambiri yomwe imatalika kuposa nyumba 30 zosanjikizana mpaka tizomera ting’onoting’ono tooneka ndi maikosikopu tomwe timadzaza m’nyanja zikuluzikulu n’kumapereka mpweya wambiri wa okosijeni womwe timapuma, timaona umboni woti Yehova ali ndi mphamvu. Ngakhalenso mudothi muli zinthu zamoyo zambirimbiri monga nyongolotsi, tomera ting’onoting’ono tooneka ngati nkhungu ndiponso tizilombo ting’onoting’ono. Zonsezi zimathandizira kuti zomera zikule. M’pake kuti Baibulo limati nthaka ili ndi mphamvu yothandiza kuti anthu azikolola mokwanira.—Genesis 4:12.
14. Kodi atomu, yomwe ndi kanthu kakang’ono kwambiri, ili ndi mphamvu zambiri bwanji?
14 N’zosachita kufunsa kuti Yehova “anapanga dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake.” (Yeremiya 10:12) Umboni wakuti Mulungu ali ndi mphamvu timauonanso ngakhale m’tinthu ting’onoting’ono kwambiri timene analenga. Mwachitsanzo, mutaika pamodzi maatomu 1 miliyoni amaonekabe kanthu kakang’ono poyerekeza ndi tsitsi limodzi la munthu. Kuwonjezera pamenepa, kanthu komwe kali pakati pa atomu, komwe ndi kakang’ono kwambiri, kali ndi mphamvu zambiri moti anthu amakagwiritsa ntchito popangira mabomba amphamvu kwambiri a nyukiliya.
“Chamoyo Chilichonse”
15. Pofotokoza nyama zosiyanasiyana zakutchire, kodi Yehova ankafuna kumuphunzitsa chiyani Yobu?
15 Umboni wina wosatsutsika wakuti Yehova ali ndi mphamvu zolenga, timaupeza tikaona nyama zambirimbiri zomwe zili padzikoli. Salimo 148 limanena za zinthu zambiri zomwe zimatamanda Yehova, ndipo vesi 10 limatchula ‘nyama zakutchire ndi nyama zoweta.’ Posonyeza chifukwa chake munthu ayenera kupereka ulemu kwa Mlengi, Yehova analankhula ndi Yobu za nyama monga mkango, mbidzi, njati, mvuu ndi ng’ona. Kodi ankafuna kumuphunzitsa chiyani? Ngati anthu amachita mantha ndi nyama zimenezi zomwe ndi zamphamvu, zoopsa ndiponso zosazolowereka, kodi ayenera kumva bwanji akaganizira za Mlengi wa nyamazi?—Yobu, chaputala 38-41.
16. N’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi mbalame zina zimene Yehova analenga?
16 Salimo 148:10 likutchulanso “mbalame zamapiko.” Ndipotu mbalame zimenezi zilipo zamitundu yambirimbiri. Yehova anauza Yobu za nthiwatiwa, imene “imaseka hatchi ndi wokwerapo wake.” Mbalameyi ndi yaitali mamita awiri ndi hafu ndipo siuluka. Komatu imathamanga makilomita 65 pa ola limodzi ndipo ikamathamanga, imaponya phazi lake mamita 4 ndi hafu kuchokera paphazi lina. (Yobu 39:13, 18) Ndiye palinso mbalame ina yotchedwa albatross imene nthawi yambiri ya moyo wake imakhala ikuuluka pamwamba pa nyanja. Imatha kuuluka kwa maola ambirimbiri popanda kukupiza mapiko ake omwe ikawatambasula ndi aatali mamita atatu. Ndiyeno tasiyanitsani ndi mbalame inanso yofanana ndi choso yotchedwa bee hummingbird. Mbalameyi ndi yaitali masentimita 5 okha ndipo ndi mbalame yaing’ono kwambiri pa mbalame zonse. Imatha kukupiza mapiko ake ka 80 pa sekondi imodzi. Mbalamezi zimanyezimira ngati miyala ing’onoing’ono yamtengo wapatali, ndipo zimatha kuuluka chobwerera m’mbuyo komanso zimatha kuima m’malere ngati ndege za helikoputa.
17. Kodi nsomba yotchedwa blue whale ndi yaikulu bwanji, nanga tinganene chiyani pambuyo poganizira nyama zimene Yehova analenga?
17 Lemba la Salimo 148:7 limanena kuti ngakhalenso ‘zamoyo zam’nyanja’ zimalemekeza Yehova. Taganizirani za nangumi wotchedwa blue whale, nyama imene ambiri amati ndi yaikulu kwambiri pa nyama zonse. Chinsomba chimenechi, chomwe chimasambira “m’madzi akuya,” chimatha kutalika mpaka kufika mamita 30 kapena kuposa. Kulemera kwake kungafanane ndi kulemera kwa njovu zikuluzikulu 30. Kulemera kwa lilime lake lokha kumafanana ndi njovu imodzi. Mtima wake ndi waukulu ngati galimoto yaing’ono. Chiwalo chachikulu chimenechi chimagunda maulendo 9 okha pa 1 miniti, mosiyana ndi mtima wa mbalame yotchedwa hummingbird ija womwe umagunda pafupifupi maulendo 1,200 pa 1 miniti. Chinsomba chimenechi chili ndi mtsempha wina waukulu kwambiri moti mwana akhoza kukwawamo. Kunena zoona, timagwirizana ndi mawu omaliza a m’buku la Masalimo akuti: “Chamoyo chilichonse chitamande Ya.”—Salimo 150:6.
Zimene Tingaphunzire Tikaganizira Mphamvu za Yehova
18, 19. Kodi zinthu zamoyo zimene Yehova analenga padzikoli ndi zochuluka bwanji, nanga kodi chilengedwe chimatiphunzitsa chiyani zokhudza ulamuliro wake?
18 Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu? Timasowa chonena tikaona kuchuluka kwa zinthu zosiyanasiyana zimene analenga. Wolemba masalimo wina anati: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! . . . Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.” (Salimo 104:24) Zimenezitu ndi zoona. Asayansi apeza kuti padzikoli pali mitundu ya zamoyo yopitirira 1 miliyoni. Koma ena amati n’kutheka kuti pali zamoyo zambiri kuposa pamenepa. Nthawi zina munthu waluso angaone kuti akusowa zinthu zatsopano zoti achite. Koma luso la Yehova komanso mphamvu zake zotha kulenga zinthu zatsopano ndiponso zosiyanasiyana, sizidzatha.
19 Mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu zimatiphunzitsa kuti iye ndi woyenera kulamulira. Ndipotu mawu akuti “Mlengi” amasiyanitsa Yehova ndi aliyense m’chilengedwechi chifukwa zinthu zina zonse zinachita kulengedwa ndi iyeyo. Ngakhalenso Mwana wobadwa yekha wa Yehova, amene anali “mmisiri waluso” pa nthawi yolenga zinthu, m’Baibulo samutchula kuti Mlengi kapena Mlengi mnzake. (Miyambo 8:30; Mateyu 19:4) M’malomwake, iye ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Popeza Yehova ndi amene analenga chilichonse, iye yekha ndi amene ali ndi ufulu wolamulira aliyense komanso chilichonse.—Aroma 1:20; Chivumbulutso 4:11.
20. Kodi tikamati Yehova atamaliza kulenga zinthu padziko lapansi anapuma zikutanthauza chiyani?
20 Kodi Yehova anasiya kugwiritsa ntchito mphamvu zake zolengera zinthu? Baibulo limanena kuti Yehova atamaliza ntchito yake yolenga pa tsiku la 6, ‘pa tsiku la 7 anayamba kupuma pa ntchito yonse imene ankagwira.’ (Genesis 2:2) Mtumwi Paulo anasonyeza kuti “tsiku” la 7 limeneli ndi lalitali zaka masauzande ambiri, poti linali lidakalipo m’nthawi yake. (Aheberi 4:3-6) Koma kodi ‘kupuma’ kukutanthauza kuti Yehova anasiyiratu kugwira ntchito? Ayi, Yehova sasiya kugwira ntchito. (Salimo 92:4; Yohane 5:17) Choncho mfundo yoti anapuma iyenera kuti ikungotanthauza kuti anasiya kugwira ntchito yolenga zinthu padzikoli. Komabe, akupitiriza kugwira ntchito yokwaniritsa zolinga zake ndipo ntchito imeneyi sinaimitsidwe. Zina mwa zimene anachita ndi kuuzira anthu kuti alembe Malemba Opatulika komanso anapanga “cholengedwa chatsopano.” Tidzakambirana za zimenezi m’Mutu 19.—2 Akorinto 5:17.
21. Kodi kuganizira mphamvu za Yehova zolenga zinthu kudzathandiza bwanji anthu okhulupirika omwe adzakhalepo mpaka kalekale?
21 Tsiku lopuma la Yehova likadzatha, iye adzanena kuti ntchito zake zonse zapadziko lapansi ndi “zabwino kwambiri,” ngati mmene ananenera tsiku la 6 lolenga zinthu litatha. (Genesis 1:31) Tidzaona nthawi yomweyo mmene pa nthawiyo azidzagwiritsira ntchito mphamvu zake zolenga zinthu. Koma tingakhale otsimikiza kuti nthawi zonse tizidzachita chidwi ndi mmene Yehova azidzagwiritsira ntchito mphamvu zotha kulenga. Tizidzaphunzira zokhudza Yehova mpaka kalekale kudzera m’zinthu zimene analenga. (Mlaliki 3:11) Pamene tizidzaphunzira zambiri zokhudza Mlengi wathu wamkuluyu, m’pamenenso tizidzamulemekeza kwambiri, kuchita naye chidwi ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wolimba.
a Kuti mumvetse bwino kutalika kwa mtunda umenewu, ganizirani izi: Kuti muyende mtunda umenewu pa galimoto, ngakhale mutamayendetsa pa liwiro la makilomita 160 pa ola limodzi kwa maola 24 pa tsiku, zingakutengereni zaka zoposa 100 kuti mukafike.
b Ena amaganiza kuti kale anthu ankagwiritsa ntchito chipangizo chachikale choonera zinthu zomwe zili kutali. Iwo amati, kodi anthu a nthawi imeneyo paokha akanadziwa bwanji kuti nyenyezi zilipo zambiri ndipo n’zosawerengeka? Koma amanyalanyaza mfundo yoti Yehova, yemwe ndi Mlembi wamkulu wa Baibulo, ndi amene ankathandiza anthuwo kudziwa zimenezi.—2 Timoteyo 3:16.
c Taganizirani kuti mungatenge nthawi yaitali bwanji kuti muwerenge nyenyezi 100 biliyoni zokha. Ngati mungakwanitse kumawerenga nyenyezi imodzi pa sekondi iliyonse, kwa maola 24 pa tsiku, mungatenge zaka 3,171 kuti mumalize kuwerenga zonsezo.
-
-
Mphamvu Zowononga—‘Yehova Ndi Msilikali Wamphamvu’Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 6
Mphamvu Zowononga—“Yehova Ndi Msilikali Wamphamvu”
1-3. (a) Kodi Aisiraeli anakumana ndi zinthu ziti zoopsa? (b) Kodi Yehova anachita chiyani pomenyera nkhondo anthu ake?
AISIRAELI analibe kothawira chifukwa anali pakati pa mapiri ovuta kukwera ndipo kutsogolo kwawo kunali nyanja yoti sakanatha kuwoloka. Pa nthawiyi n’kuti gulu la asilikali a Aigupto, omwe anali ankhanza kwambiri, likuwathamangitsa ndipo linali litatsimikiza mtima kuti liphe Aisiraeli onse.a Koma Mose analimbikitsa anthu a Mulunguwo kuti asataye mtima. Anawatsimikizira kuti: “Yehova adzakumenyerani nkhondo.”—Ekisodo 14:14.
2 Komabe zikuoneka kuti Mose anafuulira Yehova, ndipo iye anayankha kuti: “N’chifukwa chiyani ukundidandaulira? . . . Utenge ndodo yako n’kutambasula dzanja lako kuloza panyanja kuti nyanjayo igawanike.” (Ekisodo 14:15, 16) Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona zimene zikuchitika. Nthawi yomweyo Yehova akulamula mngelo kuti apite kumbuyo kwa Aisiraeli, ndipo mtambo ukuchoka kutsogolo kwa Aisiraeli n’kukaima kumbuyo kwawo, mwina ngati khoma n’kutsekereza Aigupto kuti asayambe kupha Aisiraeliwo. (Ekisodo 14:19, 20; Salimo 105:39) Mose akutambasula dzanja lake. Chifukwa cha mphepo yamphamvu imene ikukankha madzi, nyanjayo ikugawanika. Madziwo akuunjikana n’kuima ngati makoma. Zimenezi zikupangitsa kuti pakhale njira yaikulu moti mtundu wonsewu ukudutsa bwinobwino.—Ekisodo 14:21; 15:8.
3 Zinthu zodabwitsa zimenezi, zikanatha kupangitsa Farao kulamula asilikali ake kuti abwerere. Koma Farao, yemwe anali wonyada, akuwalamula kuti amenye nkhondo. (Ekisodo 14:23) Asanaganize n’komwe, Aiguputowo akuyamba kuwoloka pofuna kuthamangitsa Aisiraeliwo. Koma pasanapite nthawi, pakuyambika chisokonezo chifukwa mawiro a magaleta awo ayamba kuguluka. Aisiraeli atafika kutsidya lina la nyanja, Yehova akulamula Mose kuti: “Tambasula dzanja lako n’kuloza panyanja kuti madzi abwerere n’kumiza Aiguputo, magaleta awo ankhondo ndi asilikali awo apamahatchi.” Makoma a madziwo akugwa n’kumiza Farao ndi asilikali ake.—Ekisodo 14:24-28; Salimo 136:15.
4. (a) Kodi Yehova anakhala ndani pa Nyanja Yofiira? (b) Kodi anthu ena angamve bwanji akadziwa kuti nthawi zina Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake kumenya nkhondo?
4 Zimene Yehova anachita populumutsa Aisiraeli pa Nyanja Yofiira zimatiphunzitsa zambiri zokhudza iyeyo. Pamenepa Yehova anasonyezadi kuti ndi “msilikali wamphamvu.” (Ekisodo 15:3) Komabe, kodi inuyo mukumva bwanji kudziwa kuti Yehova nthawi zina amakhala msilikali? Kunena zoona, anthu ambiri akhala akuvutika komanso kusowa mtendere chifukwa cha nkhondo. Kodi mwina mfundo yoti nthawi zina Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake popha anthu ikukuchititsani kuona kuti sangakhale mnzanu?
Pa Nyanja Yofiira Yehova anasonyeza kuti ndi “msilikali wamphamvu”
Nkhondo ya Mulungu Ndi Yosiyana ndi Nkhondo za Anthu
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti Mulungu amatchedwa “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba”? (b) Kodi nkhondo za Mulungu zimasiyana bwanji ndi za anthu?
