Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Ofalitsa Atsopano
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Ophunzira a Yesu atsopano ayenera kuphunzitsidwa kusunga “zinthu zonse” zimene Yesu anatilamula. (Mat. 28:19, 20) Zina mwa zinthu zimenezi ndi kuphunzitsa ena choonadi. Ofalitsa ambiri atsopano anayamba kale kukamba nkhani za m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kulalikira kwa achibale komanso kwa anzawo. Komabe akaphunzira zambiri n’kuyamba kuzindikira kuti Yehova akufuna kuti anthu amve uthenga wabwino, amafuna kuti ayambe kulalikira kunyumba ndi nyumba. (Aroma 10:13, 14) Anthu amenewa akavomerezedwa kukhala ofalitsa osabatizidwa, amafunika kuwaphunzitsa kuti asamakhale ndi mantha akamagwira ntchito imeneyi.—Luka 6:40.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Yendani ndi munthu amene mukumuphunzitsa kulalikira ndipo mulalikire naye kunyumba ndi nyumba komanso mupite naye ku ulendo wobwereza kapena ku phunziro. Ngati palibe munthu amene mukumuphunzitsa kulalikira, mungayende ndi wofalitsa amene alibe luso kwenikweni.