Zakumwa Zoledzeretsa Nchiyani Chomwe Chiri Kawonedwe Kachikristu ka Izo?
“NDANI ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Ngamene achedwa pali vinyo.” (Miyambo 23:29, 30) Inde, Baibulo limadziwikitsa kuti zakumwa zoledzeretsa zingatulutse ziyambukiro zoipa kwenikweni: Kubwebweta, khalidwe lochititsa manyazi, khalidwe lamisala, kusoweka kwa umoyo wabwino, mavuto a banja, ndipo ngakhale umphawi.
Dziwani kuti lemba la Baibulo liri pamwambalo likulankhula za awo amene “amakhalitsa nthawi yaitali” ndi vinyo, zidakwa za chizolowezi! Kwa oterowo, zakumwa zoledzeretsa ziri monga ululu, kawirikawiri zopangitsa ziyambukiro zoipa zakuthupi ndi zamaganizo. (Miyambo 23:32-35) Akumwa mopambanitsa angasowe kudziletsa ndipo angayambe kuchita zinthu zimene mwachibadwa amachita nazo manyazi. Baibulo chotero likuchenjeza: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka, ndipo kusinza kudzveka munthu nsanza.” (Miyambo 23:20, 21)Kuledzera kukundandalikidwa pakati pa “ntchito zathupi,” zimene zingaletse munthu kulowa mu Ufumu wa Mulungu.—Agalatiya 5:19, 21; 1 Akorinto 6:10.
“Osati Chanzeru”—Kwa Yani?
Kodi ichi chikutanthauza kuti zakumwa zoledzeretsa zimaletsedwa kotheratu kwa Akristu? Bwanji ponena za chilengezo cha mtsogoleri wa chipembedzo, wotchulidwa mu nkhani yapitapo, cholingaliridwa kukhala chozikidwa pa Miyambo 20:1, kuti “anthu anzeru samwa vinyo nkomwe.” King James Version limatchula versi limeneli: “Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosocheranazo alibe nzeru.” Ndiponso, Baibulo silimapereka chilango kwa awo amene amamwa vinyo, koma m’malomwake, awo amene amasokeretsedwa naye! “Awo amene amachedwa pali vinyo” ndi “okumwa vinyo mopambanitsa”—awa ali amene “sali anzeru.”
Lingalirani, kachiwirinso, Yesaya 5:11, 22. Maversi amenewa amawerenga: “Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Tsoka kwa iwo amene ali amphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali.” Kodi nchiyani chimene Yesaya akutsutsa? Kodi sikuli kumwa kopambanitsa, kunena kuti, kumwa kuyambira “m’mamawa” kufikira “madzulo m’mdima”?
Atumiki okhulupirika a Mulungu—monga Abrahamu, Isake, ndi Yesu—anasimbidwa kukhala akumwa vinyo, pa muyezo wabwino. (Genesis 14:18; 27:25; Luka 7:34) Baibulo limatchulanso vinyo pakati pa madalitso ochokera kwa Yehova. (Genesis 27:37; Deutronomo 11:14; Yesaya 25:6-8) Ndipo Baibulo limasonyeza kuti vinyo wochepa angakhale ndi chotulukapo chopindulitsa. Vinyo “amapangitsa mtima wa munthu kukondwera,” anatero wamasalmo. (Masalmo 104:15) Mtumwi Paulo anavomereza Timoteo: “Usakhalenso wakumwa madzi okha [oipa], komatu uchite naye vinyo pang’ono, chifukwa cha mimba yako ndizo fooka zako zobwera kaŵiri kaŵiri.”—1 Timoteo 5:23.
Vinyo kapena Madzi a Mphesa?
Ena amatsutsa kuti “vinyo” wolankhulidwa mu malemba otero a Baibulo anali chabe madzi a mphesa. McClintock and Strong’s Cyclopedia, ngakhale kuli tero, imatikumbutsa ife kuti “Baibulo silimapanga kusiyanitsa pakati pa vinyo woledzeretsa ndi wosaledzeretsa—silimalozera nkomwe kapena kulankhula mwachindunji ponena za kusiyana koteroko.” M’chigwirizano ndi ichi, mu Baibulo “vinyo” akusonyezedwa kukhala chakumwa choledzeretsa ndipo wagwirizanitsidwa ndi “chakumwa chaukali.”—Genesis 9:21; Luka 1:15; Deutronomo 14:26; Miyambo 31:4 ,6.