5 Mulungu amatchulidwa ndi dzina laudindo lakuti, “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba” pafupifupi maulendo 260 m’Malemba a Chiheberi ndiponso kawiri m’Malemba a Chigiriki Achikristu. (1 Samueli 1:11) Popeza Yehova ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse, iye amalamulira gulu lankhondo lalikulu la angelo. (Yoswa 5:13-15; 1 Mafumu 22:19) Angelo amenewa ndi amphamvu kwambiri. (Yesaya 37:36) Sizisangalatsa kumva nkhani yokhudza kuphedwa kwa anthu. Komabe, tisaiwale kuti nkhondo ya Mulungu ndi yosiyana ndi nkhondo za anthu. Akuluakulu a asilikali komanso atsogoleri andale nthawi zina amanena kuti anali ndi zifukwa zomveka zomenyera nkhondo. Koma nthawi zonse anthu amamenya nkhondo chifukwa cha dyera komanso kudzikonda.
6 Koma mosiyana ndi anthu, Yehova sachita zinthu chifukwa cha mmene akumvera basi. Lemba la Deuteronomo 32:4 limati: “Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita zinthu zopanda chilungamo. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.” Mawu a Mulungu amaletsa kukwiya mosadziletsa, nkhanza ndiponso chiwawa. (Genesis 49:7; Salimo 11:5) Choncho Yehova samenya nkhondo popanda chifukwa chomveka. Sagwiritsa ntchito mwachisawawa mphamvu zake zowononga ndipo amazigwiritsa ntchito pakakhala kuti palibenso njira ina yothetsera vutolo. Kudzera mwa mneneri wake Ezekieli iye ananena kuti: “‘Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wochimwa? Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wochimwayo alape n’kupitiriza kukhala ndi moyo?’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”—Ezekieli 18:23.
7, 8. (a) Kodi Yobu ankaganiza kuti akuvutika chifukwa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani ankalakwitsa kuganiza choncho? (b) Kodi Elihu anathandiza bwanji Yobu kuti asinthe maganizo olakwika? (c) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinachitikira Yobu?
7 Ndiye n’chifukwa chiyani Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga? Tisanayankhe funsoli, tiyeni tiganizire za Yobu yemwe anali munthu wolungama. Satana anakayikira ngati Yobu, komanso munthu wina aliyense, angakhalebe wokhulupirika akamayesedwa. Yehova anayankha nkhaniyi polola kuti Satana ayese Yobu. Zotsatira zake zinali zakuti Yobu anadwala, chuma chake chinawonongeka komanso ana ake anafa. (Yobu 1:1-22; 2:1-8) Chifukwa chakuti Yobu sankadziwa zimene zinkachititsa kuti azivutika, iye anayamba kuganiza kuti Mulungu ankamulanga mopanda chilungamo. Yobu anafunsa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukulimbana ndi ine?” Anamufunsanso kuti: ‘N’chifukwa chiyani mukundiona ngati mdani wanu?’—Yobu 7:20; 13:24.
8 Mnyamata wina wotchedwa Elihu anathandiza Yobu kuzindikira kuti ankaganiza molakwika pomufunsa kuti: “Kodi mukutsimikiza kuti zimene mukunena n’zoona moti munganene kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu’?” (Yobu 35:2) Choncho n’kupanda nzeru kuganiza kuti ndife abwino kuposa Mulungu kapena kuganiza kuti iye wachita zinthu mopanda chilungamo. Elihu ananena kuti: “N’zosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa, kapena kuti Wamphamvuyonse achite zinthu zolakwika.” Pa nthawi ina ananenanso kuti: “Wamphamvuyonse sitingathe kumumvetsa. Iye ali ndi mphamvu zazikulu, ndipo sachita zinthu zosemphana ndi chilungamo chake komanso kulungama kwake kodabwitsa.” (Yobu 34:10; 36:22, 23; 37:23) Sitiyenera kukayikira kuti Mulungu akamamenya nkhondo, amakhala ndi zifukwa zomveka zochitira zimenezo. Pamene tikuganizira mfundo imeneyi, tiyeni tione zifukwa zimene zimachititsa kuti nthawi zina Mulungu, yemwe ndi wamtendere, amenye nkhondo.—1 Akorinto 14:33.
N’chifukwa Chiyani Mulungu Wamtendere Amamenya Nkhondo?
9. N’chifukwa chiyani Mulungu yemwe ndi woyera amamenya nkhondo?
9 Mose atatamanda Mulungu kuti ndi “msilikali wamphamvu,” ananena kuti: “Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova? Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa, ndani angafanane ndi inu?” (Ekisodo 15:11) Nayenso mneneri Habakuku ananena kuti: “Maso anu ndi oyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa, ndipo simungalekerere khalidwe loipa.” (Habakuku 1:13) Ngakhale kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, iye ndi Mulungunso woyera komanso wachilungamo. Nthawi zina, makhalidwe amenewa amamuchititsa kuti agwiritse ntchito mphamvu zake zowononga. (Yesaya 59:15-19; Luka 18:7) Choncho Mulungu akamamenya nkhondo sizitanthauza kuti si woyera. Ndipotu iye amamenya nkhondo chifukwa choti ndi woyera.—Ekisodo 39:30.
10. Kodi ndi njira iti yokha yomwe ingathandize kuthetsa chidani chomwe chinanenedwa pa Genesis 3:15, nanga zimenezo zidzathandiza bwanji anthu olungama?
10 Taganizirani zimene zinachitika anthu awiri oyamba, Adamu ndi Hava, atagalukira Mulungu. (Genesis 3:1-6) Yehova akanangonyalanyaza zimene anthuwa anachitazi, udindo wake monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse ukanaoneka ngati wopanda mphamvu. Popeza iye ndi Mulungu wachilungamo, ankayenera kuwapatsa chilango cha imfa. (Aroma 6:23) Mu ulosi woyambirira wa m’Baibulo, iye ananeneratu kuti padzakhala chidani pakati pa atumiki ake ndi anthu amene ali kumbali ya “njoka,” yemwe ndi Satana. (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:15) Yehova ankadziwa kuti chidani chimenechi chidzatha akadzawononga Satana. (Aroma 16:20) Koma chiweruzo chimenecho chidzachititsa kuti anthu olungama alandire madalitso ambiri, chidzachotsa mavuto onse amene Satana wayambitsa padzikoli komanso chidzachititsa kuti dziko lonse likhale Paradaiso. (Mateyu 19:28) Mpaka pamene nthawi imeneyo idzafika anthu amene ali kumbali ya Satana akupitirizabe kutsutsa, kuzunza komanso kufuna kupha anthu a Mulungu. Nthawi zina Yehova amafunika kulowererapo kuti athandize atumiki ake.
Mulungu Amalowererapo Kuti Achotse Zoipa
11. N’chifukwa chiyani Mulungu anaona kuti n’koyenera kuti abweretse chigumula padziko lonse?
11 Chitsanzo cha nthawi imene Yehova anafunika kulowererapo ndi pa nthawi ya Chigumula cha Nowa. Lemba la Genesis 6:11, 12 limati: “Dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi chiwawa. Mulungu anayang’ana dziko lapansi ndipo anaona kuti laipa. Anthu onse padziko lapansi ankachita zinthu zoipa.” Kodi Mulungu akanalola kuti anthu oipa achititse kuti anthu abwino ochepa amene anatsala padziko lapansi atheretu? Ayi. Yehova anaona kuti n’koyenera kuti abweretse chigumula padziko lonse kuti awononge anthu onse amene ankachita zachiwawa ndiponso makhalidwe oipa.
12. (a) Kodi Yehova ananeneratu chiyani zokhudza “mbadwa” ya Abulahamu? (b) N’chifukwa chiyani Aamori ankayenera kuphedwa?
12 N’chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika pamene Mulungu anawononga Akanani. Yehova ananena kuti mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa kudzera mwa munthu wina amene adzakhale mbadwa ya Abulahamu. Mogwirizana ndi cholinga chimenechi, Mulungu analamula kuti mbadwa za Abulahamu zidzapatsidwa dziko la Kanani limene munkakhala anthu otchedwa Aamori. Kodi panali chifukwa chomveka choti Mulungu achotse anthuwa m’dziko lawo? Yehova ananeneratu kuti anthuwo adzawachotsa m’dziko lawolo patapita zaka 400 komanso ‘tchimo la Aamori litafika poti alangidwe.’b (Genesis 12:1-3; 13:14, 15; 15:13, 16; 22:18) Pa zaka zimenezi, Aamori ankachita zinthu zoipa kwambiri. Anthu m’dziko la Kanani ankalambira mafano, kupha anthu ndiponso kuchita chiwerewere chonyansa kwambiri. (Ekisodo 23:24; 34:12, 13; Numeri 33:52) Anthu a m’dzikolo anafika mpaka popha ana awo powapereka nsembe pamoto. Kodi Mulungu yemwe ndi woyera akanalola kuti anthu ake azikhala pakati pa anthu oipa chonchi? Ayi. Iye anati: “Dzikolo ndi lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha zolakwa zake moti dzikolo lidzalavula anthu ake kunja.” (Levitiko 18:21-25) Komabe sikuti Yehova anapha anthu onse. Akanani omwe anasonyeza kuti anali ndi mtima wabwino, monga Rahabi ndi Agibiyoni, sanawaphe.—Yoswa 6:25; 9:3-27.
Amamenya Nkhondo Chifukwa cha Dzina Lake
13, 14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anaona kuti n’koyenera kuti ayeretse dzina lake? (b) Kodi Yehova anachita chiyani kuti dzina lake liyeretsedwe?
13 Chifukwa choti Yehova ndi woyera, dzina lakenso ndi loyera. (Levitiko 22:32) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Pamene Satana ananama zokhudza Yehova ndiponso ulamuliro wake, n’kuchititsa kuti Adamu ndi Hava agalukire, ananyoza kwambiri dzina la Mulungu komanso kuipitsa mbiri yake. Yehova sakanalekerera bodza limeneli ndiponso kugalukiraku. Iye anaona kuti n’koyenera kuti ayeretse dzina lake.—Yesaya 48:11.
14 Taganiziraninso za Aisiraeli. Pa nthawi yonse imene anali akapolo ku Iguputo, lonjezo la Mulungu kwa Abulahamu lakuti kudzera mwa mbadwa yake mabanja onse a padziko lapansi adzadalitsidwa linkaoneka ngati losatheka. Koma atawapulumutsa n’kuwapangitsa kukhala mtundu, Yehova anayeretsa dzina lake. N’chifukwa chake mneneri Danieli popemphera ananena kuti: “Inu Yehova Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m’dziko la Iguputo ndi dzanja lamphamvu n’kuchititsa kuti dzina lanu lidziwike bwino.”—Danieli 9:15.
15. N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Ayuda ku ukapolo ku Babulo?
15 N’zochititsa chidwi kuti Danieli anapemphera chonchi pa nthawi imene Ayuda ankafunikiranso kuti Yehova awapulumutse n’cholinga choti ayeretse dzina lake. Pa nthawiyi, Ayuda osakhulupirikawo anali akapolo ku Babulo. Mzinda wa Yerusalemu, omwe unali likulu lawo, n’kuti utawonongedwa. Danieli ankadziwa kuti ngati Ayuda atabwereranso kwawo ndiye kuti dzina la Yehova lidzalemekezedwa. Choncho iye anapemphera kuti: “Tikhululukireni, inu Yehova. Timvereni ndipo muchitepo kanthu, inu Yehova! Musazengereze inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu. Chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”—Danieli 9:18, 19.
Amamenyera Nkhondo Anthu Ake
16. Kodi Yehova akamayeretsa dzina lake ndiye kuti ndi wodzikonda ndipo amangoganizira za iyeyo? Fotokozani.
16 Kodi Yehova akamayeretsa dzina lake ndiye kuti ndi wodzikonda ndipo amangoganizira za iyeyo? Ayi, chifukwa akamachita zinthu mogwirizana ndi kuti iye ndi woyera komanso amakonda chilungamo, iye amateteza anthu ake. Taganizirani nkhani yopezeka m’chaputala 14 cha Genesis. M’chaputalachi timawerenga za mafumu 4 omwe anagwira Loti, mwana wa mchimwene wake wa Abulahamu, limodzi ndi banja lake. Mothandizidwa ndi Mulungu, Abulahamu anagonjetsa adaniwo ngakhale kuti anali amphamvu kuposa iyeyo. Nkhani yokhudza kupambana kumeneku inali yoyamba kulembedwa “m’buku la Nkhondo za Yehova.” M’buku limeneli munalembedwanso nkhondo zina zimene sizinatchulidwe m’Baibulo. (Numeri 21:14) Pambuyo pake, anthu a Mulungu anapambananso pa nkhondo zina zambiri.
17. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ankamenyera nkhondo Aisiraeli atalowa m’dziko la Kanani? Perekani zitsanzo.
17 Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’dziko la Kanani, Mose anawatsimikizira kuti: “Yehova Mulungu wanu adzakutsogolerani ndipo adzakumenyerani nkhondo, ngati mmene anachitira ku Iguputo inu mukuona.” (Deuteronomo 1:30; 20:1) Kuyambira ndi Yoswa, amene analowa m’malo mwa Mose, mpaka nthawi ya Oweruza ndi ya mafumu okhulupirika a Yuda, Yehova ankamenyeradi nkhondo anthu ake. Ankawathandiza kugonjetsa modabwitsa adani awo pa nkhondo zambiri.—Yoswa 10:1-14; Oweruza 4:12-17; 2 Samueli 5:17-21.
18. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kuti Yehova sanasinthe? (b) Kodi chidzachitike n’chiyani chidani chotchulidwa pa Genesis 3:15 chikadzafika pachimake?
18 Yehova sanasinthe. Komanso cholinga chake choti dzikoli lidzakhale Paradaiso wamtendere sichinasinthe. (Genesis 1:27, 28) Mpaka pano Mulungu amadana ndi zoipa. Koma amakonda kwambiri anthu ake ndipo posachedwapa adzachitapo kanthu kuti awathandize. (Salimo 11:7) Ndipotu chidani chotchulidwa pa Genesis 3:15 chidzafika poipa kwambiri posachedwapa pamene anthu a Mulungu adzaukiridwe. Kuti adzayeretse dzina lake ndiponso kuteteza anthu ake, Yehova adzakhalanso “msilikali wamphamvu.”—Zekariya 14:3; Chivumbulutso 16:14, 16.
19. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Mulungu akamagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga zimatithandiza kumuyandikira. (b) Kodi tiyenera kumva bwanji tikaganizira mfundo yoti Mulungu ndi wokonzeka kutimenyera nkhondo?
19 Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti chilombo cholusa chikufuna kugwira anthu a m’banja la munthu winawake. Ndiyeno bambo wa m’nyumbamo akulimbana nacho mpaka kuchipha. Kodi mukuganiza kuti mkazi ndi ana ake angayambe kumuopa chifukwa chakuti wapha chilombocho? Ayi, iwo angathokoze kuti bamboyo wasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena ndipo wawateteza. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu akagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga tiyenera kufuna kuti akhale mnzathu osati kumuopa. Tiyenera kumukonda kwambiri chifukwa amakhala wokonzeka kumenya nkhondo pofuna kutiteteza. Tiyeneranso kumulemekeza kwambiri chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zopanda malire. Choncho tingathe ‘kumachita utumiki wopatulika m’njira yovomerezeka, moopa Mulungu komanso mwaulemu kwambiri.’—Aheberi 12:28.
