Bokosi la Mafunso
◼ Kodi wofalitsa wosabatizidwa yemwe akufuna kubatizidwa ayenera kukhala atasonkhana komanso kulalikira kwa nthawi yaitali bwanji?
Kubatizidwa ndi chosankha chachikulu pa moyo wa munthu. Choncho munthu asanavomerezedwe kuti abatizidwe, ayenera kusonyeza kuti akumvetsa zimene Mulungu amafuna kwa Akhristu obatizidwa. Komanso ayenera kukhala atayamba kale kusonyeza kuti ndi wofunitsitsa kutsatira zimene Mulungu amafuna.
Akhristu amalamulidwa kuti azisonkhana nthawi zonse, choncho wofalitsa wosabatizidwa ayenera kukhala atayamba kale kufika pa misonkhano ya mpingo mokhazikika. (Aheb. 10:24, 25) Ayeneranso kuyesetsa kumayankha pa misonkhanoyo. Komanso, ngakhale kuti si lamulo, iye ayenera kukhala atalembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Popeza Akhristu anapatsidwa lamulo loti azilalikira uthenga wabwino ndi kuthandiza anthu kukhala ophunzira a Yesu, wofalitsa wosabatizidwa ayeneranso kumalalikira nthawi zonse. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kodi wofalitsa wosabatizidwa ayenera kulalikira kwa miyezi ingati asanabatizidwe? Payenera kupita nthawi yokwanira kuti asonyeze zoti amakonda kulalikira. Zimenezi zingaonekere ngati amalalikira mwakhama mwezi uliwonse. (Sal. 78:37) Komabe sipayenera kutenga nthawi yaitali kuchokera pamene anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Mwina pangangotenga miyezi chabe. Kodi ayenera kupereka maola ochuluka bwanji pa mwezi? Palibe lamulo. Akulu ayenera kuona mmene zinthu zilili pa moyo wa wofalitsa wosabatizidwayo.—Luka 21:1-4.
Akulu (kapena atumiki othandiza, ngati palibe akulu okwanira) amene amafunsa mafunso anthu ofuna kubatizidwa, ayenera kukumbukira kuti anthu timasiyanasiyana, choncho ayenera kuona ngati munthuyo ali woyenera kubatizidwa. Akulu aone ngati munthuyo ndi wofunitsitsa kukhala wa Mboni za Yehova ndipo akusonyeza kuti amayamikira mwayi wokhala m’gulu la Yehova komanso wolalikira. Ayeneranso kuzindikira kuti munthuyo sanafike podziwa zambiri komanso alibe luso ngati mmene anthu amene anabatizidwa kale alili. Ngati akulu aona kuti iye sakuyenera kubatizidwa, ayenera kumuuza mokoma mtima zifukwa za m’Malemba zomwe zikusonyeza kuti ndi wosayenera n’kumulimbikitsa kuti apitirize kuphunzira.