Mosangalatsa, chozizwitsa choyamba cha Yesu chinali kutembenuza madzi kukhala vinyo. Mbiri ya Baibulo imanena kuti: “Koma, pamene mkulu wa phwandolo analawa vinyo . . . ndipo sanadziwa kumene anachokera, . . . [iye] anaitana mkwati nanena naye: ‘Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo pamene anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma. Koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopanolino.’ ” (Yohane 2:9, 10) Inde, “vinyo wokoma” amene anatulutsidwa ndiYesu anali vinyo weniweni.
Indedi, atsogoleri achipembedzo odzilungamitsa a m’tsiku la Yesu anam’suliza iye kaamba ka kumwa vinyo pakanthawi. Yesu anati:“Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo, ndipo munena, ‘Ali ndi chiwanda.’ Mwana wa munthu wafika wakudya ndi wakumwa, ndipo munena, ‘Onani!munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo!’” (Luka 7:33, 34) Kodi nchiyani chimene chikanakhala nsonga ya kusiyanitsa pakati pa kumwa kwa Yesu ndi kusamwa kwa Yohane ngati Yesu anakhala akumwa kokha madzi a mphesa osaledzeretsa? Kumbukirani, chinanenedwa ponena za Yohane kuti sanayenera “kumwa vinyo kapena kachasu.”—Luka 1:15.
Mwachidziwikire, Yesu sanatsutse kumwa pang’ono kwa zakumwa zoledzeretsa. M’tsiku lake kumwa kwa vinyo inali mbali ya chikondwerero cha Paskha.a Ndipo vinyo weniweni anapitiriza kukhala mbali ya Mgonero wa Ambuye, womwe unalowa m’malo mwa Paskha.
Chiweruzo Chimafunika
Chotero Baibulo silimaletsa kumwa kwa zakumwa zoledzeretsa. Mu nkhani zambiri, kaya kumwa chakumwa chaukali kapena ayi chiri chosankha chaumwini. Koma Baibulo mwamphamvu limaletsa kuledzera, limodzi ndi kususuka: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, . . . ankhuli osusuka. Pakuti wakumwa imwa ndi wosusukayo adzasauka.” (Miyambo 23:20, 21) Chotero, onse ayenera kusonyeza kudzisunga ndi kudziletsa. “Musaledzere naye vinyo, mmene muli chitaiko, komatu mudzale nawo mzimu.” Kumbukirani, kudziletsa chiri chimodzi cha zipatso zamzimu wa Mulungu.—Aefeso 5:18; Agalatiya 5:19-23.
Indedi, munthu sachita kufunikira kuledzera kuti alowe mu mavuto ndi zakumwa zoledzeretsa. Kabukhu kotulutsidwa ndi U. S. National Institute on Drug Abuse kamatikumbutsa ife: “Pamene munthu amwa, chakumwa choledzeretsa, chimalowerera kupyola mu njira yake yogaya chakudya kulowa mu mitsempha ya mwazi ndi kufika ku bongo mofulumira. Zimayamba kuchepetsa kayendedwe kambali zina za bongo zomwe zimalamulira kulingalira ndi malingaliro. Munthuyo amadzimva kukhala wosatsenderezedwa kwenikweni, wosamasuka koposa.” Lingaliro lakudzimva “wotsenderezedwa mochepa” limeneli lingavumbule munthu ku chiwopsyezo chamakhalidwe abwino.
Chiwopsyezo china chimakhalapo pamene chibwera kukuyendetsa. Malinga ndi ziyerekezo zina, mu United States mokha anthu 25, 000 pa chaka amaphedwa mu ngozi zopangidwa ndi oyendetsa magalimoto oledzera. Mwachiwonekere, ambiri mokulira amaderera ndi mokulira chotani mmene zakumwa zoledzeretsa zimasakazira kachitidwe kawo ka mphamvu za kuzindikira kwachibadwa za mthupi. Koma Akristu amawona moyo monga mphatso yochokera kwa Yehova. (Masalmo 36:9) Kodi chingakhale choyenera ndi kawonedwe kameneka kwa munthu kuika pangozi moyo wake weniweniwo, ndi uja wa ena, mwakuyendetsa galimoto pamene mphamvu zake za kuzindikira kwachibadwa za mthupi zachepetsedwa ndi zakumwa zoledzeretsa? Chotero, Akristu ambiri asankha kusakhudza nkomwe zakumwa zoledzeretsa pamene ayenera kuyendetsa galimoto.