Yandikirani Mulungu Yemwe Ndi “Msilikali Wamphamvu”
20. Tikawerenga nkhani za m’Baibulo zokhudza nkhondo zimene Mulungu anamenya zomwe sitikuzimvetsa, kodi tiyenera kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
20 Si nthawi zonse pamene Baibulo limafotokoza mwatsatanetsatane zifukwa zimene zinachititsa Yehova kuti amenye nkhondo inayake. Koma nthawi zonse tingakhale otsimikiza kuti: Yehova sagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga mopanda chilungamo, mwachisawawa kapena mwankhanza. Nthawi zambiri, kuganizira nkhani yonse kapena pamene nkhaniyo inayambira kungatithandize kuti tiyambe kuona zinthu moyenera. (Miyambo 18:13) Ngakhale pamene sitikudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo, kuphunzira zambiri za Yehova ndiponso kuganizira mozama makhalidwe ake abwino kungatithandize kuti tichotse maganizo alionse okayikira. Tikamachita zimenezi, tidzakhala ndi chifukwa chomveka chotichititsa kuti tizikhulupirira Mulungu wathu, Yehova.—Yobu 34:12.
21. Ngakhale kuti nthawi zina Yehova amakhala “msilikali wamphamvu,” kodi iye amakonda chiyani?
21 Ngakhale kuti Yehova amakhala “msilikali wamphamvu” pakafunika, zimenezi sizikutanthauza kuti iye amakonda nkhondo. M’masomphenya a galeta lakumwamba, Ezekieli anaona Yehova ali wokonzeka kumenyana ndi adani ake. Komabe Ezekieli anaonanso Mulungu atazunguliridwa ndi utawaleza womwe ndi chizindikiro cha mtendere. (Genesis 9:13; Ezekieli 1:28; Chivumbulutso 4:3) Choncho n’zoonekeratu kuti Yehova ndi wofatsa ndiponso wokonda mtendere. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndi chikondi.” (1 Yohane 4:8) Yehova akamasonyeza khalidwe lake lililonse, amalisonyeza mogwirizana ndi makhalidwe ake ena. Kunena zoona, tili ndi mwayi waukulu kwambiri woti tikhoza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu wamphamvu ngati ameneyu, koma wachikondi.
a Malinga ndi zimene ananena Myuda wina wolemba mbiri yakale dzina lake Josephus, “magaleta 600, amuna 50,000 okwera pamahatchi komanso chigulu cha asilikali oyenda pansi okwana 200,000 ndi amene ankalondola” Aheberi.—Jewish Antiquities, II, 324 [xv, 3].
b Mawu akuti “Aamori” ayenera kuti akunena za anthu onse a m’dziko la Kanani.—Deuteronomo 1:6-8, 19-21, 27; Yoswa 24:15, 18.
-
-
Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 7
Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”
1, 2. Kodi Aisiraeli anakumana ndi mavuto otani pamene ankalowa m’dera la Sinai m’chaka cha 1513 B.C.E., nanga Yehova anawalimbikitsa bwanji?
AISIRAELI anakumana ndi mavuto pamene ankalowa m’dera la Sinai chakumayambiriro kwa chaka cha 1513 B.C.E. Ankayembekezera kuyenda ulendo woopsa wodutsa ‘m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, chokhala ndi njoka zapoizoni ndiponso zinkhanira.’ (Deuteronomo 8:15) Akanathanso kuukiridwa ndi anthu a mitundu ina omwe ankadana nawo. Yehova ndiye anachititsa kuti anthu ake akumane ndi zimenezi. Popeza kuti iye anali Mulungu wawo, kodi akanatha kuwateteza?
2 Zimene Yehova anawauza zinawalimbikitsa kwambiri. Iye anati: “Inu munaona nokha zimene ndinachitira Aiguputo, kuti ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga n’kukubweretsani kwa ine.” (Ekisodo 19:4) Yehova anakumbutsa anthu akewo kuti anawapulumutsa ku Iguputo ngati mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake n’kukawasiya kumalo otetezeka. Palinso zifukwa zina zomwe zimachititsa kuti “mapiko a chiwombankhanga” akhale chitsanzo chabwino chofotokoza mmene Yehova anatetezera anthu ake.
3. N’chifukwa chiyani “mapiko a chiwombankhanga” ndi chitsanzo chabwino chofotokoza mmene Yehova amatetezera anthu ake?
3 Sikuti chiwombankhanga chimangogwiritsa ntchito mapiko ake, omwe ndi aatali komanso amphamvu pouluka m’mwamba kwambiri, koma chimawagwiritsanso ntchito m’njira zina. Kukatentha kwambiri, chiwombankhanga chachikazi chimatambasula mapiko ake, omwe angakwane mamita awiri, kuti chipange mthunzi wotetezera ana ake kuti asapse ndi dzuwa. Nthawi zina chimafungatira ana ake m’mapiko powateteza ku mphepo yozizira. Yehova ankateteza mtundu wa Aisiraeli womwe unali watsopano, ngati mmene chiwombankhanga chimatetezera ana ake. Pamene anthu a Yehova anali m’chipululu, akanapitiriza kukhala otetezeka mumthunzi wa mapiko ake amphamvu ngati akanakhalabe okhulupirika. (Deuteronomo 32:9-11; Salimo 36:7) Koma kodi masiku ano Mulungu amatetezanso anthu ake?
Yehova Amalonjeza Kuti Aziteteza Atumiki Ake
4, 5. N’chifukwa chiyani sitingakayikire ngakhale pang’ono lonjezo la Mulungu lakuti adzateteza anthu ake?
4 Yehova amakwanitsa kuteteza atumiki ake. Iye ndi “Mulungu Wamphamvuyonse” ndipo dzina laudindo limeneli limasonyeza kuti ali ndi mphamvu zambiri moti palibe amene angamuletse kuchita zomwe akufuna. (Genesis 17:1) Mofanana ndi mafunde omwe sangaimitsidwe, palibe amene angaletse mphamvu za Yehova. Popeza iye amatha kuchita chilichonse chimene wafuna, tingafunse kuti, ‘Kodi Yehova ndi wofunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake poteteza anthu ake?’
5 Yankho ndi lakuti inde. Yehova amatitsimikizira kuti adzateteza anthu ake. Lemba la Salimo 46:1 limati: “Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.” Popeza Mulungu “sanganame,” sitingakayikire ngakhale pang’ono lonjezo lake lakuti adzateteza anthu ake. (Tito 1:2) Tiyeni tione mawu ena oyerekezera zinthu amene Yehova amagwiritsa ntchito pofotokoza mmene amatetezera anthu ake.
6, 7. (a) Kodi kale abusa ankateteza bwanji nkhosa zawo? (b) Kodi Baibulo limayerekezera zochita za Yehova ndi za ndani posonyeza kuti Yehovayo amafunitsitsa kuteteza nkhosa zake ndiponso kuzisamalira?
6 Yehova ndi M’busa wathu ndipo ife “ndife anthu ake komanso nkhosa zimene akuweta.” (Salimo 23:1; 100:3) Pali nyama zochepa zomwe zimafuna kuthandizidwa kwambiri ngati mmene zilili ndi nkhosa. Kale abusa ankafunika kukhala olimba mtima kuti ateteze nkhosa zawo kwa mikango, mimbulu, zimbalangondo komanso akuba. (1 Samueli 17:34, 35; Yohane 10:12, 13) Koma nthawi zina m’busa ankafunika kuchita zinthu mwachikondi poteteza nkhosa. Nkhosa ikaberekera kutali ndi khola, m’busa wachikondi ankayang’anira nkhosa yofunika kuthandizidwayo ndipo kenako ankanyamula kamwana kongobadwa kumeneko n’kupita nako kukhola.
“Adzawanyamulira pachifuwa pake”
7 Podziyerekezera ndi m’busa, Yehova amatitsimikizira kuti ndi wofunitsitsa kutiteteza. (Ezekieli 34:11-16) Kumbukirani zimene lemba la Yesaya 40:11 limafotokoza zokhudza Yehova. Lembali linafotokozedwa m’Mutu 2 wa bukuli ndipo limati: “Iye adzasamalira gulu la nkhosa zake ngati m’busa. Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” Kodi zimatheka bwanji kuti kamwana kankhosa kakhale “pachifuwa” cha m’busa, kapena kuti pachovala chake chakumtunda chomwe wachipinda? Kamwanako kangafike pamene pali m’busayo, mwinanso n’kumakhudza mwendo wake. Komabe m’busayo ndi amene amayenera kuwerama n’kukanyamula ndiponso kukaika mosamala pachifuwa chake pomwe kangakhale motetezeka. Zimenezitu zikusonyeza bwino kuti M’busa wathu wamkulu amafunitsitsa kutiteteza.
8. (a) Ndi ndani amene Mulungu amalonjeza kuti aziwateteza, ndipo lemba la Miyambo 18:10 likusonyeza bwanji mfundo imeneyi? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizitetezedwa ndi dzina la Mulungu?
8 Koma Mulungu amalonjeza kuti aziteteza anthu okhawo amene amafuna kukhala naye pa ubwenzi. Lemba la Miyambo 18:10 limati: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.” Kale, nthawi zina anthu ankamanga nsanja m’chipululu kuti azithawiramo. Koma munthu yemwe moyo wake uli pangoziyo ndi amene ankafunika kuthamangira kunsanjako kuti apulumuke. N’chimodzimodzinso ndi kutetezedwa ndi dzina la Mulungu. Dzina la Mulungu lilibe mphamvu zamatsenga, choncho kungolitchula mobwerezabwereza si kumene kungatiteteze. M’malomwake, timafunika kudziwa ndiponso kukhulupirira Mwiniwake wa dzina limeneli n’kumayesetsa kutsatira mfundo zake pa moyo wathu. Yehova anatikomera mtima kwambiri potitsimikizira kuti tikamamukhulupirira, azititeteza mofanana ndi mmene nsanja imatetezera.
“Mulungu Wathu . . . Akhoza Kutipulumutsa”
9. Kuwonjezera pa kulonjeza kuti aziteteza anthu ake, kodi Yehova wachitanso chiyani?
9 Sikuti Yehova amangolonjeza kuteteza anthu ake. M’Baibulo muli nkhani zimene zimasonyeza kuti iye ankachita zodabwitsa posonyeza kuti akhoza kuwateteza. Mwachitsanzo, nthawi zambiri Yehova ankagwiritsa ntchito “dzanja” lake lamphamvu poteteza Aisiraeli kwa adani awo amphamvu. (Ekisodo 7:4) Komabe, Yehova ankagwiritsanso ntchito mphamvu zake zoteteza pothandiza munthu aliyense payekha.
10, 11. Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zimasonyeza mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake poteteza anthu ena?
10 Anyamata atatu, Shadireki, Misheki ndi Abedinego, omwe anali Aheberi, atakana kugwadira fano lagolide la Mfumu Nebukadinezara, mfumuyo inakwiya kwambiri ndipo inawaopseza kuti iwaponya m’ng’anjo yotentha kwambiri. Nebukadinezara, yemwe anali mfumu yamphamvu kwambiri padziko lapansi, analankhula monyoza kuti: “Ndi mulungu uti amene angakupulumutseni m’manja mwanga?” (Danieli 3:15) Anyamata atatuwo ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu wawo ali ndi mphamvu zoti atha kuwateteza, koma sanaganize kuti iye achita zimenezo pa nthawiyo. Choncho anayankha kuti: “Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa.” (Danieli 3:17) Ndi zimenedi zinachitika, chifukwa ng’anjo yotenthayo, ngakhale kuti anaisonkhezera kuwirikiza ka 7 kuposa nthawi zonse, sinalepheretse kuti Mulungu wawo wamphamvu zonse awapulumutse. Iye anawateteza ndipo mfumuyo inakakamizika kuvomereza kuti: “Palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa anthu ake mofanana ndi ameneyu.”—Danieli 3:29.
11 Yehova anasonyezanso mochititsa chidwi mphamvu zake zoteteza pamene anasamutsa moyo wa Mwana wake wobadwa yekha n’kuuika m’mimba mwa namwali wa Chiyuda dzina lake Mariya. Mngelo anauza Mariya kuti ‘adzakhala woyembekezera n’kubereka mwana wamwamuna.’ Mngeloyo anafotokoza kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba.” (Luka 1:31, 35) Pa nthawiyi Mwana wa Mulungu ankafunikira kwambiri kutetezedwa. Popeza kuti mayi ake sanali angwiro, kodi zimenezi zikanachititsa kuti mwanayo abadwe wochimwa? Kodi Satana akanavulaza kapena kupha mwanayo asanabadwe? Ayi, zimenezi zinali zosatheka. Yehova anateteza Mwana wake amene anali m’mimba mwa Mariya kungoyambira pamene Mariyayo anakhala ndi pakati, moti panalibe chilichonse kapena aliyense amene akanamuvulaza. Yehova anapitiriza kuteteza Yesu pa nthawi imene anali mnyamata. (Mateyu 2:1-15) Mulungu anapitirizabe kuteteza Mwana wake mpaka pamene inafika nthawi yoti apereke moyo wake.
12. N’chifukwa chiyani kale Yehova ankateteza anthu ena modabwitsa?
12 N’chifukwa chiyani Yehova ankateteza anthu ena modabwitsa chonchi? Nthawi zambiri Yehova ankateteza anthu ena n’cholinga choti ateteze chinthu chofunika kwambiri, chomwe ndi kukwaniritsidwa kwa cholinga chake. Mwachitsanzo, zinali zofunika kwambiri kuti Yesu ali wakhanda apulumuke kuti cholinga cha Mulungu, chomwe pamapeto pake chidzathandiza anthu onse, chikwaniritsidwe. Nkhani zambiri zimene zimafotokoza mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake zoteteza, ndi mbali ya Malemba ouziridwa amene ‘analembedwa kuti atilangize. Malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa n’cholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.’ (Aroma 15:4) Zitsanzo zimenezi zimatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu wathu wamphamvu zonse. Koma kodi tingayembekezere kuti Mulungu azititeteza bwanji masiku ano?
Kodi Kutetezedwa ndi Mulungu Sikutanthauza Chiyani?
13. Kodi Yehova amafunika kutiteteza modabwitsa nthawi zonse? Fotokozani.
13 Lonjezo la Mulungu loti aziteteza anthu ake silitanthauza kuti Yehova amafunika kutiteteza modabwitsa nthawi zonse. Mulungu wathu sananene kuti tizikhala moyo wopanda mavuto m’dziko loipali. Atumiki a Yehova ambiri amakumana ndi mavuto aakulu monga umphawi, nkhondo, matenda ndiponso imfa. Yesu anauza ophunzira ake mosapita m’mbali kuti ena a iwo adzaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. N’chifukwa chake iye anatsindika mfundo yakuti tifunika kupirira mpaka mapeto. (Mateyu 24:9, 13) Yehova akanati nthawi zonse azigwiritsa ntchito mphamvu zake kupulumutsa atumiki ake modabwitsa, bwenzi Satana akumunyoza ndiponso kunena kuti timatumikira Mulungu osati chifukwa choti timamukonda koma chifukwa choti amatiteteza.—Yobu 1:9, 10.
14. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova sateteza atumiki ake onse mofanana?
14 Ngakhalenso kale, Yehova sankagwiritsa ntchito mphamvu zake poteteza mtumiki wake aliyense kuti asaphedwe. Mwachitsanzo, Herode anapha mtumwi Yakobo cha m’ma 44 C.E. koma pasanapite nthawi yaitali, Petulo anapulumutsidwa “m’manja mwa Herode” yemweyo. (Machitidwe 12:1-11) Ndipo Yohane, mchimwene wake wa Yakobo, anakhala ndi moyo nthawi yaitali kuposa Petulo ndi Yakobo. Choncho n’zoonekeratu kuti sitingayembekezere Mulungu wathu kuti aziteteza atumiki ake onse mofanana. Ndiponso “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka” zimagwera tonsefe. (Mlaliki 9:11) Ndiyeno kodi Yehova amatiteteza bwanji masiku ano?
Yehova Amateteza Moyo Wathu
15, 16. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amateteza atumiki ake ngati gulu? (b) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova aziteteza atumiki ake panopa komanso adzawateteza pa “chisautso chachikulu”?
15 Choyamba, tiyeni tiganizire mmene Yehova amatetezera moyo wathu. Atumiki a Yehovafe tingayembekezere kuti iye azititeteza ngati gulu. Akanakhala kuti sachita zimenezi, bwenzi Satana akungotipha. Taganizirani izi: Satana, yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli,” amafunitsitsa kuthetseratu kulambira koona. (Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:17) Maboma ena amphamvu kwambiri akhala akuletsa ntchito yathu yolalikira ndiponso kuyesetsa kuti athetseretu gulu lathu. Koma anthu a Yehova amakhalabe olimba komanso amapitiriza kulalikira. N’chifukwa chiyani maboma amphamvu alephera kuletsa ntchito ya Akhristu omwe amaoneka kuti ndi ochepa komanso opanda chitetezo? N’chifukwa chakuti Yehova amatiteteza ndi mapiko ake amphamvu.—Salimo 17:7, 8.
16 Nanga kodi Yehova adzatiteteza pa “chisautso chachikulu” chimene chikubwerachi? Sitikufunika kudzachita mantha Mulungu akamadzawononga anthu oipa. Pajatu “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero. Koma anthu osalungama amawasunga kuti adzawawononge pa tsiku lopereka chiweruzo.” (Chivumbulutso 7:14; 2 Petulo 2:9) Panopa, nthawi zonse tizikhala otsimikiza za zinthu ziwiri izi: Choyamba, Yehova sadzalola kuti Satana aphe atumiki onse a Mulungu okhulupirika. Chachiwiri, adzapereka mphoto ya moyo wosatha kwa anthu okhulupirika m’dziko latsopano lolungama ndipo amene anamwalira adzawaukitsa. Komanso anthu amene akumwalira panopa ndi otetezeka chifukwa Mulungu akuwakumbukira.—Yohane 5:28, 29.
17. Kodi Yehova amatiteteza bwanji pogwiritsa ntchito Mawu ake?
17 Ngakhale panopa Yehova amatiteteza pogwiritsa ntchito “mawu” ake. Mawu akewa ndi amoyo ndipo ali ndi mphamvu yothandiza munthu kusintha n’kumakhala wosangalala. (Aheberi 4:12) Tikamatsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu, timatetezeka ku zinthu zina zomwe zingawononge moyo wathu. Lemba la Yesaya 48:17 limati: “Ine Yehova . . . ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.” N’zosakayikitsa kuti kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu kungachititse kuti tikhale ndi thanzi labwino komanso moyo wautali. Mwachitsanzo, chifukwa chotsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizipewa chiwerewere ndiponso tiziyesetsa kukhala oyera, timapewa makhalidwe odetsa komanso zizolowezi zoipa zimene zimawononga moyo wa anthu ambiri osaopa Mulungu. (Machitidwe 15:29; 2 Akorinto 7:1) Tikuthokozatu kwambiri kuti Mawu a Mulungu amatiteteza.
Yehova Amatiteteza Mwauzimu
18. Kodi Yehova amatiteteza bwanji mwauzimu?
18 Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amatiteteza mwauzimu. Mulungu wathu wachikondi amatipatsa chilichonse chimene tingafunikire kuti tizipirira mayesero komanso kuti tisawononge ubwenzi wathu ndi iye. Choncho Yehova amatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo panopa komanso mpaka kalekale. Taganizirani zinthu zina zimene Mulungu amatipatsa kuti tikhalebe anzake.
19. Kodi mzimu wa Yehova ungatithandize bwanji kupirira mayesero alionse amene tingakumane nawo?
19 Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Tikapanikizika ndi mavuto, kupemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kungathandize kuti tiyambe kumvako bwino. (Afilipi 4:6, 7) Iye sangatichotsere mavuto athuwo modabwitsa, koma poyankha pemphero lathu lochokera pansi pamtima, angatipatse nzeru kuti tidziwe zoyenera kuchita. (Yakobo 1:5, 6) Kuwonjezera pamenepo, Yehova amapereka mzimu woyera kwa anthu amene amamupempha. (Luka 11:13) Mzimuwu, womwe ndi wamphamvu kwambiri, ungatithandize kupirira mayesero alionse kapenanso vuto lililonse limene tingakumane nalo. Ungatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tipirire mpaka pamene Yehova adzachotse mavuto onse m’dziko latsopano limene lili pafupi kwambiri.—2 Akorinto 4:7.
20. Kodi Yehova amatiteteza bwanji pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu?
20 Nthawi zina, Yehova amatiteteza pogwiritsa ntchito abale ndi alongo athu. Iye wasonkhanitsa anthu ake kuti akhale “gulu la abale” la padziko lonse. (Yohane 6:44; 1 Petulo 2:17) Abale akamasonyezana chikondi, timaona umboni wakuti mzimu wa Mulungu umathandiza anthu kuchita zabwino. Mzimu umenewo umatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso amtengo wapatali monga chikondi, kukoma mtima ndiponso ubwino. (Agalatiya 5:22, 23) Choncho ngati takumana ndi vuto linalake ndipo Mkhristu mnzathu watipatsa malangizo othandiza kapena watiuza mawu olimbikitsa amene timafunikira kwambiri, tiyenera kuthokoza Yehova chifukwa chotithandiza pogwiritsa ntchito Mkhristuyo.
21. (a) Kodi ndi chakudya chauzimu cha pa nthawi yoyenera chiti chomwe Yehova amatipatsa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru”? (b) Kodi inuyo mwapindula bwanji ndi zinthu zimene Yehova amatipatsa pofuna kutiteteza mwauzimu?
21 Palinso chinthu china chimene Yehova amatipatsa pofuna kutiteteza, chomwe ndi chakudya chauzimu cha pa nthawi yoyenera. Kuti tizipeza mphamvu kuchokera m’Mawu ake, Yehova wauza “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu. Kapoloyu amagwiritsa ntchito mabuku, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, webusaiti yathu ya jw.org ndiponso misonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo kuti azitipatsa “chakudya pa nthawi yoyenera.” Amatipatsa zimene timafunikira komanso pa nthawi yomwe zikufunikira. (Mateyu 24:45) Kodi nthawi ina pamisonkhano yampingo munamvapo mfundo inayake mundemanga, munkhani kapena m’pemphero, imene inakulimbikitsani komanso kukupatsani mphamvu zomwe munkafunikira? Kapena kodi moyo wanu unasintha chifukwa cha nkhani inayake imene munawerenga m’magazini yathu ina? Kumbukirani kuti Yehova amatipatsa zinthu zonsezi kuti azititeteza mwauzimu.
22. Kodi nthawi zonse Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake, nanga n’chifukwa chiyani akamachita zimenezi amakhala kuti akutithandiza?
22 Kunena zoona, Yehova amateteza “onse amene amathawira kwa iye.” (Salimo 18:30) Tikudziwa kuti panopa sagwiritsa ntchito mphamvu zake potiteteza ku mavuto onse amene tingakumane nawo. Komabe, nthawi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zake zoteteza poonetsetsa kuti cholinga chake chikukwaniritsidwa. Ndipo zimene amachitazi pamapeto pake zidzathandiza atumiki ake. Tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kumachitabe zinthu zomwe zingachititse kuti azitikonda, iye adzatipatsa moyo wosatha. Popeza tikuyembekezera zimenezi, tingamaone mavuto alionse amene tikukumana nawo m’dzikoli kuti ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.”—2 Akorinto 4:17.
-
-
Mphamvu Zobwezeretsa—Yehova ‘Akupanga Zinthu Zonse Kuti Zikhale Zatsopano’Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 8
Mphamvu Zobwezeretsa—Yehova ‘Akupanga Zinthu Zonse Kuti Zikhale Zatsopano’
1, 2. Kodi anthu masiku ano amataya zinthu ziti, nanga zimenezi zimatikhudza bwanji?
TIYEREKEZE kuti mwana wataya kapena wawononga chidole chake chimene amachikonda kwambiri ndipo akulira momvetsa chisoni. Mayi kapena bambo ake nawonso akumva chisoni kumuona akulira choncho. Koma kenako bambo kapena mayi akewo apeza kapenanso kukonza chidolecho ndipo mwanayo akusangalala kwambiri. Makolowo sangavutike kupeza chidolecho kapena kuchikonza. Koma kwa mwanayo, zimene makolowo achita n’zodabwitsa kwambiri. Tsopano iye azithanso kuseweretsa chidolecho ngakhale kuti poyamba amaganiza kuti sadzakhala nachonso.
2 Yehova, yemwe ndi Bambo wabwino kwambiri, ali ndi mphamvu zobwezeretsa zinthu zimene ana ake apadziko lapansi angaone ngati sizingatheke kuzibwezeretsa. Koma apa sikuti tikunena zidole. Mu “nthawi yapadera komanso yovuta” ino, timataya zinthu zofunika kwambiri. (2 Timoteyo 3:1-5) Nthawi iliyonse anthu akhoza kutaya nyumba kapena katundu wawo, ntchito ikhoza kuwathera komanso akhoza kuyamba kudwala. Timadanso nkhawa tikaganizira kuwonongedwa kwa zinthu zachilengedwe komwe kukuchititsa kuti mitundu yambiri ya zamoyo itheretu. Koma palibe chimene chimatiwawa kwambiri kuposa imfa ya munthu yemwe timam’konda. Timamva kuti tataya chinthu chofunika kwambiri ndipo timasowa mtengo wogwira.—2 Samueli 18:33.
3. Kodi ndi mfundo yolimbikitsa iti yomwe ili pa Machitidwe 3:21, nanga Yehova adzagwiritsa ntchito chiyani kuti akwaniritse zimenezi?
3 Choncho n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa zinthu. M’mutuwu tiona kuti pali zinthu zambiri zokhudza ana ake apadziko lapansi zimene Mulungu angabwezeretse ndiponso zomwe adzabwezeretse. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti Yehova akufuna ‘kudzabwezeretsa zinthu zonse.’ (Machitidwe 3:21) Kuti akwaniritse zimenezi, iye adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya, womwe wolamulira wake ndi Mwana wake, Yesu Khristu. Umboni umasonyeza kuti Ufumu umenewu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914.a (Mateyu 24:3-14) Koma kodi Yehova adzabwezeretsa zinthu ziti? Tiyeni tikambirane chinthu china chimene wabwezeretsa kale m’nthawi yathu ino komanso zina zomwe adzabwezeretse m’tsogolo, zimene zidzakhudze anthu onse. Zinthu zonsezi ndi zikuluzikulu.
Kubwezeretsa Kulambira Koona
4, 5. N’chiyani chinachitikira anthu a Mulungu mu 607 B.C.E., ndipo kodi Yehova anawalonjeza chiyani?
4 Chinthu china chimene Yehova wabwezeretsa kale ndi kulambira koona. Kuti timvetse bwino zimenezi, tiyeni tikambirane mwachidule mbiri ya ufumu wa Yuda. Kuchita zimenezi kutithandiza kumvetsa bwino mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zobwezeretsa.—Aroma 15:4.
5 Taganizirani mmene Ayuda okhulupirika anamvera mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E. Mzinda umene ankaukonda kwambiriwu unagumulidwa ndipo mpanda wake unagwetsedwa. Koma chomvetsa chisoni kwambiri chinali chakuti kachisi wokongola amene Solomo anamanga anawonongedwanso. Kachisiyu anali likulu la kulambira koona padziko lonse. (Salimo 79:1) Anthu amene anapulumuka anawatenga kupita nawo ku ukapolo ku Babulo ndipo dziko lawo analisiya lili bwinja moti nyama zakutchire zinayamba kukhalamo. (Yeremiya 9:11) Mwina Ayuda ankaona kuti palibenso chiyembekezo. (Salimo 137:1) Koma Yehova, yemwe anali atanena kale kuti mzindawu udzawonongedwa, analonjeza kuti adzabwezeretsa zinthu.
6-8. (a) Kodi ndi nkhani iti imene aneneri a Chiheberi anailemba mobwerezabwereza, nanga maulosi amenewa anakwaniritsidwa bwanji koyamba? (b) Kodi maulosi amenewa akukwaniritsidwa bwanji munthawi yathu ino?
6 Ndipotu aneneri a Chiheberi analemba mobwerezabwereza nkhani yokhudza kubwezeretsa zinthu.b Kudzera mwa aneneriwa, Yehova analonjeza kuti dzikolo lidzabwereranso mwakale, muzidzakhalanso anthu, lidzakhala lachonde ndiponso lotetezeka ku nyama zolusa ndi adani. Iye ananena kuti dziko lawolo lidzakhala lokongola kwambiri. (Yesaya 65:25; Ezekieli 34:25; 36:35) Chofunika kwambiri chinali choti kulambira koona kudzayambiranso ndipo kachisi adzamangidwanso. (Mika 4:1-5) Maulosiwa anathandiza Ayuda kukhala ndi chiyembekezo komanso kupirira ukapolo wawo kwa zaka 70 ku Babulo.
7 Kenako inadzafika nthawi yoti Yehova abwezeretse zinthu. Ayuda anamasulidwa ku Babulo ndipo anabwerera ku Yerusalemu n’kukamanganso kachisi wa Yehova. (Ezara 1:1, 2) Kulambira kwawo kukakhala koyera, Yehova ankawadalitsa, kuchititsa kuti dziko lawo likhale lachonde komanso ankawapatsa zinthu zina zambiri. Ankawateteza kwa adani awo ndiponso nyama zolusa zomwe zinakhala m’dzikolo kwa zaka zambiri. Iwo ayenera kuti anasangalala kwambiri chifukwa cha mphamvu zobwezeretsa za Yehova. Komabe zinthu zimenezi zinali kukwaniritsidwa koyamba ndiponso kochepa kwambiri kwa maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa zinthu. Kukwaniritsidwa kwakukulu kunali koti kudzachitika munthawi yathu ino, yomwe ndi “masiku otsiriza,” pamene mbadwa ya Mfumu Davide imene Mulungu analonjeza kalekale inayamba kulamulira.—Yesaya 2:2-4; 9:6, 7.