Mkristu amakhalanso wodera nkhawa ponena za zotulukapo za kumwa kwake pa ena. Mosakaikira ichi ndicho chifukwa chake oyang’anira Achikristu, atumiki otumikira, ndi akazi achikulire onse achenjezedwa kusadzipereka iwo eni “kukumwetsa vinyo.” (1 Timoteo 3:2, 3, 8; Tito 2:2, 3) Pamene kuli kwakuti munthu wina angawonekere kukhala ndi chizolowezi cha zakumwa zoledzeretsa, iye amakhala wosamala kukhala wodziletsa mu kumwa kwake kotero kuti asasonkhezere wina wake molakwika; ndiponso samakalamira kukakamiza chakumwacho pa wina wake amene sakukhumba kumwa. Baibulo mowonjezera limanena kuti: “Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chirichonse chakukhumudwitsa mbale wako.”—Aroma 14:21.
Mikhalidwe ina ingaitanire ngakhale pa kusala kumwa. Talingalirani kukhala ndi pakati. International Herald Tribune (Paris edition) inagwira mawu pa phunziro lochitidwa pa Yuniversite ya ku North Carolina (U. S. A. ) ndi kusimba kuti “nkhani imodzi ya kumwa kopambanitsa kumayambiriro kwakukhala ndi pakati kungatulukemo m’kusakaza kopambanitsa kwa kuthupi ndi kwa maganizo kwa mwana womakulayo.” Akazi mosamalitsa ayenera kupenda ngozi zothekera zoterozo za kumwa mkati mwa kukhala ndi pakati.
Awo okhala ndi mbiri yakale ya kuledzera kapena chikhoterero cha kukhala osadziletsa angachipezenso icho kukhala chabwino koposa kuleka kumwa.bMofananamo kungakhale kwabwino koposa kupewa kumwa pamaso pa wina amene ali chidakwa kapena amene chikumbumtima chake chimaletsa kumwa. Ndipo kumwa zakumwa zoledzeretsa musanapite ku misonkhano Yachikristu kapena pamene mulowa mu ntchito yolalikira poyera kungakhale chinthu cholakwa. Alevi amakedzana anapereka chitsanzo cha ichi mu kuleka kumwa pamene anali pantchito mu kachisi.—Levitiko 10:8-10.
Pomalizira, ulemu uyenera kuperekedwa ku malamulo a dzikolo. M’maiko ena zakumwa zoledzeretsa ziri zoletsedwa kotheratu. Mu ena, ziridi ndi malire kwa achikulire opitirira msinkhu wokhazikitsidwa. Mkristu amamvera malamulo oterowo a “maulamuliro a akulu.”—Aroma 13:1.
Ndithudi, kaya mudzamwa zakumwa zoledzeretsa kapena ayi kapena kaya ndi zochuluka motani kapena zochepera chotani zimene mudzamwa ziri zosankha zaumwini. Mulungu amalemekezedwa pamene tigwiritsira ntchito kuzindikira ndipo mofunitsitsa kusankha njira ya kudziletsa. Chotero, tsatirani, njira yanzeru iyi kotero kuti “mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena,” “chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.
[Mawu a m’munsi]
a Mu Palestina, mphesa zinali kututidwa kumapetokwa chirimwe. Komabe, Paskha wa Chiyuda ndiMgonero wa Ambuye, zinali kuchitika mu ngululu—miyezi isanu ndi umodzi pambuyo pake. Popanda njira ya kusungira, madzi a mphesa mwachibadwa angawole.
b Adokotala amavomereza kuti amene anatsimikiziridwa kukhala chidakwa ayenera kupewa zakumwa zoledzeretsa kotheratu. Onani Galamukani! ya July 8, 1982, Chingelezi.
[Chithunzi patsamba 6]
Mkristu angasankhe kupewa kumwa kwa zakumwa zoledzeretsa pa maziko a chikumbumtima cha ena