8 Yesu atangoyamba kulamulira mu Ufumu wakumwamba mu 1914, anayamba kuthandiza anthu okhulupirika padzikoli kuti ayambirenso kulambira Mulungu moyenera. Mofanana ndi zomwe Koresi, mfumu ya Perisiya anachita pomasula Ayuda ku Babulo mu 537 B.C.E., Yesu anamasulanso Ayuda auzimu, omwe ndi otsatira ake. Anawamasula m’Babulo Wamkulu yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga. (Aroma 2:29; Chivumbulutso 18:1-5) Kungochokera mu 1919, Akhristu oona anayambiranso kulambira Yehova m’njira imene iye amafuna. (Malaki 3:1-5) Kuyambira nthawi imeneyo, anthu a Yehova akhala akumulambira m’kachisi wake wauzimu woyeretsedwa, yemwe amaimira dongosolo la kulambira koyera limene Mulungu anakhazikitsa. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika kwa ife masiku ano?
N’chifukwa Chiyani Kubwezeretsa Kulambira Koona Kuli Kofunika?
9. Atumwi onse atafa, kodi matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu anachita zotani pa nkhani yolambira Mulungu, koma kodi Yehova wachita chiyani m’nthawi yathu ino?
9 Taganizirani zimene zakhala zikuchitika. Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankasangalala ndi madalitso ambiri auzimu. Koma Yesu ndi atumwi analosera kuti anthu adzasiya kulambira Mulungu m’njira yoyenera. (Mateyu 13:24-30; Machitidwe 20:29, 30) Atumwi onse atafa, panayambika matchalitchi omwe amati ndi a Chikhristu. Atsogoleri a matchalitchiwa anatengera ziphunzitso ndi miyambo yachikunja. Anachititsanso kuti anthu aziona ngati n’zosatheka kupemphera kwa Mulungu. Iwo ankauza anthu kuti Mulungu ndi Utatu wosamvetsetseka. Ankawaphunzitsanso kuti aziulula machimo awo kwa ansembe komanso azipemphera kwa Mariya ndi kwa “oyera mtima” osiyanasiyana m’malo mopemphera kwa Yehova. Ndiye popeza kuti ziphunzitso zabodzazi zakhala zilipo kwa zaka zambiri, kodi Yehova wachita chiyani? Ngakhale kuti panopa padzikoli pali mfundo zambiri zabodza zachipembedzo komanso anthu ali ndi makhalidwe osonyeza kuti saopa Mulungu, iye wabwezeretsa kulambira koona. Choncho sikungakhale kukokomeza kunena kuti kubwezeretsa kulambira koonaku ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zomwe zachitika m’nthawi yathu ino.
10, 11. (a) Kodi m’paradaiso wauzimu muli mbali ziwiri ziti, nanga mungatani kuti inunso mukhale m’paradaisoyu? (b) Kodi Yehova wasonkhanitsa anthu otani kuti akhale m’paradaiso wauzimu, nanga anthuwa adzakhala ndi mwayi woona chiyani?
10 Choncho masiku ano Akhristu oona ali m’paradaiso wauzimu yemwe akupitiriza kukula komanso kukongola. Kodi m’paradaiso ameneyu muli zinthu ziti? Muli mbali ziwiri zikuluzikulu. Mbali yoyamba ndi kulambira Yehova Mulungu woona movomerezeka. Iye watithandiza kuti tizimulambira popanda kusocheretsedwa ndi mabodza achipembedzo. Komanso amatipatsa chakudya chauzimu. Zimenezi zimatithandiza kuti tiziphunzira za Atate wathu wakumwamba, tizichita zinthu zomusangalatsa ndiponso kuti akhale mnzathu. (Yohane 4:24) Mbali yachiwiri ya paradaiso wauzimu ikukhudza anthu. Mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera, “m’masiku otsiriza” ano Yehova waphunzitsa anthu ake zimene angachite kuti azikhala mwamtendere. Watiphunzitsa kuti tisamamenye nawo nkhondo. Ngakhale kuti si ife angwiro, amatithandiza kuvala ‘umunthu watsopano.’ Tikamayesetsa kuchita zabwino, amatidalitsa potipatsa mzimu wake woyera umene umatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. (Aefeso 4:22-24; Agalatiya 5:22, 23) Mukamachita zinthu mogwirizana ndi mzimu wa Mulungu, mumasonyeza kuti mulidi m’paradaiso wauzimu.
11 Yehova wasonkhanitsa m’paradaiso wauzimu ameneyu anthu amene amawakonda. Anthuwa amamukonda, amakonda mtendere ndiponso “amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Anthu amenewa ndi omwe adzakhale ndi mwayi woona kubwezeretsa kwina kwapadera. Kubwezeretsa kumeneku kudzakhudza anthu onse pa nthawiyo ndiponso dziko lonse lapansi.
“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga Ndi Zatsopano”
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani maulosi okhudza kubwezeretsa zinthu akuyenera kukwaniritsidwa m’njira inanso? (b) Kodi m’munda wa Edeni Yehova anasonyeza kuti ali ndi cholinga chotani chokhudza dziko lapansi, nanga kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji kukhala ndi chiyembekezo?
12 Maulosi ambiri onena za kubwezeretsa zinthu sikuti amangonena za kubwezeretsa kwauzimu kokha. Mwachitsanzo, Yesaya analemba kuti nthawi ina odwala, olumala komanso amene ali ndi vuto losaona ndiponso losamva adzachiritsidwa ndipo ngakhale imfa sidzakhalaponso. (Yesaya 25:8; 35:1-7) Malonjezo amenewa sanakwaniritsidwe ku Isiraeli wakale. Ndipo ngakhale kuti m’nthawi yathu ino taona maulosiwa akukwaniritsidwa m’paradaiso wauzimu, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti m’tsogolomu adzakwaniritsidwa padziko lonse. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
13 M’munda wa Edeni, Yehova anasonyeza bwino cholinga chake chokhudza dziko lapansi. Iye ankafuna kuti padzikoli pakhale anthu osangalala, athanzi ndiponso ogwirizana. Ankafuna kuti anthu azisamalira zinyama komanso dziko lapansili mpaka lonse likhale paradaiso. (Genesis 1:28) Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi mmene zinthu zilili panopa. Komabe tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti zofuna za Yehova sizilephereka. (Yesaya 55:10, 11) Yesu, yemwe ndi Mesiya komanso Mfumu yosankhidwa ndi Yehova, ndi amene adzabweretse Paradaiso ameneyu padziko lonse lapansi.—Luka 23:43.
14, 15. (a) Kodi Yehova adzapanga bwanji ‘zinthu zonse kuti zikhale zatsopano’? (b) Kodi moyo udzakhala wotani m’Paradaiso, nanga inuyo n’chiyani chomwe mukuyembekezera mwachidwi?
14 Mukuganiza kuti mudzamva bwanji mukadzaona dziko lonseli lili Paradaiso? Ponena za nthawi imeneyo, Yehova ananena kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Taganizirani tanthauzo la zimenezi. Yehova akadzamaliza kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuwononga dziko loipali, chimene chidzatsale ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Izi zikutanthauza kuti boma latsopano lakumwamba lizidzalamulira anthu padziko lapansi omwe amakonda Yehova n’kumachita zimene iye amafuna. (2 Petulo 3:13) Satana ndi ziwanda zake adzaletsedwa kuchita chilichonse. (Chivumbulutso 20:3) Ndiyeno kwa nthawi yoyamba pambuyo pa zaka masauzande ambiri, anthu sazidzasokonezedwanso ndi zochita za Satana ndiponso ziwanda zake. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri.
15 Pa nthawi imeneyo tizidzasamalira dziko lokongolali ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Dzikoli lili ndi mphamvu zotha kubwezeretsa zinthu zachilengedwe. Mwachitsanzo, nyanja ndi mitsinje zomwe zaipitsidwa zikhoza kudzikonza ngati chomwe chikuchititsa kuti ziwonongekecho chitachotsedwa. Malo amene anawonongeka chifukwa cha nkhondo akhoza kukhalanso bwinobwino ngati nkhondozo zitatha. Tidzasangalalatu kwambiri kugwira nawo ntchito yokonza dziko lonse lapansi kuti likhale Paradaiso ngati mmene unalili munda wa Edeni, ndipo lidzakhala ndi zomera ndiponso nyama zamitundumitundu. M’malo momawononga mwadala nyama ndi zomera, anthu sazidzawononga zinthu zimenezi. Ngakhalenso ana sazidzaopa nyama zakutchire.—Yesaya 9:6, 7; 11:1-9.
16. Kodi ndi kubwezeretsa kuti m’Paradaiso kumene kudzakhudze munthu aliyense wokhulupirika?
16 Yehova adzabwezeretsanso zinthu kwa munthu aliyense payekha. Padziko lonse, anthu onse amene adzapulumuke pa Aramagedo adzachiritsidwa modabwitsa. Mofanana ndi mmene anachitira ali padziko lapansi, Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa ndipo adzachiritsa anthu olumala, odwala komanso amene ali ndi vuto losaona ndi losamva. (Mateyu 15:30) Achikulire adzasangalala kukhalanso achinyamata amphamvu komanso athanzi. (Yobu 33:25) Makwinya adzatha ndipo manja, miyendo ndiponso minofu izidzagwiranso ntchito bwino ngati kale. Anthu onse okhulupirika adzazindikira kuti mavuto amene amabwera chifukwa choti ndife ochimwa komanso siife angwiro akutha. Tidzathokoza kwambiri Yehova Mulungu chifukwa cha mphamvu zake zazikulu zobwezeretsa zinthu. Tsopano tiyeni tikambirane chinthu china chosangalatsa kwambiri chimene chidzachitike pa nthawi yobwezeretsa zinthu imeneyi.
Kubwezeretsa Moyo kwa Anthu Amene Anamwalira
17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula Asaduki? (b) N’chiyani chinachititsa Eliya kupempha Yehova kuti aukitse munthu?
17 Munthawi ya atumwi, atsogoleri achipembedzo ena otchedwa Asaduki sankakhulupirira zoti akufa adzaukitsidwa. Yesu anawadzudzula kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.” (Mateyu 22:29) Malemba amasonyezadi kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kubwezeretsa moyo kwa anthu amene anamwalira. Tiyeni tione zitsanzo pa nkhaniyi.
18 Taganizirani zimene zinachitika munthawi ya Eliya. Mayi wamasiye anali atanyamula mwana wake wamwamuna mmodzi yekhayo yemwe anali atamwalira. Mneneri Eliya, yemwe anali mlendo kunyumba kwa mayiyo kwa nthawi ndithu, ayenera kuti zinamuvuta kukhulupirira. Poyamba, iye anathandiza kupulumutsa mwanayu kuti asafe ndi njala. N’kutheka kuti Eliya ankagwirizana kwambiri ndi mnyamatayo. Mayi ake a mwanayo anali ndi chisoni kwambiri. Mwamuna wawo atamwalira, ankatonthozedwa akaona mnyamatayu. Komanso mwina ankaganiza kuti mwana wawoyo ndi amene adzawasamalire akadzakalamba. Chifukwa cha chisoni, mayiwa anayamba kuganiza kuti akulangidwa chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyomo. Eliya anakhudzidwa kwambiri ndi zimenezi. Choncho anatenga mwanayo kuchokera m’manja mwa mayi ake n’kupita naye kuchipinda kwake ndipo anapempha Yehova Mulungu kuti amuukitse.—1 Mafumu 17:8-21.
19, 20. (a) Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa anthu amene amwalira, ndipo n’chiyani chinachititsa kuti azikhulupirira zimenezi? (b) Kodi Yehova anadalitsa bwanji Eliya chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro?
19 Eliya sanali woyamba kukhulupirira zoti munthu amene wamwalira akhoza kuukitsidwa. Zaka zambiri m’mbuyomo, Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa akufa, ndipo iye anali ndi zifukwa zomveka. Abulahamu ali ndi zaka 100 ndipo Sara ali ndi zaka 90, Yehova anabwezeretsa mphamvu zawo zobereka, ndipo Sara anabereka mwana wamwamuna. (Genesis 17:17; 21:2, 3) Kenako mnyamatayo ali wamkulu, Yehova anauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wakeyo. Abulahamu anasonyeza kuti ankakhulupirira zoti Yehova angachititse kuti Isaki, mwana wake wokondedwayo, akhalenso ndi moyo. (Aheberi 11:17-19) N’chifukwa chake pamene ankapita kuphiri kuti akapereke nsembe Isaki, anatsimikizira antchito ake kuti iye ndi mwana wakeyo abwerera limodzi.—Genesis 22:5.
“Mwana wanu uja tsopano ali moyo.”
20 Yehova anapulumutsa Isaki, choncho sipanafunike kuti amuukitse. Koma pa nkhani ya Eliya, mwana wa mayi wamasiye uja nali atamwalira kale, koma panali pasanathe nthawi yaitali. Yehova anadalitsa Eliya chifukwa cha chikhulupiriro chake poukitsa mwanayo. Kenako Eliya anapereka mwanayo kwa amayi ake ndipo ananena mawu osaiwalika akuti: “Mwana wanu uja tsopano ali moyo.”—1 Mafumu 17:22-24.
21, 22. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo limafotokoza nkhani za anthu amene anaukitsidwa? (b) Kodi ndi anthu ambiri bwanji amene adzaukitsidwe m’Paradaiso, nanga ndani adzawaukitse?
21 Imeneyi ndi nkhani yoyamba m’Baibulo yomwe imasonyeza kuti Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu zake poukitsa munthu. Patapita nthawi, Yehova anapatsanso mphamvu Elisa, Yesu, Paulo ndiponso Petulo kuti aukitse anthu. N’zoona kuti anthu amene anaukitsidwawo kenako anamwaliranso. Komabe nkhani za m’Baibulo zimenezi zimatithandiza kudziwa zimene zidzachitike m’tsogolo.
22 M’Paradaiso, Yesu adzakwaniritsa udindo wake monga “kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Adzaukitsa anthu mamiliyoni osawerengeka n’kuwapatsa mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. (Yohane 5:28, 29) Taganizirani mmene tidzasangalalire tikadzakumana komanso kuhagana ndi anzathu ndiponso achibale amene tinkawakonda kwambiri koma tinasiyana nawo kalekale chifukwa cha imfa. Anthu onse adzatamanda Yehova chifukwa cha mphamvu zake zoukitsa.
23. Kodi ndi chinthu chachikulu chiti chimene Yehova anachita posonyeza mphamvu zake, ndipo zimenezi zimatitsimikizira bwanji kuti akufa adzaukitsidwa?
23 Yehova watithandiza kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono zoti akufa adzaukitsidwa. Iye anaukitsa Mwana wake Yesu ndi thupi lauzimu ndipo anamupatsa mphamvu komanso udindo waukulu kuposa angelo onse. Imeneyi inali njira yaikulu kwambiri imene Yehova anasonyezera mphamvu zake. Yesu ataukitsidwa, anthu ambirimbiri anamuona. (1 Akorinto 15:5, 6) Umenewu ndi umboni wokwanira wakuti akufa adzauka, ngakhale kwa anthu amene sakhulupirira zimenezi. Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa moyo.
24. N’chifukwa chiyani tiyenera kumakhulupirira kuti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira, nanga ndi chiyembekezo chiti chimene tonsefe tiyenera kuchiona kuti ndi chamtengo wapatali?
24 Sikuti Yehova wangokhala ndi mphamvu zobwezeretsa moyo kwa anthu amene anamwalira, koma ndi wofunitsitsanso kuchita zimenezi. Yobu, yemwe anali wokhulupirika, anauziridwa kunena kuti Yehova amachita kulakalaka kuti adzaukitse anthu amene anamwalira. (Yobu 14:15) Kodi simukufunitsitsa kuti Mulungu wathu, yemwe amalakalaka kugwiritsa ntchito mwachikondi mphamvu zake zobwezeretsa zinthu, akhale mnzanu? Komabe, kumbukirani kuti kuukitsa anthu amene anamwalira ndi mbali imodzi yokha ya ntchito yaikulu yobwezeretsa zinthu imene Yehova adzachite. Pamene mukuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye, nthawi zonse muziona kuti chiyembekezo chanu, choti mukhoza kudzakhalapo Yehova ‘akamadzapanga zonse kuti zikhale zatsopano,’ ndi chamtengo wapatali.—Chivumbulutso 21:5.
a “Nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” inayamba pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa komanso pamene mbadwa ya Mfumu Davide, yemwe anali wokhulupirika, inakhala Mfumu. Yehova analonjeza Davide kuti mmodzi wa mbadwa zake adzalamulira mpaka kalekale. (Salimo 89:35-37) Koma Ababulo atawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., palibe mbadwa ya Davide iliyonse imene inakhala pampando wachifumu wa Mulungu. Yesu, amene anabadwa monga wolowa ufumu wa Davide, anakhala Mfumu yomwe Mulungu analonjeza kalekale, pamene anapatsidwa Ufumu kumwamba.
b Mwachitsanzo, Mose, Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Hoseya, Yoweli, Amosi, Obadiya, Mika ndi Zefaniya analemba za nkhani imeneyi.
-
-
“Khristu Ndi Mphamvu ya Mulungu”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 9
“Khristu Ndi Mphamvu ya Mulungu”
1-3. (a) Kodi ophunzira a Yesu anakumana ndi zoopsa zotani panyanja ya Galileya, nanga Yesu anatani? (b) N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti mtumwi Paulo ananena kuti “Khristu ndi mphamvu ya Mulungu”?
PA NTHAWI ina ophunzira a Yesu anachita mantha kwambiri. Iwo ankawoloka nyanja ya Galileya ndipo mwadzidzidzi panyanjapo panayambika chimphepo. N’zosakayikitsa kuti anali atakumanapo kale ndi mphepo panyanja chifukwa ena mwa iwo anali asodzi odziwa bwino ntchito yawo.a (Mateyu 4:18, 19) Koma imeneyi inali “mphepo yamphamvu,” ndipo inachititsa kuti panyanjapo payambike mafunde akuluakulu. Ophunzirawo anachita mantha ndipo anapalasa ngalawa ndi mphamvu zawo zonse koma mphepoyo inkawaposa mphamvu. Mafunde “ankawomba ngalawayo” ndipo inayamba kudzaza madzi. Ngakhale kuti zinthu zinali chonchi, Yesu anali m’tulo tofa nato kumbuyo kwa ngalawayo chifukwa anali atatopa ndi kuphunzitsa gulu la anthu pa tsikulo. Poopa kufa, ophunzirawo anamudzutsa n’kumupempha kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!”—Maliko 4:35-38; Mateyu 8:23-25.
2 Yesu sanachite mantha chifukwa ankadziwa kuti ali ndi mphamvu zoletsa mphepoyo. Choncho anadzudzula mphepo komanso nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!” Nthawi yomweyo, mphepo ndi nyanjayo zinamvera moti mafunde aja anasiya ndipo “panachita bata lalikulu.” Koma ophunzirawo ataona zimenezi anachita mantha kwambiri. Anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni?” Zimenezi n’zomveka, nanga ndi munthu uti amene angadzudzule mphepo ndi nyanja ngati kuti akudzudzula mwana wosamvera?—Maliko 4:39-41; Mateyu 8:26, 27.
3 Komatu Yesu sanali munthu wamba. Yehova ankagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza Yesu m’njira zapadera komanso kumulola kuti azithandiza ena. Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo ananena moyenerera kuti: “Khristu ndi mphamvu ya Mulungu.” (1 Akorinto 1:24) Kodi Yesu amasonyeza mphamvu za Mulungu m’njira ziti? Nanga timapindula bwanji ndi mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zimenezi?
Mphamvu za Mwana Wobadwa Yekha wa Mulungu
4, 5. (a) Kodi Yehova anapatsa Mwana wake wobadwa yekha mphamvu komanso udindo wochita chiyani? (b) Kodi n’chiyani chinkathandiza Mwanayu kuti akwanitse kugwira ntchito yolenga zinthu imene Atate wake anamupatsa?
4 Taganizirani mphamvu zimene Yesu anali nazo asanakhale munthu. Yehova anasonyeza “mphamvu zake zosatha” pamene analenga Mwana wake wobadwa yekha, yemwe kenako ankadziwika kuti Yesu Khristu. (Aroma 1:20; Akolose 1:15) Kenako Yehova anapatsa Mwanayu mphamvu zambiri komanso udindo waukulu ndipo anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. Ponena za Mwana ameneyu, Baibulo limati: “Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.”—Yohane 1:3.
5 Tikhoza kungomvetsa zochepa chabe zokhudza kukula kwa ntchito imeneyi. Taganizirani mphamvu zomwe zinafunika kuti alenge angelo amphamvu mamiliyoni ambiri, nyenyezi zosawerengeka komanso zinthu zamoyo zambirimbiri zapadzikoli. Kuti akwanitse kugwira ntchito imeneyi, Yehova anapatsa Mwana wobadwa yekhayu mzimu woyera womwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse. Mwanayu anasangalala kwambiri kukhala Mmisiri Waluso amene Yehova anagwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse.—Miyambo 8:22-31.
6. Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atafa n’kuukitsidwa?
6 Kodi Yehova akanapatsanso Mwana wake mphamvu komanso udindo wina wowonjezera? Yesu atafa padzikoli n’kuukitsidwa, anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anapatsidwa mphamvu zoti angathe kulamulira chilichonse m’chilengedwechi. Popeza iye ndi ‘Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,’ wapatsidwa mphamvu zoti adzathetse “maboma onse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse” zimene zimatsutsana ndi Atate wake. (Chivumbulutso 19:16; 1 Akorinto 15:24-26) Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa” Yesu, kungopatulapo iyeyo.—Aheberi 2:8; 1 Akorinto 15:27.
7. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yesu sangagwiritse ntchito molakwika mphamvu zimene Yehova anamupatsa?
7 Kodi tiyenera kumada nkhawa kuti mwina Yesu akhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika? Ayi ndithu. Yesu amakonda kwambiri Atate ake ndipo sangachite chilichonse chimene chingawakhumudwitse. (Yohane 8:29; 14:31) Iye amadziwa kuti ngakhale kuti Yehova ali ndi mphamvu zonse, sagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zakezo. Yesu anaona yekha kuti Yehova amafunafuna mipata “kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mofanana ndi Atate ake, Yesu nayenso amakonda anthu. Choncho tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti nthawi zonse azigwiritsa ntchito bwino mphamvu zake. (Yohane 13:1) Ndipotu Yesu wakhala akugwiritsa ntchito mphamvu zake moyenera. Tiyeni tione mmene ankazigwiritsira ntchito pamene anali padzikoli komanso chifukwa chake ankachita zimenezo.
“Wamphamvu . . . M’mawu”
8. Kodi Yesu atadzozedwa anapatsidwa mphamvu zochita chiyani, nanga anazigwiritsa ntchito bwanji?
8 N’zodziwikiratu kuti Yesu sanachitepo zodabwitsa pamene anali mnyamata ku Nazarete. Koma zinthu zinasintha atabatizidwa mu 29 C.E., ndipo pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka pafupifupi 30. (Luka 3:21-23) Baibulo limati: “Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye, anayenda m’dziko lonse n’kumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi ankawazunza.” (Machitidwe 10:38) Mawu akuti “n’kumachita zabwino,” akusonyeza kuti Yesu ankagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza anthu. Atadzozedwa, anakhala “mneneri wamphamvu m’zochita komanso m’mawu.”—Luka 24:19.
9-11. (a) Kodi nthawi zambiri Yesu ankaphunzitsira kuti, nanga panali mavuto otani? (b) N’chifukwa chiyani gulu la anthu linadabwa ndi mmene Yesu ankaphunzitsira?
9 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wamphamvu m’mawu? Nthawi zambiri ankaphunzitsira panja. Mwachitsanzo, ankaphunzitsira m’mbali mwa nyanja, m’munsi mwa mapiri, m’misewu ndiponso m’misika. (Maliko 6:53-56; Luka 5:1-3; 13:26) Omvera ake akanatha kuchoka mosavuta zikanakhala kuti zolankhula zake sizikuwafika pamtima. Popeza pa nthawiyi kunalibe mabuku osindikiza, anthu amene ankasangalala ndi zomwe Yesu ankaphunzitsa ankafunika kuzisunga m’maganizo mwawo n’kumazikumbukirabe. Choncho zimene Yesu ankaphunzitsa zinkafunika kukhala zokopa, zomveka bwino ndiponso zosavuta kukumbukira. Koma limeneli silinali vuto kwa Yesu. Mwachitsanzo, taganizirani ulaliki wake wa paphiri.
10 Tsiku lina m’mawa chakumayambiriro kwa chaka cha 31 C.E., gulu la anthu linasonkhana m’mbali mwa phiri pafupi ndi nyanja ya Galileya. Ena anachokera ku Yudeya enanso ku Yerusalemu, mtunda wa makilomita pafupifupi 100 kapena 110. Ena anachokera kumpoto m’madera a m’mbali mwa nyanja, a ku Turo ndi Sidoni. Anthu ambiri odwala ankayandikira Yesu kuti amugwire, ndipo iye ankawachiritsa. Atachiritsa odwala onse pagululo, anayamba kuwaphunzitsa. (Luka 6:17-19) Atamaliza kulankhula, iwo anadabwa ndi zimene anamva. Chifukwa chiyani?
11 Patatha zaka zingapo, munthu wina amene anamva ulaliki umenewo analemba kuti: “Gulu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu waulamuliro.” (Mateyu 7:28, 29) Zonena za Yesu zinali zogwira mtima. Ankalankhula m’malo mwa Mulungu ndipo chilichonse chimene ankaphunzitsa chinkachokera m’Mawu a Mulungu. (Yohane 7:16) Mfundo za Yesu zinali zomveka bwino, zosatsutsika komanso zogwira mtima moti anthu ankazitsatira. Ankathandiza omvera ake kudziwa pamene pali vuto ndiponso kudzifufuza moona mtima. Anawaphunzitsa zimene angachite kuti azisangalala, aziika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba, akhale ndi tsogolo labwino komanso mmene angapempherere. (Mateyu 5:3 mpaka 7:1-27) Mawu ake anathandiza kuti anthu amene ankafunafuna choonadi ndi chilungamo achitepo kanthu. Anthuwa anali okonzeka ‘kudzikana’ n’kusiya chilichonse kuti ayambe kumutsatira. (Mateyu 16:24; Luka 5:10, 11) Umenewu ndi umboni wakuti mawu a Yesu analidi ndi mphamvu.
“Wamphamvu M’zochita”
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anali “wamphamvu m’zochita”? (b) Kodi ndi zodabwitsa zosiyanasiyana ziti zimene iye anachita?
12 Yesu analinso “wamphamvu m’zochita.” (Luka 24:19) Mabuku a Uthenga Wabwino amatchula zodabwitsa zoposa 30 zimene iye anachita mothandizidwa ndi “mphamvu ya Yehova.”b (Luka 5:17) Zodabwitsa zimene anachitazi zinathandiza anthu ambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anadyetsa amuna 5,000 ndipo kenako amuna 4,000. Ngati titaphatikizapo akazi ndi ana, ndiye kuti anadyetsa anthu masauzande ambiri.—Mateyu 14:13-21; 15:32-38.
13 Zodabwitsa zimene Yesu ankachita zinali zosiyanasiyana. Anali ndi mphamvu kuposa ziwanda ndipo sankavutika kuzitulutsa. (Luka 9:37-43) Ankathanso kusandutsa madzi kukhala vinyo. (Yohane 2:1-11) Komanso taganizirani mmene ophunzira ake anadabwira pamene “anaona Yesu akuyenda panyanja.” (Yohane 6:18, 19) Analinso ndi mphamvu zogonjetsa matenda moti ankachiritsa olumala, odwala matenda okhalitsa ndiponso amene anali atatsala pang’ono kufa. (Maliko 3:1-5; Yohane 4:46-54) Anthuwa ankawachiritsa m’njira zosiyanasiyana. Anthu ena anawachiritsa ali kutali, pamene ena, ankachita kuwagwira. (Mateyu 8:2, 3, 5-13) Ena ankachira nthawi yomweyo pamene ena ankachira pang’onopang’ono.—Maliko 8:22-25; Luka 8:43, 44.
“Anaona Yesu akuyenda panyanja”
14. Kodi ndi nkhani ziti zomwe zikusonyeza kuti Yesu anali ndi mphamvu zoukitsa akufa?
14 Koma chochititsa chidwi kwambiri n’choti Yesu analinso ndi mphamvu zoukitsa akufa. Pali nkhani zitatu zomwe zinalembedwa. Anaukitsa mtsikana wazaka 12 n’kumupereka kwa makolo ake, mnyamata yemwe anali mwana yekhayo wa mayi wamasiye ndiponso munthu wina amene azichemwali ake ankamukonda kwambiri. (Luka 7:11-15; 8:49-56; Yohane 11:38-44) Panalibe chimene chinalepheretsa Yesu kuti aukitse anthuwa. Mtsikana wazaka 12 anamuukitsira pamalo omwe anamugoneka atangomwalira kumene. Mwana wa mayi wamasiyeyo ayenera kuti anamuukitsa pa tsiku lomwe anamwalira ndipo anamuukitsira pachithatha chimene anamunyamulirapo. Koma Lazaro anamuukitsa kumanda patatha masiku 4 kuchokera pamene anamwalira.
Ankagwiritsa Ntchito Mphamvu pa Zifukwa Zoyenera Komanso M’njira Yoyenera
15, 16. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yesu sankagwiritsa ntchito mphamvu zake modzikonda?
15 Kodi mukuganiza kuti mphamvu za Yesu zikanaperekedwa kwa wolamulira yemwe si wangwiro akanazigwiritsa ntchito bwanji? Nthawi zambiri olamulira a m’dzikoli amakhala odzikonda, onyada ndiponso adyera, choncho amagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika. Koma Yesu sanachimwepo ndipo sankachita zimenezi.—1 Petulo 2:22.
16 Yesu sankagwiritsa ntchito mphamvu zake modzikonda koma ankazigwiritsa ntchito kuti athandize ena. Mwachitsanzo, pamene anali ndi njala, anakana kusandutsa miyala kuti ikhale mkate woti iyeyo adye. (Mateyu 4:1-4) Umboni woti sanagwiritse ntchito mphamvu zake kuti adzilemeretse ndi woti analibe katundu wambiri. (Mateyu 8:20) Komanso sankachita zodabwitsa n’cholinga choti apindulepo kenakake. Ndipotu Yesu akamachita zodabwitsa, ankaluzapo zinthu zina. Mwachitsanzo, akachiritsa odwala mphamvu zina zinkatuluka m’thupi mwake ndipo iye ankadziwa zimenezi ngakhale akangochiritsa munthu mmodzi. (Maliko 5:25-34) Komabe ankalola kuti anthu ambirimbiri amukhudze n’kuchiritsidwa. (Luka 6:19) Izitu zikusonyeza kuti Yesu sanali wodzikonda.
17. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti sankagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachisawawa?
17 Yesu sankagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachisawawa. Sanachitepo zodabwitsa pofuna kungodzionetsera kapena kutchuka. (Mateyu 4:5-7) Mwachitsanzo, anakana kuchita zodabwitsa atazindikira kuti Herode akungofuna kumuona akuchita zimenezo. (Luka 23:8, 9) M’malo molengeza zokhudza mphamvu zake, nthawi zambiri akachiritsa munthu ankamuuza kuti asauze aliyense. (Maliko 5:43; 7:36) Sankafuna kuti anthu adziwe zoti iye ndi Mesiya chifukwa chongomva nkhani zosangalatsa zokhudza zodabwitsa zimene ankachita.—Mateyu 12:15-19.
18-20. (a) Kodi n’chiyani chinkachititsa kuti Yesu azigwiritsa ntchito mphamvu zake kuthandiza ena? (b) Kodi mukumva bwanji mukaganizira mmene Yesu anachiritsira munthu wina yemwe anali ndi vuto losamva?
18 Ngakhale kuti Yesu anali ndi mphamvu zambiri chonchi, anali wosiyana kwambiri ndi olamulira amene amagwiritsa ntchito mphamvu zawo mosaganizira zimene anthu akufunikira komanso mavuto amene akukumana nawo. Iye ankachita zinthu moganizira ena. Akaona anthu akuvutika, zinkamukhudza kwambiri moti ankawathandiza. (Mateyu 14:14) Ankaganizira mmene ena akumvera komanso zomwe akufunikira, choncho ankagwiritsa ntchito mphamvu zake kuti awathandize. Chitsanzo chochititsa chidwi cha zimenezi chili pa Maliko 7:31-37.
19 Pa nthawiyi gulu la anthu litapeza Yesu, linamubweretsera odwala ambiri ndipo iye anachiritsa onsewo. (Mateyu 15:29, 30) Koma kenako anasankhapo munthu wina kuti amuthandize mwapadera. Bambo ameneyu anali ndi vuto losamva komanso ankavutika kulankhula. Mwina Yesu anazindikira kuti munthuyu anali ndi mantha kapena ankachita manyazi. Choncho posonyeza kumuganizira, Yesu anamutengera pambali. Kenako anachita zinthu zingapo pofuna kuthandiza munthuyo kudziwa zomwe ankafuna kuchita. “Anapisa zala zake m’makutu a munthuyo, ndipo atalavulira pazala zake anakhudza lilime la munthuyo.”c (Maliko 7:33) Kenako Yesu anayang’ana kumwamba n’kupumira m’mwamba. Zimenezi zinathandiza munthuyo kudziwa kuti zomwe amuchitire zitheka chifukwa chothandizidwa ndi Mulungu. Kenako Yesu anati: “Tseguka.” (Maliko 7:34) Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kumva ndiponso kulankhula bwinobwino.
20 N’zochititsa chidwi kwambiri kudziwa kuti Yesu akamachiritsa anthu pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa, ankachita zimenezi mwachifundo komanso mowaganizira. Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova wasankha Yesu, yemwe ali ndi makhalidwe amenewa, kuti akhale Mfumu ya Ufumu wake?
Anasonyeza Zimene Adzachite M’tsogolo
21, 22. (a) Kodi zodabwitsa zimene Yesu anachita zinasonyeza chiyani? (b) Popeza Yesu amatha kulamulira zinthu zam’chilengedwe, kodi tingayembekezere zotani mu ulamuliro wake?
21 Zodabwitsa zimene Yesu anachita ali padzikoli zinkangosonyeza madalitso ambiri amene tidzasangalale nawo mu ulamuliro wake. M’dziko latsopano, Yesu adzachitanso zodabwitsa, koma adzazichita padziko lonse. Taonani zina mwa zinthu zomwe tikuyembekezera.
22 Yesu adzabwezeretsa zinthu zonse zachilengedwe zimene zinawonongeka padzikoli. Kumbukirani kuti anasonyeza kuti akhoza kulamulira zinthu zam’chilengedwe poletsa mphepo panyanja. Choncho mu ulamuliro wa Khristu, anthu sazidzaopa kuti akhoza kuvulazidwa ndi mphepo zamkuntho, zivomerezi, kuphulika kwa mapiri kapena ngozi zina zam’chilengedwe. Popeza Yesu ndi Mmisiri Waluso, yemwe Yehova anamugwiritsa ntchito polenga dziko lapansi ndi zamoyo zonse, amadziwa mmene dzikoli linapangidwira. Amadziwanso mmene tingagwiritsire ntchito bwino zinthu zapadzikoli. Mu ulamuliro wake, dziko lonseli lidzakhala Paradaiso.—Luka 23:43.
23. Monga Mfumu, kodi Yesu adzathandiza bwanji anthu?
23 Nanga kodi Yesu adzathandiza bwanji anthu? Iye ankatha kudyetsa mokwanira anthu masauzande ambiri pogwiritsa ntchito chakudya chochepa. Zimenezi zikutitsimikizira kuti sikudzakhala njala akamadzalamulira. Aliyense adzakhala ndi chakudya chambiri. (Salimo 72:16) Yesu anali ndi mphamvu zochiritsa matenda ndipo zimenezi zimasonyeza kuti anthu odwala, ovulala, olumala komanso amene ali ndi vuto losaona ndiponso losamva adzachiritsidwa ndipo sadzadwalanso. (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Popeza Yesu, yemwe ndi Mfumu yamphamvu ya Ufumu wa Mulungu, ankatha kuukitsa akufa, ndiye kuti adzaukitsa anthu mamiliyoni osawerengeka amene Atate ake asankha kuwakumbukira.—Yohane 5:28, 29.
24. Tikamaganizira zokhudza mphamvu za Yesu, kodi tiyenera kukumbukira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
24 Tikamaganizira zokhudza mphamvu za Yesu, tizikumbukira kuti iye amatsanzira kwambiri Bambo ake. (Yohane 14:9) Choncho mmene Yesu amagwiritsira ntchito mphamvu zimasonyeza bwino mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yesu anachitira zinthu mokoma mtima pamene ankachiritsa munthu wina wakhate. Atagwidwa chifundo, Yesu anakhudza munthuyo n’kunena kuti: “Ndikufuna.” (Maliko 1:40-42) Tikamawerenga nkhani ngati zimenezi, zimakhala ngati Yehova akutiuza kuti, ‘Mphamvu zanga ndimazigwiritsa ntchito chonchi.’ Kunena zoona, tiyenera kutamanda komanso kuthokoza Mulungu wathu wamphamvuyonse chifukwa choti amagwiritsa ntchito mphamvu zake mwachikondi.
a Nthawi zambiri panyanja ya Galileya pamatha kuyamba mphepo mwadzidzidzi. Chifukwa chakuti nyanjayi ili pamalo otsika kwambiri, mpweya wapanyanjayi umakhala wotentha kwambiri kusiyana ndi madera ozungulira. Chifukwa cha zimenezi, nyengo imakhala yosakhazikika. M’chigwa cha Yorodano mumawomba mphepo yamphamvu yochokera m’phiri la Herimoni lomwe lili kumpoto kwa nyanjayi. Nyengo yabata imatha kusintha mwadzidzidzi kenako mphepo ya mkuntho n’kuyamba.
b Kuwonjezera pamenepa, nthawi zina mabuku a Uthenga Wabwino amaphatikiza zodabwitsa zambiri n’kuzifotokozera pamodzi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina “anthu onse amumzinda” anabwera kudzaona Yesu, ndipo iye anachiritsa “anthu ambiri.”—Maliko 1:32-34.
c Ayuda komanso anthu amitundu ina ankakhulupirira kuti kulavula malovu ndi njira kapena chizindikiro cha kuchiritsa, ndipo mabuku a Arabi amafotokozanso za kuchiritsa pogwiritsa ntchito njirayi. Mwina Yesu analavula malovu pongofuna kuuza munthuyu kuti anali atatsala pang’ono kumuchiritsa. Koma sikuti anagwiritsa ntchito malovu ake ngati mankhwala.
-
-
“Muzitsanzira Mulungu” Mukamagwiritsa Ntchito MphamvuYandikirani Yehova
-
-
MUTU 10
“Muzitsanzira Mulungu” Mukamagwiritsa Ntchito Mphamvu
1. Kodi anthu omwe si angwirofe timakodwa mosavuta mumsampha uti?
“MUNTHU aliyense amene wapatsidwa mphamvu, pakapita nthawi amakodwa mumsampha wosaonekera.” Mawu amenewa ananena ndi wandakatulo wina wa m’zaka za m’ma 1800, ndipo amanena za vuto linalake lomwe ndi kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika. N’zomvetsa chisoni kuti anthu omwe si angwirofe timakodwa mosavuta mumsampha umenewu. Kuyambira kalekale, “munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Munthu waudindo akamagwiritsa ntchito mphamvu zake mopanda chikondi, anthu ambiri amavutika.
2, 3. (a) Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu? (b) Kodi anthufe tili ndi mphamvu zotha kuchita chiyani, nanga tiyenera kuzigwiritsa ntchito bwanji?
2 Ndiye kodi si zochititsa chidwi kuti Yehova Mulungu, amene ali ndi mphamvu zopanda malire, sagwiritsa ntchito mphamvuzo molakwika? Monga taonera m’mitu yapitayi, nthawi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu, kuwononga, kuteteza kapena kubwezeretsa pa zifukwa zabwino komanso mwachikondi. Tikamaganizira mozama mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zake, timafunitsitsa kuti akhale mnzathu. Zimenezi zingatichititse kuti ‘tizimutsanzira’ tikamagwiritsa ntchito mphamvu zathu. (Aefeso 5:1) Komabe anthufe ndife otsika poyerekezera ndi Mulungu. Ndiye kodi tili ndi mphamvu zotani?
3 Kumbukirani kuti munthu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu” ndipo ndi wofanana naye. (Genesis 1:26, 27) Choncho ifenso tili ndi mphamvu ndithu. Tili ndi mphamvu zotha kukwaniritsa zinazake, kugwira ntchito, kuuza ena zochita kapena kuwalamulira ndiponso kulimbikitsa ena kuchita zinazake, makamaka amene amatikonda. Tithanso kukhala ndi thupi lamphamvu kapenanso kukhala ndi chuma n’kumatha kuchita zinazake. Ponena za Yehova, wolemba masalimo wina anati: “Inu ndinu kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Choncho mphamvu zilizonse zomwe tili nazo, Mulungu ndi amene amatipatsa kapena kutilola kuti tikhale nazo. N’chifukwa chake timafuna kuti azisangalala ndi mmene timazigwiritsira ntchito. Ndiye kodi tingachite bwanji zimenezi?
Chinsinsi Chake Ndi Chikondi
4, 5. (a) Kodi chinsinsi chogwiritsa ntchito bwino mphamvu n’chiyani, nanga chitsanzo cha Mulungu chimasonyeza bwanji zimenezi? (b) Kodi chikondi chingatithandize bwanji kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphamvu?
4 Chinsinsi chogwiritsa ntchito mphamvu moyenera ndi chikondi. Timaona zimenezi tikaganizira chitsanzo cha Mulungu. Kumbukirani zomwe tinakambirana m’Mutu 1 zokhudza makhalidwe 4 akuluakulu a Mulungu, omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru komanso chikondi. Pa makhalidwe amenewa, kodi lalikulu kwambiri ndi liti? Chikondi. Lemba la 1 Yohane 4:8 limati, “Mulungu ndi chikondi.” Choncho khalidwe lalikulu la Yehova ndi chikondi ndipo zonse zimene amachita, amazichita chifukwa cha chikondi komanso kuti zithandize anthu amene amamukonda.
5 Nafenso chikondi chingatithandize kuti tisamagwiritse ntchito mphamvu molakwika. Ndipotu Baibulo limatiuza kuti chikondi “n’chokoma mtima” komanso “sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:4, 5) Choncho ngati tili ndi chikondi, anthu amene tikuwalamulira sitingawachitire zinthu mosawaganizira kapena mwankhanza. M’malomwake timawalemekeza n’kumaganizira kwambiri zofuna zawo osati zathu.—Afilipi 2:3, 4.
6, 7. (a) Kodi kuopa Mulungu n’kutani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti khalidweli lingatithandize kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphamvu? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuopa kukhumudwitsa Mulungu n’kogwirizana ndi kumukonda.
6 Chikondi chimagwirizananso ndi khalidwe lina limene lingatithandize kuti tisamagwiritse ntchito mphamvu molakwika, lomwe ndi kuopa Mulungu. Kodi kuopa Mulungu n’kofunika bwanji? Lemba la Miyambo 16:6 limati: “Chifukwa choopa Yehova, munthu amapewa kuchita zoipa.” Chimodzi mwa zinthu zoipa zimene tiyenera kupewa ndi kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika. Ngati timaopa Mulungu, sitingamazunze anthu amene timawalamulira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti timadziwa kuti tidzayankha kwa Mulungu pa nkhani ya mmene timachitira zinthu ndi anthu amenewa. (Nehemiya 5:1-7, 15) Koma palinso chifukwa china chofunika kwambiri. Mawu a chilankhulo choyambirira omwe anawamasulira kuti “kuopa,” nthawi zambiri amatanthauza kulemekeza kwambiri Mulungu. Choncho Baibulo limasonyeza kuti timafunika kukonda Mulungu kuti tizimulemekeza kwambiri. (Deuteronomo 10:12, 13) Tikamalemekeza Mulungu kwambiri chonchi, timapewa kuchita zimene zingamukhumudwitse osati chifukwa chongoopa zotsatira zake, koma chifukwa choti timamukonda.
7 Mwachitsanzo, taganizirani za mnyamata wamng’ono amene amagwirizana kwambiri ndi bambo ake. Mnyamatayo amadziwa kuti bambo akewo amamukonda komanso amasangalala naye. Koma amadziwanso zimene bambo akewo amafuna kuti iye azichita ndiponso kuti akachita zosayenera akhoza kumupatsa chilango. Mnyamatayu sachita mantha ndi bambo akewo koma amawakonda kwambiri ndipo amafunitsitsa kumachita zimene zimawasangalatsa. Ndi zimenenso zimachitika munthu akamaopa Mulungu. Chifukwa choti timakonda Yehova, yemwe ndi Bambo wathu wakumwamba, timaopa kuchita chilichonse chimene chingamukhumudwitse. (Genesis 6:6) M’malomwake, timafunitsitsa kuti tizisangalatsa mtima wake. (Miyambo 27:11) N’chifukwa chake timafuna kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphamvu zathu. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.
M’banja
8. (a) Kodi amuna ali ndi udindo wotani m’banja, nanga ayenera kumachita bwanji zinthu? (b) Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amalemekeza mkazi wake?
8 Choyamba, taganizirani za m’banja. Lemba la Aefeso 5:23 limati: “Mwamuna ndi mutu wa mkazi wake.” Kodi mwamuna ayenera kumagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zimene Mulungu anamupatsazi? Baibulo limauza amuna kuti azikhala ndi akazi awo “mowadziwa bwino” komanso ‘aziwapatsa ulemu chifukwa akazi ali ngati chiwiya chosachedwa kusweka.’ (1 Petulo 3:7) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kupatsa ulemu” amatanthauza kuona kuti chinthu ndi “chodula, chofunika kwambiri, . . . cholemekezeka.” Mawu ena ochokera ku mawu amenewa amamasulidwanso kuti “mphatso” ndiponso “chamtengo wapatali.” (Machitidwe 28:10; 1 Petulo 2:7) Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake samumenya, kumuchititsa manyazi kapena kumunyoza. Kumuchitira zimenezi kungachititse kuti mkaziyo azidziona kuti ndi wosafunika. Koma amazindikira kuti mkazi wakeyo ndi wofunika kwambiri ndipo amamupatsa ulemu. Kaya ali kwa okha kapena pagulu, zolankhula komanso zochita zake zimasonyeza kuti amaona kuti mkazi wake ndi wamtengo wapatali kwa iye. (Miyambo 31:28) Mwamuna wotereyu, mkazi wake amamukonda komanso kumulemekeza ndiponso chofunika kwambiri n’choti Mulungu amasangalala naye.
Mwamuna ndi mkazi wake amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo akamakondana komanso kulemekezana
9. (a) Kodi akazi ali ndi mphamvu zotani m’banja? (b) N’chiyani chingathandize mkazi kuti azigwiritsa ntchito maluso ake pothandiza mwamuna wake, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
9 Akazi nawonso ali ndi mphamvu m’banja. Baibulo limatiuza za akazi oopa Mulungu amene molemekeza mutu wabanja, anathandiza amuna awo kuchita zabwino kapenanso kuti asasankhe zinthu molakwika. (Genesis 21:9-12; 27:46–28:2) Mkazi akhoza kukhala wanzeru kwambiri komanso kuti amachita bwino zinthu zina kuposa mwamuna wake. Komabe ayenera ‘kumalemekeza kwambiri’ mwamuna wake ndiponso ‘kumugonjera ngati mmene amagonjerera Ambuye.’ (Aefeso 5:22, 33) Mkazi akakhala ndi cholinga chosangalatsa Mulungu, amagwiritsa ntchito maluso ake pothandiza mwamuna wake m’malo momupeputsa kapena kufuna kuti azimulamulira. ‘Mkazi wanzeru’ ameneyu amachita zinthu mogwirizana ndi mwamuna wakeyo polimbitsa banja lawo. Choncho amapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Miyambo 14:1.
10. (a) Kodi Mulungu anapereka udindo wotani kwa makolo? (b) Kodi mawu akuti “malangizo” amatanthauza chiyani, nanga makolo ayenera kulangiza bwanji ana awo? (Onaninso mawu am’munsi.)
10 Nawonso makolo ali ndi udindo umene Mulungu anawapatsa. Baibulo limati: “Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.” (Aefeso 6:4) M’Baibulo, mawu akuti “malangizo” angatanthauze “kulera, kuphunzitsa ndiponso kulangiza.” Ana amafunika kulangizidwa. Amakula bwino akamapatsidwa malamulo komanso malangizo omveka bwino. Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kulangiza mwana ndi kumukonda. (Miyambo 13:24) Choncho ‘ndodo yolangira’ siyenera kukhala yochitira nkhanza mwana kapena kumuopsezera.a (Miyambo 22:15; 29:15) Makolo akamapereka chilango chokhwima, chankhanza ndiponso mopanda chikondi ndiye kuti akugwiritsa ntchito molakwika udindo wawo. Chilango choterocho chingakwiyitse mwana. (Akolose 3:21) Koma chilango choyenera chingathandize ana kudziwa kuti makolo awo amawakonda ndiponso amawafunira zabwino.
11. Kodi ana angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo?
11 Nanga bwanji ana? Kodi angatani kuti azigwiritsa bwino mphamvu zawo? Lemba la Miyambo 20:29 limati: “Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo.” Kunena zoona, palibe njira yabwino kwambiri imene achinyamata angagwiritsire ntchito mphamvu zawo kuposa kutumikira “Mlengi” wathu Wamkulu. (Mlaliki 12:1) Achinyamata ayenera kukumbukira kuti zochita zawo zikhoza kusangalatsa kapena kukhumudwitsa makolo awo. (Miyambo 23:24, 25) Akamamvera makolo awo omwe ndi oopa Mulungu n’kumachita zoyenera, makolowo amasangalala. (Aefeso 6:1) Zimenezi ‘zimasangalatsanso Ambuye.’—Akolose 3:20.
Mu Mpingo
12, 13. (a) Kodi akulu ayenera kumauona bwanji udindo wawo mumpingo? (b) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kusamalira nkhosa mokoma mtima? Perekani chitsanzo.
12 Yehova anatipatsa oyang’anira kuti azitsogolera mumpingo wa Chikhristu. (Aheberi 13:17) Amuna oyenerera amenewa amafunika kugwiritsa ntchito udindo womwe Mulungu wawapatsa pothandiza nkhosa. Kodi oyang’anirawa ali ndi ufulu woti azilamulira abale ndi alongo awo? Ayi ndithu. Akulu amafunika kuti aziona moyenera udindo wawo mumpingo komanso azikhala odzichepetsa. (1 Petulo 5:2, 3) Baibulo limauza oyang’anira kuti: “Muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Machitidwe 20:28) Chimenechitu ndi chifukwa chachikulu chochitira zinthu mokoma mtima ndi aliyense mumpingo.
13 Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mnzanu wapamtima wakupemphani kuti mumusungire chinthu chinachake chamtengo wapatali. Mukudziwa kuti mnzanuyo anagula chinthucho modula kwambiri. Kodi simungachisunge mosamala kwambiri kuti chisawonongeke? Mofanana ndi zimenezi, Mulungu anapatsa akulu udindo wosamalira mpingo, womwe ndi chinthu chofunika kwambiri ndipo anthu amumpingowo amayerekezeredwa ndi nkhosa. (Yohane 21:16, 17) Yehova amakonda kwambiri nkhosa zake moti mpaka anazigula ndi magazi amtengo wapatali a Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu. Palibenso mtengo wokwera kuposa pamenepa umene Yehova akanalipira kuti agule nkhosazi. Akulu odzichepetsa amakumbukira zimenezi ndipo amasamalira nkhosa za Yehova mwachikondi.
“Mphamvu ya Lilime”
14. Kodi lilime lili ndi mphamvu yotani?
14 Baibulo limati: “Imfa ndiponso moyo zili mumphamvu ya lilime.” (Miyambo 18:21) Lilime likhozadi kuwononga zinthu. Tonsefe tinakhumudwapo chifukwa choti munthu wina anatilankhula mawu opweteka. Komatu lilime lilinso ndi mphamvu yokonza zinthu. Lemba la Miyambo 12:18 limati: “Lilime la anthu anzeru limachiritsa.” Izitu ndi zoona chifukwa mawu abwino komanso olimbikitsa amakhala ngati mankhwala ndipo angathandize munthu kuti ayambe kumva bwino. Taganizirani zitsanzo izi.
15, 16. Kodi tingagwiritse ntchito lilime lathu m’njira ziti polimbikitsa ena?
15 Lemba la 1 Atesalonika 5:14 limati: “Muzilankhula molimbikitsa kwa anthu amene ali ndi nkhawa.” Zoonadi, ngakhalenso atumiki okhulupirika a Yehova nthawi zina amavutika ndi nkhawa. Ndiye kodi tingawathandize bwanji? Muziwayamikira mosapita m’mbali komanso moona mtima, zomwe zingawathandize kuti azidziwa kuti Yehova amawaona kuti ndi amtengo wapatali. Muziwalimbikitsa ndi malemba omwe amasonyeza kuti Yehova amadera nkhawa komanso kukonda anthu a “mtima wosweka” ndiponso “amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.” (Salimo 34:18) Tikamagwiritsa ntchito lilime lathu polimbikitsa ena, timasonyeza kuti tikutsanzira Mulungu wathu wachifundo, yemwe “amalimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa.”—2 Akorinto 7:6.
16 Tingagwiritsenso ntchito lilime lathu polimbikitsa ena omwe akufunika kwambiri kulimbikitsidwa. Ngati Mkhristu mnzathu waferedwa, tikhoza kumulimbikitsa pomuuza mawu osonyeza kuti ifenso zatikhudza ndipo tikumudera nkhawa. Kodi pali m’bale kapena mlongo wachikulire amene akudziona kuti ndi wosafunika? Tikasankha kulankhula mawu abwino, tingamutsimikizire kuti ndi wofunika kwambiri ndiponso timamuyamikira. Kodi wina akudwala matenda okhalitsa? Mawu abwino amene tingamuuze pafoni, pomulembera kapena pamasom’pamaso angamulimbikitse kwambiri. Mlengi wathu amasangalala tikamalankhula mawu ‘abwino kuti alimbikitse ena.’—Aefeso 4:29.
17. Kodi tingagwiritse ntchito lilime lathu m’njira yofunika iti pothandiza ena, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?
17 Palibe njira ina yofunika kwambiri yogwiritsa ntchito mphamvu ya lilime lathu kuposa kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Lemba la Miyambo 3:27 limati: “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira zabwinozo, ngati ungathe kuwathandiza.” Ndi udindo wathu kuuza ena uthenga wabwino wowathandiza kuti adzapulumuke. Si bwino kungosunga uthenga wofunika kulengezedwa mwamsangawu, womwe Yehova watipatsa mowolowa manja. (1 Akorinto 9:16, 22) Koma kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita zambiri bwanji pa ntchito imeneyi?
Njira yabwino kwambiri yogwiritsa ntchito mphamvu zathu, ndi kuuza ena uthenga wabwino
Kutumikira Yehova ndi ‘Mphamvu Zathu Zonse’
18. Kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani?
18 Chifukwa chakuti timakonda Yehova, timagwira nawo ntchito yolalikira ndi mtima wonse. Koma kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani? Zimene amayembekezera, aliyense akhoza kukwanitsa kaya zinthu zili bwanji pa moyo wake. Baibulo limati: “Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova, osati anthu.” (Akolose 3:23) Pofotokoza lamulo lalikulu kwambiri pa onse, Yesu anati: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.” (Maliko 12:30) Yehova amayembekezera kuti aliyense azimukonda ndiponso kum’tumikira ndi moyo wake wonse.
19, 20. (a) Popeza mawu akuti moyo amaphatikizapo mtima, maganizo ndi mphamvu, n’chifukwa chiyani zimenezi zinatchulidwanso pa Maliko 12:30? (b) Kodi kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse kumatanthauza chiyani?
19 Kodi kutumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse kumatanthauza chiyani? Mawu akuti moyo akutanthauza munthu yense, kuphatikizapo mtima, maganizo ndi mphamvu zake. Popeza moyo ukuphatikizapo mtima, maganizo ndi mphamvu, n’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zikutchulidwanso pa Maliko 12:30? Taganizirani chitsanzo ichi. Kale munthu ankatha kudzigulitsa, kapena kuti kugulitsa moyo wake, kuti akhale kapolo. Koma kapoloyo akanatha kusankha kuti asamatumikire mbuye wake ndi mtima wonse. Akanathanso kusankha kuti asamagwiritse ntchito mphamvu zake zonse kapena nzeru zake zonse kuti zinthu za mbuye wake ziziyenda bwino. (Akolose 3:22) Choncho n’zodziwikiratu kuti Yesu anatchula mbali zinazi pofuna kutsindika mfundo yoti tisamasiye dala kuchita zambiri potumikira Mulungu. Kutumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse kumatanthauza kuchita zonse zomwe tingathe komanso kugwiritsa ntchito mphamvu zathu zonse pomutumikira.
20 Kodi kutumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse kukutanthauza kuti tonse tiyenera kumachita zofanana? Ayi. Zimenezi sizingatheke, chifukwa mmene zinthu zilili pa moyo wathu zimasiyana komanso tili ndi maluso osiyana. Mwachitsanzo, wachinyamata amene ndi wamphamvu komanso sadwaladwala akhoza kumalalikira nthawi yaitali kusiyana ndi munthu amene mphamvu zake ndi zochepa chifukwa cha uchikulire. Munthu yemwe sali pa banja angathe kuchita zambiri kusiyana ndi munthu amene ali pa banja chifukwa amakhala ndi udindo wosamalira banjalo. Tiyenera kuthokoza kwambiri ngati tili ndi mphamvu komanso timatha kuchita zambiri mu utumiki. Komabe sitiyenera kumadziyerekezera ndi ena n’kumaganiza kuti sakuchita zonse zomwe angathe. (Aroma 14:10-12) M’malomwake, tizigwiritsa ntchito mphamvu zathu polimbikitsa anzathu.
21. Kodi njira yabwino komanso yofunika kwambiri imene tingagwiritsire ntchito mphamvu zathu ndi iti?
21 Yehova amatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yogwiritsa ntchito mphamvu moyenera. Ngakhale kuti siife angwiro, timafuna kumutsanzira mmene tingathere. Tingagwiritse ntchito bwino mphamvu zathu ngati timalemekeza anthu amene timawayang’anira kapena kuwalamulira. Kuwonjezera pamenepa, timafuna kuti tizigwira ndi mtima wonse ntchito yolalikira imene Yehova watipatsa yomwe imathandiza kuti anthu adzapulumuke. (Aroma 10:13, 14) Kumbukirani kuti Yehova amasangalala mukamachita zonse zomwe inuyo mungakwanitse pomutumikira. Kodi simukufunitsitsa kumachita zonse zimene mungathe potumikira Mulungu yemwe ndi womvetsa komanso wachikondi chonchi? Palibenso njira ina yabwino komanso yofunika kwambiri imene mungagwiritsire ntchito mphamvu zanu kuposa imeneyi.
a Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “ndodo” ankatanthauza kamtengo kamene m’busa ankagwiritsa ntchito poweta nkhosa. (Salimo 23:4) Mofanana ndi zimenezi, mfundo yakuti makolo ayenera kugwiritsa ntchito “ndodo” polangiza ana awo ikusonyeza kuti ayenera kuchita zimenezi mwachikondi, osati mwankhanza.
-